Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 5/95 tsamba 1
  • Kutsatira Wotipatsa Chitsanzo Monga Onyamula Kuunika

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kutsatira Wotipatsa Chitsanzo Monga Onyamula Kuunika
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Nkhani Yofanana
  • Bwerani ku Msonkhano Wachigawo wa “Onyamula Kuunika”
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Kodi Ndani Amene Akutsatira Kuunika kwa Dziko?
    Nsanja ya Olonda—1993
  • “Onetsani Kuwala Kwanu”
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
  • ‘Muwalitse Kuunika Kwanu’
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
km 5/95 tsamba 1

Kutsatira Wotipatsa Chitsanzo Monga Onyamula Kuunika

1 Yesu, ponena za iye mwini analengeza kuti: “Ine ndine kuunika kwa dziko lapansi.” Mwa kutsatira chitsanzo chake, ophunzira a Yesu nawonso anali “kuunika kwa dziko lapansi.” (Mat. 5:14) Monga “kuunika kwa dziko lapansi,” Yesu anakhoza kunena kuti onse akumtsata adzakhala nako “kuunika kwa moyo.” (Yoh. 8:12) Zimenezo zimatipangitsa kukhala onyamula kuunika auzimu, amene sitiyenera konse kulola kanthu kalikonse kuphimba kapena kutsitikira kuunikako.

2 Gulu la Yehova limagaŵira maphunziro osonyeza mmene tingakhalire onyamula kuunika ogwira mtima. Ngati titsatira mosamalitsa uphungu ndi chitsogozo chimene timalandira, tidzakhoza kufotokoza kwa anthu a mitundu yonse za choonadi cha Ufumu. (1 Tim. 4:6) Kutumikira monga onyamula kuunika kumaphatikizapo osati kokha kulankhula choonadi pa mpata uliwonse komanso kusunga khalidwe labwino monga Akristu. Khalidwe la Wotipatsa Chitsanzo linali losanenezedwa. Monga otsatira ake, tiyenera kusonyeza kuti Chikristu ndicho moyo wathu wa tsiku lililonse. (Aef. 5:9; Tito 2:7, 8, 10) Tiyenera kuchita ntchito zabwino zimene ena angaone, zikumawasonkhezera kulemekeza Mulungu.—Mat. 5:16.

3 Mboni ina inapemphedwa mwachilendo pamene inali kupita kunyumba ndi nyumba. Mwamuna wina wabanja ndi mkazi wake anali odwala kwambiri, komanso anafuna kuti akaike ndalama kubanki. Anapempha Mboniyo kuwachitira zimenezo. Iye anavomera ndipo anapatsidwa kashi ya $2,000 kuti akaike kubanki! Pamene anabwerako, anafunsa kuti: “Kodi mwandikhulupirira bwanji popanda kundidziŵa bwino?” Yankho linali lakuti: “Timadziŵa, ndiponso aliyense amadziŵa kuti Mboni za Yehova ndizo anthu okha odalirika.” Tikuthokoza chotani nanga kuti kumamatira kwathu mosamalitsa ku makhalidwe abwino a Baibulo kumadzetsa mbiri yotero yolemekezetsa Mulungu!

4 Mphunzitsi wina wamkazi wa kalasi loyamba anafotokozera kalasi lake chifukwa chimene wophunzira wina wa Mboni wa zaka zisanu ndi chimodzi sanatengere mbali m’kujambula zithunzithunzi za Halloween. Mphunzitsiyo anati anali wonyadira kwambiri ndi msungwanayo chifukwa cha kulimba mtima pa kukhala wosiyana ndi ena chifukwa cha zimene amakhulupirira. Ngati tikhulupiriradi kanthu kena, mphunzitsiyo anatero, tiyenera kukhala olimba mtima kukamamatira. Usikuwo mphunzitsiyo anasinkhasinkha pa zikhulupiriro zake ndipo anavomereza kuti sanasonyeze kulimba mtima kumodzimodziko kwa kukhala womamatira pa zimene amakhulupirira. Tsiku lotsatira analengeza kuti sadzaloŵetsanso kalasi lake m’kukondwerera maholide alionse mtsogolo, zimene zina za izo sanazikhulupirire iye mwiniyo!

5 Anthu a Yehova ali ofunitsitsa kuŵalitsa kuunika kwawo, mosasamala kanthu za kumene ali. Khalidwe labwino la achichepere kusukulu lachititsa chidwi akusukulu anzawo ndi aphunzitsi. Mboni zachikulire zimene zimasonyeza khalidwe labwino kumene zimakhala zimasonkhezera ena kuyamikira uthenga wa Ufumu. Umboni wamwamwaŵi m’mikhalidwe yosiyanasiyana umakopa anthu oona mtima amene amafuna kudziŵa zambiri. Ngakhale khama lathu ndi kuona mtima pantchito yolembedwa zimapereka umboni. Inde, mosasamala kanthu za kulikonse komwe tili kapena zimene tikuchita, tingathe kudzutsa mwa anthu chidwi cha choonadi.

6 Mwa kuyang’anitsitsabe pa chitsanzo changwiro cha Wotipatsa Chitsanzo wamkulu, tingapitirize kuwongolera maluso athu monga ophunzira ake. Kutsanzira chitsanzo chake kudzachititsa kuunika kwathu ‘kuunikira onse.’—Mat. 5:15; 1 Pet. 2:21.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena