Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Zimene Ena Amachita pa Khirisimasi Pofuna Kusangalala
    Nsanja ya Olonda—2012 | December 1
    • Zimene Ena Amachita pa Khirisimasi Pofuna Kusangalala

      “N’zosavuta kutengeka ndi zimene anthu amachita pa nthawi ya Khirisimasi. Komabe pa nthawi ya holide ngati imeneyi pamakhala zambiri zochita moti anthu sakhalanso ndi nthawi yokwanira yocheza ndi achibale komanso anzawo. Choncho m’malo moti tisangalale pa nthawiyi, timakhala otanganidwa kwambiri ndipo zimangotiwonjezera mavuto.”—BRAD HENRY, BWANAMKUBWA WAKALE WA KU OKLAHOMA [U.S.A.] ANANENA ZIMENEZI PA DECEMBER 23, 2008.

      NTHAWI ya Khirisimasi ikamayandikira pamakhala nyimbo, mafilimu komanso mapulogalamu a pa TV zimene zimapangitsa anthu kuona kuti nthawiyi ndi yosangalatsa. Kodi mukuganiza kuti chinthu chofunika kwambiri kuchita pa Khirisimasi n’chiyani? Kapena kodi ndi

      • Kukumbukira Yesu Khristu?

      • Kupatsana mphatso?

      • Kuthandiza osowa?

      • Kukachezera achibale?

      • Kukhala mwamtendere?

      Monga mmene mawu a bwanamkubwa amene ali kumanzerewa akusonyezera, anthu ambiri amalephera kuchita zimene ankafuna pa nthawi ya Khirisimasi. Pa nthawiyi anthu ambiri amakhala otanganidwa kwambiri, ankhawa komanso amawononga ndalama zambiri kugula zinthu. Koma kodi zimenezi zikutanthauza kuti anthu sangapeze zochita zina mkati mwa chaka zimene zingachititse kuti azikhala osangalala?

      Baibulo limatilimbikitsa kuti tiyenera kukumbukira Yesu Khristu, kukhala owolowa manja, kuthandiza osowa komanso kuchezera achibale. Komanso limatiphunzitsa kuti tiyenera kukhala amtendere. Choncho m’malo mokambirana chifukwa chimene anthu ena sakondwerera Khirisimasi,a m’nkhanizi tikambirana mafunso otsatirawa:

      • Kodi n’chifukwa chiyani anthu ambiri amaona kuti n’koyenera kukondwerera Khirisimasi?

      • Kodi n’chiyani chimachititsa kuti anthu asamasangalale pa nthawi ya Khirisimasi ngati mmene amafunira?

      • Ndi mfundo ziti za m’Baibulo zimene zathandiza anthu ambiri kukhala osangalala ngakhale kuti sakondwerera Khirisimasi?

      a Kuti mudziwe mfundo za m’Malemba zimene zimapangitsa anthu ena kuti asamachite Khirisimasi, onani nkhani yakuti, “Zimene Owerenga Amafunsa—N’chifukwa Chiyani Anthu Ena Sachita Nawo Khirisimasi?”

  • Kukumbukira Yesu Khristu
    Nsanja ya Olonda—2012 | December 1
    • Kukumbukira Yesu Khristu

      “Muzichita zimenezi pondikumbukira.”​—LUKA 22:19.

      Chifukwa chimene ena amakondwerera Khirisimasi.

      Anthu ambiri amati pa Khirisimasi amakumbukira kubadwa kwa Yesu.

      Pamene pagona vuto.

      Zochitika zambiri za pa Khirisimasi, kuphatikizapo nyimbo, sizigwirizana kwenikweni ndi zimene Yesu Khristu anaphunzitsa. Anthu ambiri amene amasangalala pa Khirisimasi satsatira mfundo zimene Yesu anaphunzitsa kapenanso sakhulupirira n’komwe zoti iye anakhalako. Masiku ano, nyengo ya Khirisimasi ikafika anthu ambiri amaona kuti ndi nthawi yogulitsa malonda m’malo mokumbukira Yesu.

      Mfundo za m’Baibulo zimene zingakuthandizeni.

      “Mwana wa munthu sanabwere kudzatumikiridwa, koma . . . kudzapereka moyo wake dipo kuwombola anthu ambiri.” (Maliko 10:45) N’zodziwikiratu kuti Yesu analankhula mawu a palemba la Luka 22:19, omwe ali poyambirira pa nkhaniyi, pa usiku woti afa mawa osati pa tsiku limene anabadwa. Usiku umene analankhula mawu amenewa anayambitsanso mwambo wokumbukira imfa yake. Komano kodi n’chifukwa chiyani Yesu anafuna kuti otsatira ake azikumbukira imfa yake osati kubadwa kwake? Chifukwa choti nsembe ya dipo la Yesu imathandiza anthu omvera kuti adzapeze moyo wosatha. Baibulo limati: “Malipiro a uchimo ndi imfa, koma mphatso imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha kudzera mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.” (Aroma 6:23) Choncho, chaka chilichonse otsatira a Yesu Khristu amamukumbukira monga “mpulumutsi wa dziko” osati monga khanda lobadwa kumene.—Yohane 4:42.

      “Khristu anavutika chifukwa cha inu, ndipo anakusiyirani chitsanzo kuti mutsatire mapazi ake mosamala kwambiri.” (1 Petulo 2:21) Muyenera kuphunzira zimene Yesu anachita komanso kuyesetsa kumutsanzira ndipo zimenezi ndi zimene zingasonyeze kuti mumamulemekeza komanso kumukumbukira. Muyeneranso kuganizira kwambiri mmene Yesu anasonyezera kuti anali wachifundo, woleza mtima komanso wolimba mtima pochita zoyenera. Pezani njira zimene mungamutsanzirire pa moyo wanu.

      “Ufumu wa dziko wakhala ufumu wa Ambuye wathu ndi wa Khristu wake. Iye adzalamulira monga mfumu kwamuyaya.” (Chivumbulutso 11:15) Mukamakumbukira Yesu Khristu muziganizira zimene iye akuchita panopa. Yesu akulamulira kumwamba monga Mfumu. Ponena za iye Mawu a Mulungu analosera kuti: “Adzaweruza mwachilungamo anthu onyozeka ndipo adzadzudzula anthu mowongoka mtima, pothandiza ofatsa a padziko lapansi.” (Yesaya 11:4) Wolamulira wamphamvu, osati mwana wakhanda, ndi amene angaweruze komanso kudzudzula anthu mwachilungamo.

  • Kupatsana Mphatso
    Nsanja ya Olonda—2012 | December 1
    • Kupatsana Mphatso

      “Kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.”​—MACHITIDWE 20:35.

      Chifukwa chimene ena amakondwerera Khirisimasi.

      Monga mmene Yesu ananenera, kupatsa kumathandiza kuti munthu wopereka komanso wolandirayo asangalale. Pofuna kupeza chisangalalo chimenechi, anthu ambiri amaona kuti Khirisimasi ndi nthawi yabwino yopatsana mphatso. Mwachitsanzo, kafukufuku wina anasonyeza kuti chaka chatha ku Ireland, ngakhale kuti kunali mavuto azachuma, banja lililonse linkayembekezera kuwononga ndalama zokwana madola 660 a ku America kugula mphatso za Khirisimasi.

      Pamene pagona vuto.

      Anthu ambiri amaona kuti kugula mphatso za Khirisimasi kumangowawonjezera mavuto m’malo mowathandiza kukhala osangalala. Kodi n’chifukwa chiyani zili choncho? Anthu ambiri amakakamizika kugula mphatso za ndalama zambiri kuposa ndalama zimene amapeza. Komanso popeza kuti pa nthawiyi, anthu ambiri amagula zinthu, m’malo ogulitsira zinthu mumakhala mizere italiitali ndipo izi zimakhala zotopetsa.

      Mfundo za m’Baibulo zimene zingakuthandizeni.

      Yesu anati: “Khalani opatsa.”a (Luka 6:38) Iye sananene kuti pali nthawi inayake imene anthu ayenera kupatsana mphatso. M’malomwake iye analimbikitsa otsatira ake kuti akhale ndi chizolowezi chopatsana mphatso nthawi zonse.

      “Aliyense achite mogwirizana ndi mmene watsimikizira mumtima mwake, osati monyinyirika kapena mokakamizika, chifukwa Mulungu amakonda munthu wopereka mokondwera.” (2 Akorinto 9:7) Buku lina linanena kuti malangizo a Paulo palembali ndi akuti: “Munthu sayenera kupereka kanthu asakufuna ngati kuti wachita ‘kukakamizidwa.’” Mosiyana ndi mmene mphatso za Khirisimasi zimakhalira, “munthu wopereka mokondwera” saona kuti zivute zitani ayenera kupereka mphatso inayake kwa munthu winawake pa nthawi inayake.

      “Mphatso yochokera pansi pa mtima ndi imene Mulungu amakondwera nayo, chifukwa Mulungu amafuna kuti munthu apereke zimene angathe, osati zimene sangathe.” (2 Akorinto 8:12) Mulungu safuna kuti Akhristu azichita kutenga ngongole kuti agulire anzawo mphatso zodula. Koma munthu akagula mphatso mogwirizana ndi “zimene angathe,” mphatso yakeyo imakondweretsa Mulungu. Choncho si bwino kungotsatira zimene otsatsa malonda amanena, chifukwatu iwo amalimbikitsa anthu kuti azigula zinthu pa ngongole.

      a Mabaibulo ena anamasulira lemba limeneli kuti “Patsani.” Koma m’Chigiriki choyambirira, mawu amene anawagwiritsa ntchito amatanthauza kuchita zinthu mopitiriza. Choncho pofuna kupereka tanthauzo lenileni la mawu amene Yesu anagwiritsa ntchito palembali, Baibulo la Dziko Latsopano linamasulira lembali kuti “khalani opatsa.”

  • Kuthandiza Osowa
    Nsanja ya Olonda—2012 | December 1
    • Kuthandiza Osowa

      “Wa diso labwino adzadalitsidwa, chifukwa amapereka chakudya chake kwa munthu wonyozeka.”—MIYAMBO 22:9.

      Chifukwa chimene ena amakondwerera Khirisimasi.

      Popeza Yesu ankachiritsa odwala komanso kuthandiza osauka ndi ovutika, anthu ena amafuna kutengera chitsanzo chake. Iwo amaona kuti nthawi yabwino kuchita zimenezi ndi pa nyengo ya Khirisimasi pamene mabungwe ambiri othandiza osowa amalimbikitsa anthu kuti apereke zinthu zothandizira osowa.

      Pamene pagona vuto.

      Pa nthawi ya holide anthu ambiri amatanganidwa ndi kugula zinthu, kusangalala komanso kukachezera anzawo ndi achibale. Zinthu zimenezi zimachititsa kuti asakhale ndi nthawi, mphamvu kapenanso ndalama zoti angathandizire osauka kapena zoti apereke ku mabungwe othandiza osowa.

      Mfundo za m’Baibulo zimene zingakuthandizeni.

      “Usalephere kuchitira zabwino anthu amene akufunikira zabwinozo, pamene dzanja lako lingathe kuchita zimenezo.” (Miyambo 3:27) Anthu osauka ndi ovutika safunika thandizo nthawi ya Khirisimasi yokha. Ngati mukuona kuti munthu wina akufunika thandizo ndipo inuyo mungathe kumuthandiza, kodi ndi bwino kudikira kuti mudzamuthandize nthawi ya Khirisimasi? Mulungu angakudalitseni chifukwa cha kukoma mtima kwanu ndiponso chifundo chimene mungasonyeze nthawi iliyonse, osati pa Khirisimasi pokha.

      “Tsiku lililonse loyamba la mlungu, aliyense wa inu aziika kenakake pambali kunyumba kwake malinga ndi mmene zinthu zikuyendera pa moyo wake.” (1 Akorinto 16:2) Mtumwi Paulo anapereka malangizo amenewa kwa Akhristu oyambirira amene ankafuna kuthandiza osowa. Kodi nanunso nthawi zonse ‘mungamaike pambali’ ndalama zina n’cholinga choti muzizipereka kwa anthu osauka kapena ku bungwe limene lingazigwiritse ntchito bwino? Zimenezi zingachititse kuti muzithandiza osowa popanda kulowa m’ngongole.

      “Musaiwale kuchita zabwino ndi kugawana zinthu ndi ena, pakuti nsembe zotero Mulungu amakondwera nazo.” (Aheberi 13:16) Onani kuti lembali likusonyeza kuti kuwonjezera pa “kugawana zinthu ndi ena,” sitiyenera kuiwala “kuchita zabwino.” Mwachitsanzo, makolo abwino amaphunzitsa ana awo kuti azithandiza okalamba pa ntchito zosiyanasiyana, kulimbikitsa odwala pokawaona kapena kuwaimbira foni komanso kuti azikonda ana anzawo osauka ndi olumala. Zimenezi zingathandize kuti ana aphunzire kukhala okoma mtima ndi owolowa manja nthawi zonse, osati pa Khirisimasi pokha.

      Makolo abwino amaphunzitsa ana awo kuti azithandiza okalamba, odwala komanso ana anzawo ovutika. Zimenezi zingathandize kuti ana aphunzire kukhala okoma mtima ndi owolowa manja nthawi zonse, osati pa Khirisimasi pokha

  • Kukachezera Achibale
    Nsanja ya Olonda—2012 | December 1
    • Kukachezera Achibale

      “Taonani! Ndi zabwino komanso zosangalatsa kwambiri abale akakhala pamodzi mogwirizana!”—SALIMO 133:1.

      Chifukwa chimene ena amakondwerera Khirisimasi.

      Popeza kuti Aisiraeli onse anachokera kwa Yakobo kapena kuti Isiraeli, iwo anali “abale” chifukwa anali a banja limodzi. Zinkakhala “zabwino komanso zosangalatsa kwambiri” akakumana pamodzi pa nthawi ya zikondwerero ku Yerusalemu. Masiku anonso mabanja ambiri amayembekezera kuchezerana ndi kusangalala limodzi pa nthawi ya Khirisimasi.

      Pamene pagona vuto.

      Buku lina linafotokoza kuti: “Popeza anthu apachibale amakhala kuti atha chaka chonse asanakumane, akakumana pa Khirisimasi amayamba kukambirana nkhani zapamtundu ndipo nthawi zambiri m’malo moti asangalale pa nthawiyi ena amakhumudwitsana.”—Encyclopedia of Christmas and New Year’s Celebrations.

      Mfundo za m’Baibulo zimene zingakuthandizeni.

      ‘Bwezerani makolo ndi agogo anu zowayenerera.’ (1 Timoteyo 5:4) Ngati n’zotheka, muyenera kumakaona achibale anu nthawi ndi nthawi. Ngati achibale anu amakhala kutali kwambiri, mukhoza kumalankhula nawobe kawirikawiri powalembera kalata, kuwaimbira foni komanso kuwatumizira imelo kapena kucheza nawo pa Intaneti. Ngati mutamachita zimenezi nthawi zonse, zingakuthandizeni kuti muzichepetsa kusemphana maganizo.

      “M’chikondi chanu ndi mmene muli malo ochepa . . . futukulani mtima wanu.” (2 Akorinto 6:12, 13) Achibale amene amachezerana kamodzi pa chaka sagwirizana kwenikweni komanso sadziwana bwino. Izi zimachitika makamaka kwa ana. Ana ena amaona kuti zimene iwo amakonda n’zosiyana kwambiri ndi zimene agogo awo kapena achibale awo amakonda. Choncho muyenera kulimbikitsa ana anu kuti adziwane ndi achibale osiyanasiyana kuphatikizapo agogo awo, komanso azicheza nawo.a Ana amene amakonda kucheza ndi okalamba amakhala achifundo komanso amalemekeza anthu ena amene ali aakulu kuposa iwowo.

      “Mawu onenedwa pa nthawi yoyenera ndi abwino kwambiri.” (Miyambo 15:23) Kodi mungatani kuti kusemphana maganizo kapena nkhani zina zisawononge ubale wanu? Njira ina ndi kusankha “nthawi yoyenera” yokambirana nkhani zimene mwasemphana maganizo. Ngati pachibale panu mumalankhulana nthawi zonse simudzavutika kukambirana nkhani zimene mwasemphana popanda kukhumudwitsana. Zimenezi zidzathandiza kuti muzisangalala mukakumana.

      a Onani nkhani yakuti, “Kodi N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kudziwana ndi Agogo Anga?” mu Galamukani! ya May 8, 2001 ndi yakuti, “Kodi Nditani Kuti Ubale Wanga ndi Agogo Ulimbe?” mu Galamukani! ya June 8, 2001. Magaziniwa ndi ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

  • Kukhala Mwamtendere
    Nsanja ya Olonda—2012 | December 1
    • Kukhala Mwamtendere

      “Ulemerero kwa Mulungu kumwambamwamba, ndipo pansi pano mtendere pakati pa anthu amene iye amakondwera nawo.”​—LUKA 2:14.

      Chifukwa chimene ena amakondwerera Khirisimasi.

      Chaka chilichonse papa komanso atsogoleri ena azipembedzo amalalikira uthenga wonena za mtendere. Iwo amakhala ndi chikhulupiriro choti nthawi ya Khirisimasi ikhala ya mtendere mogwirizana ndi mawu amene angelo analengeza akuti: “Mtendere pakati pa anthu amene iye amakondwera nawo.” Ena pa nthawiyi amapita kukaona malo osiyanasiyana achipembedzo.

      Pamene pagona vuto.

      Mtendere umene umakhalapo pa nthawi ya Khirisimasi umangokhala wakanthawi kochepa. Mwachitsanzo, mu December 1914, pa nthawi imene ku Ulaya kunkachitika nkhondo yoyamba ya padziko lonse, asilikali a dziko la Britain ndi la Germany anasonkhana pamodzi kukondwerera Khirisimasi. Iwo anadya, kumwa ndiponso kusutira limodzi. Komanso pa tsikuli, anasewerera limodzi mpira. Komabe iwo anangogwirizana tsiku limodzi lokhali. M’kalata imene msilikali wina wa Britain analembera msilikali wa Germany, iye anati: “Lero tili pa mtendere, koma mawa tikhala adani chifukwa aliyense akhala akumenyera nkhondo dziko lake.”

      Mfundo za m’Baibulo zimene zingakuthandizeni.

      “Kwa ife kwabadwa mwana. . . . Iye adzapatsidwa dzina lakuti . . . Kalonga Wamtendere. Ulamuliro wake wangati wa kalonga udzafika kutali ndipo mtendere sudzatha.” (Yesaya 9:6, 7) Ulosi umenewu wonena za Yesu Khristu ndi wolimbikitsa kwambiri. Yesu sanabadwe padziko lapansi n’cholinga chakuti anthu azikhala pa mtendere kamodzi kokha pa chaka. Monga Wolamulira wa kumwamba, iye adzabweretsa padzikoli mtendere weniweni womwe sudzatha.

      “Mukhale mu mtendere chifukwa cha ine [Yesu]. M’dzikomu mukumana ndi masautso, koma limbani mtima. Ndaligonjetsa dziko ine.” (Yohane 16:33) Masiku anonso Yesu amathandiza otsatira ake kuti azikhala mwamtendere. N’zoona kuti Akhristu amakumana ndi mavuto. Komabe kudzera m’Baibulo, iwo aphunzira chifukwa chake padzikoli pali mavuto komanso aphunzira mmene Yesu adzabweretsere mtendere wosatha. Zimenezi zimawathandiza kukhala ndi mtendere wamumtima.

      Chifukwa choti a Mboni za Yehova amatsatira mawu a Yesu, iwo amakhala mwamtendere ngakhale kuti ndi osiyana mayiko, mitundu, khungu komanso zinenero. Tikukulimbikitsani kuti mudzapite ku Nyumba ya Ufumu kuti mukaone nokha zimenezi. Mofanana ndi anthu ambiri, nanunso mudzavomereza kuti Mboni za Yehova zimakhala pa mtendere nthawi zonse kusiyana ndi mtendere umene anthu amakhala nawo pa nthawi ya Khirisimasi yokha.

      A Mboni za Yehova amakhala mwamtendere ngakhale kuti ndi osiyana khungu komanso zinenero. Tikukulimbikitsani kuti mudzapite ku Nyumba ya Ufumu kuti mukaone nokha zimenezi

  • Amasangalala Ngakhale Kuti Sachita Khirisimasi
    Nsanja ya Olonda—2012 | December 1
    • Amasangalala Ngakhale Kuti Sachita Khirisimasi

      PALI Akhristu ambiri amene sakondwerera Khirisimasi. Kodi iwo amaona kuti akumanidwa kanthu kena? Kodi ana awo amasirira akaona anzawo akusangalala pa Khirisimasi? Taonani zimene a Mboni za Yehova osiyanasiyana ananena pa nkhaniyi.

      Kukumbukira Yesu Khristu: “Ndisanakhale wa Mboni za Yehova ndinkangopita kutchalitchi pa Khirisimasi ndi pa Isitala pokha. Komanso ngakhale ndinkapita pa nthawiyi, sindinkaganiza za Yesu Khristu. Panopa sindikondwereranso Khirisimasi koma ndimapita kumisonkhano ya mpingo kawiri mlungu uliwonse komanso ndimaphunzitsa ena zimene Baibulo limanena zokhudza Yesu.”—EVE, AUSTRALIA.

      Kupatsana mphatso: “Ndimasangalala kwambiri munthu akandipatsa mphatso pa nthawi yomwe sindikuyembekezera. Ndimakondanso kuwapangira anthu makadi ndi zithunzi chifukwa zimachititsa kuti anthuwo komanso ineyo tisangalale.”—REUBEN, NORTHERN IRELAND.

      Kuthandiza osowa: “Timakonda kuwaphikira chakudya anthu amene akudwala. Nthawi zina timawapatsanso maluwa, keke kapena mphatso inayake ndipo iwo amasangalala. Zimenezi zimatisangalatsa chifukwa timatha kuzichita nthawi iliyonse osati pa Khirisimasi pokha.”—EMILY, AUSTRALIA.

      Kukachezera achibale: “Tikakumana pachibale pathu, ana athu amadziwana ndi amalume awo, azakhali, agogo komanso asuwani awo ndipo zimakhala zosangalatsa kwambiri. Popeza timadziwa kuti tingathe kukachezera achibale nthawi iliyonse osati pa Khirisimasi pokha, sitipanikizika ndipo achibale athu amadziwa kuti timawachezera chifukwa chowakonda.”—WENDY, CAYMAN ISLANDS.

      Kukhala mwamtendere: “Pa nthawi ya Khirisimasi anthu amakhala otanganidwa kwambiri moti sakhalanso ndi nthawi yoganizira zimene angachite kuti azikhala mwamtendere ndi ena. Koma ineyo ndinaphunzira zimene Baibulo limalonjeza zokhudza anthu, choncho zimenezi zimandipangitsa kukhala ndi mtendere wamumtima. Tsopano ndimaona kuti ana anga ali ndi tsogolo labwino.”—SANDRA, SPAIN.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena