Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • gm mutu 1 tsamba 4-11
  • Kuŵerengeranji Baibulo?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuŵerengeranji Baibulo?
  • Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu?
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Logulitsidwa Kopambana Onse Kwanthaŵi Yonse
  • Bukhu Lokhala ndi Chiyambukiro
  • Kudedwa ndi Kukondedwa
  • Linenedwa Kukhala Mawu a Mulungu
  • Baibulo la William Tyndale la Anthu
    Nsanja ya Olonda—1987
  • William Tyndale—Munthu Woona Patali
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Mmene Baibulo Linadzafikira kwa Ife—Mbali Yachiŵiri
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Baibulo Ndi Buku Lochokera kwa Mulungu
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
Onani Zambiri
Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu?
gm mutu 1 tsamba 4-11

Mutu 1

Kuŵerengeranji Baibulo?

Tikukhala ndi moyo m’dziko lokhala ndi zovuta zochulukitsitsa ndi mayankho oŵerengeka kwambiri. Mamiliyoni ochuluka nthaŵi ndi nthaŵi amakhala ndi njala. Ziŵerengero zomawonjezereka zikukhala zomwerekera ndi mankhwala oledzeretsa. Mabanja owonjezerekawonjezereka akusweka. Chiwawa cha kugonana kwapachibale ndi cha m’banja ziri zakaŵirikaŵiri m’nkhani. Mpweya umene timapuma ndi madzi amene timamwa zikuipitsidwa pang’onopang’ono. Patsopano lino, owonjezerekawonjezereka a ife akukhala mikhole yaupandu. Kodi muganiza kuti zovuta zonga zimenezi zidzathetsedwa?

1. (Phatikizamoni mawu oyamba.) Kodi ndizovuta zotani zamakono zimene zikusonyeza kuti anthu afunikira chitsogozo?

KUPHATIKIZA pazimenezo, ife tikukhala ndi moyo m’nyengo ya zosankha zovuta. Mwachitsanzo, ambiri amatsutsa kotheratu kuchotsa mimba, akumakutcha kuphedwa kwa mwana wosabadwa. Ena amalingaliranso mwamphamvu kwambiri kuti akazi ali ndi ulamuliro pamatupi awo a iwo eni ndipo ayenera kudzisankhira pankhani zoterozo. Ena amawona kugonana kwa anthu ofanana ziŵalo, chigololo, ndi kugonana ukwati usanachitike kukhala mpangidwe wa chisembwere. Ena amakhulupirira kuti machitachita ameneŵa ali nkhani ya chosankha cha munthu mwini. Kodi ndani amene ayenera kunena amene ali wolondola ndi amene ali wolakwa?

2, 3. Kodi ambiri lerolino amaliwona motani Baibulo?

2 Baibulo limapereka chitsogozo pankhani zamakhalidwe, ndipo limafotokoza zothetsera zogwira mtima ku zovuta zaupandu, njala, ndi kuipitsa. Vuto nlakuti, anthu ochuluka samawonanso Baibulo monga ukumu m’nkhani zoterozo. Panthaŵi ina, linali kumvetseredwa mwaulemu—cha Kumadzulo. Ngakhale kuli kwakuti Baibulo linalembedwa ndi anthu, kale unyinji wa a m’Dziko Lachikristu unalilandira kukhala Mawu a Mulungu ndipo unakhulupirira kuti Mulungu mwini anauzira zamkati mwake.

3 Komabe, lerolino, nkofala kukhala wokaikira ponena za kanthu kalikonse: miyambo, malingaliro, makhalidwe, ngakhale kukhalapo kwa Mulungu. Makamaka, anthu amakaikira phindu la Baibulo. Ochuluka amawonekera akulilingalira kukhala lachikale ndipo losagwira ntchito. Anzeru oŵerengeka amakono amaliwona kukhala Mawu a Mulungu. Anthu ochuluka akasankha kugwirizana ndi wophunzira James Barr, amene analemba kuti: “Cholembedwa changa chonena za kupangidwa kwa mwambo wa Baibulo chiri cholembedwa cha ntchito ya munthu. Kuli kufotokoza kwa munthu kwa zikhulupiriro zake.”1

4, 5. Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kwambiri kudziŵa kuti kaya ngati Baibulo liridi louziridwa ndi Mulungu kapena ayi? Kodi nchiyani chimene chiri chifuno cha bukhu lino?

4 Kodi limeneli liri lingaliro lanu? Kodi muganiza kuti Baibulo liri mawu a Mulungu, kapena a munthu? Mulimonse mmene mungayankhire funso limeneli, lingalirani mfundo iyi: Ngati Baibulo liri mawu a munthu chabe, pamenepo moyenerera palibe yankho lomvekera bwino ku zovuta za mtundu wa anthu. Anthu adzafunikira kungopupulikapupulika monga mmene angathere, akumayembekezera kuti mwinamwake akapeŵa kudziipitsa iwo eni ndi zoipitsa kapena kudziphulitsa ndi nkhondo ya nyukliya. Koma ngati Baibulo liri Mawu a Mulungu, ndilotu chinthu chenicheni chimene ife tikuchifuna kutipyoletsa m’nthaŵi yovuta ino.

5 Bukhu lino lidzapereka umboni wakuti Baibulo liridi Mawu a Mulungu. Ndipo afalitsi ali ndi chiyembekezo chakuti mutatha kupenda umboni, mudzazindikira kuti Baibulo liri ndi mayankho enieni a mavuto a mtundu wa anthu. Komabe, choyamba, tikufuna kukusonyezani zenizeni zina zimene, mwa izo zokha, zimapangitsa Baibulo kukhala loyenera kulingalira kwanu.

Logulitsidwa Kopambana Onse Kwanthaŵi Yonse

6, 7. Kodi nzenizeni zapadera zotani ponena za Baibulo zimene zifunikira chisamaliro chathu?

6 Choyamba, iro liri logulitsidwa kopambana, bukhu lofalitsidwa kopambana m’mbiri yonse. Malinga ndi kunena kwa bukhu lotulutsidwa mu 1988 lakuti Guinness Book of World Records, makope oyerekezeredwa kukhala 2 500 000 000 anasindikizidwa pakati pa 1815 ndi 1975. Chimenecho ndichiŵerengero chachikulu kopambana. Palibe bukhu lina lirilonse m’mbiri limene lafika pafupi chabe ndi ziŵerengero za kufalitsidwa kwa Baibulo.

7 Kuphatikiza pa zimenezo, palibe bukhu lina lirilonse limene latembenuzidwira m’zinenero zochuluka kwambiri. Baibulo tsopano lingathe kuŵerengedwa, lonse lathunthu kapena mbali chabe, m’zinenero zosiyanasiyana zoposa 1 800. Baibulo Sosaite ya ku Amereka ikusimba kuti tsopano liri lopezeka ku 98 peresenti ya chiŵerengero cha anthu a paplaneti lathu. Yerekezerani kuyesayesa kwakukulu koloŵetsedwamo m’kutulutsa matembenuzidwe ochuluka kwambiri! Kodi ndibukhu lina liti limene lalandira chisamaliro chotero?

Bukhu Lokhala ndi Chiyambukiro

8, 9. Kodi ndimawu otani amene ena anena amene amasonyeza chiyambukiro chimene Baibulo lachipereka?

8 The New Encyclopædia Britannica limatcha Baibulo “mwinamwake mulu wa timabukhu tosonkhanitsidwa pamodzi toyambukira kopambana m’mbiri ya anthu.”2 Wolemba ndakatulo wa m’zaka za zana la 19 Wachijeremani Heinrich Heine anavomereza kuti: “Ine chidziŵitso changachi nnangochipeza mwa kuŵerenga bukhulo . . . Baibulo. Iro moyenerera limatchedwa Malemba Opatulika. Iye amene wataya Mulungu wake angathe kumpezanso Iye m’bukhu limeneli.”3 Mkati mwa zaka za zana lomwelo, katswiri wokangalika kulimbana ndi ukapolo William H. Seward analengeza kuti: “Chiyembekezo chonse cha kupita patsogolo kwa anthu chiri pachisonkhezero chomakulakula cha Baibulo.”4

9 Abraham Lincoln, purezidenti wachi 16 wa United States, anatcha Baibulo “mphatso yabwino kopambana imene Mulungu wapatsa anthu . . . Koma popanda iyo sitikanadziŵa choyenera ndi cholakwa.”5 Katswiri wamalamulo wa ku Briteni Bwana William Blackstone anagogomezera chiyambukiro cha Baibulo pamene iye anati: “Pamaziko aŵiri ameneŵa, lamulo lachilengedwe ndi lamulo la chivumbulutso [Baibulo], malamulo a anthu onse amadalirapo, ndiko kuti, palibe malamulo alionse a anthu amene ayenera kuvutikira kusemphana ndi ameneŵa.”6

Kudedwa ndi Kukondedwa

10. Kodi ndimotani mmene chitsutso ku Baibulo chasonyezedwera?

10 Panthaŵi imodzimodziyo, tiyenera kuzindikira kuti palibe bukhu lina lirilonse limene lakhala chandamale cha chitsutso chankhanza kopambana ndipo ngakhale chaudani mkati mwa mbiri yonse. Mabaibulo awotchedwa pamalo owotchera zinthu apoyera, kuyambira m’Nyengo Zapakati kukafika ku zaka za zana lathu lachi 20. Ndipo kuŵerenga kapena kufalitsa Baibulo kwachititsa kulangidwa mwa kulipira faindi ndi kuikidwa m’ndende ngakhale m’nthaŵi zamakono. Makedzana, “maupandu” oterowo kaŵirikaŵiri anatsogolera ku chizunzo ndi imfa.

11, 12. Kodi ndimotani mmene Tyndale anasonyezera kukonda kwake Baibulo?

11 Chofanana ndi zimenezi chakhala kudzipatulira kumene Baibulo lakusonkhezera. Ochuluka apitirizabe m’kuliŵerenga mosasamala kanthu za chizunzo chosalekeza. Lingalirani William Tyndale, Mngelezi wa m’zaka za zana lachi 16 amene anaphunzira pa Yunivesite ya Oxford ndipo anakhala mlangizi wolemekezedwa wa pa Yunivesite ya Cambridge.

12 Tyndale anakonda Baibulo. Koma m’masiku ake, akuluakulu achipembedzo anaumirira pakusunga Baibulo liri m’Chilatini, chinenero chakufa. Chotero, kuti alipangitse kukhala lopezeka kwa anthu a mtundu wake, Tyndale anatsimikizira kutembenuzira Baibulo m’Chingelezi. Popeza kuti kumeneku kunali kosemphana ndi lamulo, Tyndale anafunikira kusiya ntchito yake ya zamaphunziro imene inali kumpezetsa bwinoyo ndi kuthaŵira ku Ulaya. Iye anakhala ndi moyo wovuta monga wothaŵa kwanthaŵi yotalika mokwanira kwakuti nkutembenuza Malemba Achigriki (“Chipango Chatsopano”) ndi mbali ina ya Malemba Achihebri (“Chipangano Chakale”) kumka m’chinenero cha kwawo; koma iye potsirizira pake anagwidwa, ndi kumgomeka mlandu wa kukhala wofalitsa mphekesera, ndipo ananyongedwa, ndipo mtembo wake unatenthedwa.

13. Kodi nchinthu chimodzi chotani chimene chimapangitsa Baibulo kukhala lapaderadi?

13 Tyndale ali mmodzi chabe wa anthu ochuluka amene ataya chirichonse mmalo mwakuti aŵerenge Baibulo kapena kulipangitsa kukhala lopezeka kwa ena. Palibe bukhu lina lirilonse limene lasonkhezera amuna ndi akazi wamba ochuluka kwambiri kufikira pakukhala ndi kulimba mtima kwakukulu kotero. Pamfundoyo, Baibulo liridi lopanda lofanana nalo.

Linenedwa Kukhala Mawu a Mulungu

14, 15. Kodi nkunena kotani kumene olemba ambiri amakunena kaŵirikaŵiri?

14 Baibulo lirinso lapadera chifukwa cha mawu onenedwa ndi ochuluka a olemba ake. Anthu okwanira 40, kuphatikizapo mafumu, abusa, asodzi, ogwira ntchito zaboma, ansembe, kazembe wankhondo mmodzi, ndi sing’anga, anali ndi mbali m’kulembedwa kwa mbali zosiyanasiyana za Baibulo. Koma kaŵirikaŵiri, olembawo ananena mawu amodzimodzi: akuti iwo anali kulemba osati malingaliro a iwo eni koma a Mulungu.

15 Motero, m’Baibulo kaŵirikaŵiri timaŵerengamo mawu onga ngati akuti: “Mzimu wa Yehova ndiwo umene unalankhula nane, ndipo mawu ake anali palirime langa” kapena, “izi ndizo zimene Mfumu Ambuye, Yehova wamakamu, wanena.” (2 Samueli 23:2, NW; Yesaya 22:15, NW) M’kalata yolembedwera kwa mlaliki mnzake, mtumwi Paulo analemba kuti: “Lemba lirilonse adaliuzira Mulungu ndipo nlopindulitsa pakuphunzitsa, pakudzudzula, pakuwongolera zinthu, pakulanga m’chilungamo, kuti munthu wa Mulungu akhale wokhoza mokwanira, wokonzekeretsedwa mwachikwanekwane kaamba ka ntchito iriyonse yabwino.”—2 Timoteo 3:16, 17, NW.

16. Kodi Baibulo limafotokoza mafunso otani?

16 Mogwirizana ndi kunena kwakutiko liri mawu a Mulungu, osati a munthu, Baibulo limayankha mafunso amene Mulungu yekha angathe kuwayankha. Mwachitsanzo, limafotokoza, chifukwa chake maboma aumunthu alephera kudzetsa mtendere wosatha, mmene anthu angathe kupezera chikhutiro chachikulu kwambiri m’moyo, ndi chimene mtsogolo muli nacho kaamba ka dziko lapansi ndi anthu pa iro. Tsopano, monga munthu wolingalira bwino, nthaŵi zambiri inu mungakhale mutadabwa ponena za mafunso ameneŵa ndi ena ofanana nawo. Nkulekeranji pafupifupi kulingalira kuthekera kwakuti Baibulo liri Mawu a Mulungu ndipo motero lokhoza mwapadera kupereka mayankho aukumu?

17, 18. (a) Kodi nziti zimene ziri zisulizo zina zoperekedwa motsutsana ndi Baibulo zimene zikufotokozedwa m’bukhu lino? (b) Kodi ndinkhani zina zotani zimene zidzafotokozedwa?

17 Tikukulimbikitsani kupenda mosamalitsa umboni woperekedwa m’bukhu lino. Ina ya mitu yake idzafotokoza zisulizo zomvedwa kaŵirikaŵiri za Baibulo. Kodi Baibulo liri losagwirizana ndi sayansi? Kodi limadzitsutsa? Kodi iro liridi ndi mbiri yeniyeni kapena nthano chabe? Kodi zozizwitsa zolembedwa m’Baibulo zinachitikadi? Umboni wogwira mtima ukuperekedwa kuyankha mafunso ameneŵa. Pambuyo pa umenewu, zisonyezero zamphamvu za kuuziridwa ndi Mulungu kwa Baibulo zikufotokozedwa: maulosi ake, nzeru yake yakuya, ndi chiyambukiro chapadera chimene iro lakhala nacho pamiyoyo ya anthu. Potsirizira pake, tidzawona chiyambukiro chimene Baibulo lingathe kukhala nacho pamoyo wanu.

18 Komabe, choyamba, tidzafotokoza mmene tinalandirira Baibulo. Ngakhale mbiri ya bukhu lodabwitsa limeneli imapereka umboni wakuti liri ndi chiyambi choposa chaumunthu chabe.

[Chithunzi chachikulu patsamba 4]

[Chithunzi patsamba 6]

Baibulo ndilo bukhu lofalitsidwa kopambana ndi lotembenuzidwa kopambana m’mbiri yonse

[Chithunzi patsamba 9]

Monga momwe thabwa iri la m’zaka za zana la 15 limasonyezera, ambiri anawotchedwa ali amoyo kaamba ka “upandu” wa kuŵerenga Baibulo

[Chithunzi patsamba 11]

Olemba Baibulo analitcha kukhala louziridwa ndi Mulungu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena