Mutu 16
Changu cha Kulambira Yehova
ABALE a atate wina a Yesu—ana ena aamuna a Mariya—ndiwo Yakobo, Yosefe, Simoni, ndi Yuda. Onseŵa asanayambe ulendowo ndi Yesu ndi ophunzira ake kumka ku Kapernao, mzinda wa pafupi ndi Nyanja ya Galileya, mwinamwake iwo akuima panyumba yawo m’Nazarete kotero kuti banjalo likalongedze zinthu zimene adzafuna.
Koma kodi nchifukwa ninji Yesu akupita ku Kapernao mmalo mwa kupitiriza utumiki wake ku Kana, ku Nazarete, kapena kumalo ena ku zitunda za Galileya? Choyamba, Kapernao ali pamalo otchuka ndipo mwachiwonekere ndimzinda wokulirapo. Ndiponso, ambiri a ophunzira opezedwa chatsopano a Yesu amakhala kapena ali pafupi ndi Kapernao, chotero sadzafunikira kusiya nyumba zawo kuti akaphunzitsidwe ndi iye.
Mkati mwa kukhala kwake m’Kapernao, Yesu akuchita ntchito zozizwitsa, monga momwe iye mwiniyo akutsimikizirira zimenezi kwa miyezi ingapo pambuyo pake. Koma mwamsanga Yesu ndi mabwenzi akewo ali paulendo kachiŵirinso. Iri ngululu, ndipo iwo ali paulendo wawo wa ku Yerusalemu kukakhalapo pa Paskha wa 30 C.E. Adakali kumeneko, ophunzira ake akuwona kanthu kena ponena za Yesu kamene mwinamwake sanayambe awonapo chiyambire.
Malinga ndi Chilamulo cha Mulungu, Aisrayeli amafunikira kupanga nsembe ya nyama. Chotero, kaamba ka kuti zisawavute, amalonda a m’Yerusalemu amagulitsa ziŵeto ndi nkhunda kaamba ka chifuno chimenechi. Koma iwo akugulitsira mkati mwenimwenimo mwa kachisi, ndipo iwo akubera anthu mwa kuwalipiritsa ndalama zambiri.
Podzazidwa ndi kuipidwa, Yesu akupanga mkwapulo wa zingwe ndi kuthamangitsira kunja ogulitsawo. Iye akukhuthulira pansi ndalama za osinthitsa ndalama ndi kugubuduza magome awo. “Chotsani izi muno!” iye afuula motero kwa ogulitsa nkhunda. “Musamayesa nyumba ya Atate wanga nyumba ya malonda.”
Pamene ophunzira a Yesu awona zimenezi, akumbukira ulosi wonena za Mwana wa Mulungu: “Changu cha pa nyumba yanu chandidya ine.” Koma Ayudawo akufunsa kuti: “Mutiwonetsera ife chizindikiro chanji, pakuti muchita izi?” Yesu akuyankha kuti: “Pasulani kachisi uyu, ndipo masiku atatu ndidzamuutsa.”
Ayudawo akulingalira kuti Yesu akulankhula za kachisi weniweni, ndipo motero iwo akufunsa kuti: “Zaka makumi anayi ndi zisanu ndi chimodzi anali nkumanga kachisiyu, kodi inu mudzamuutsa masiku atatu?” Komabe, Yesu akunena za kachisi wa thupi lake. Ndipo zaka zitatu pambuyo pake, ophunzira ake akukumbukira mawu ake ameneŵa pamene aukitsidwa kwa akufa. Yohane 2:12-22; Mateyu 13:55; Luka 4:23.
▪ Pambuyo pa ukwati m’Kana, kodi nkuti kumene Yesu akupita?
▪ Kodi nchifukwa ninji Yesu akuipidwa, ndipo kodi akuchitanji?
▪ Kodi ophunzira a Yesu akukumbukira chiyani powona zochita zakezo?
▪ Kodi Yesu akunenanji za “kachisi uyu,” ndipo iye akutanthauzanji?