Misonkhano Yautumiki ya May
Mlungu Woyambira May 1
Mph. 10: Zilengezo za pamalopo ndi Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu Waufumu.
Mph. 15: “Uthenga Wabwino wa Ofatsa.” Kambitsiranani nkhaniyo ndi omvetsera, ndiyeno chitirani chitsanzo ulaliki umodzi kapena maulaliki aŵiri.
Mph. 20: “Uthenga wa Ufumu Wapadera wa Aliyense.” Nkhani ndi kukambitsirana ndi omvetsera kochitidwa ndi woyang’anira utumiki. Fotokozani zimene zachitidwa kufikira tsopano pa kugaŵiridwa kwa Uthenga wa Ufumu, makamaka kutchula chichirikizo chabwino choperekedwa pa makonzedwe a utumiki ndi kukhala ndi phande kwa atsopano mu utumiki wakumunda kwa nthaŵi yoyamba. Perekani lipoti la kufoledwa kwa gawo; fotokozani zimene zifunikira kuchitidwa ngati mpingo wina wapempha thandizo. Limbikitsani onse kuti apange kuyesayesa kowonjezereka kuti agaŵire matrakiti awo a Uthenga wa Ufumu. Gogomezerani kufunika kwa kusunga zolembapo za anthu okondwerera ndi kupanga maulendo obwereza poyesayesa kuyambitsa maphunziro a Baibulo. Sonyezani chitsanzo cha ulaliki wosonyezedwawo.
Nyimbo Na. 55 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira May 8
Mph. 15: Zilengezo za pamalopo. “Nanunso Mungakhale ndi Zokumana Nazo Zabwino!” Ngati nthaŵi ilola, pemphani omvetsera kusimba zokumana nazo zimene anapeza pamene anali kupereka Uthenga wa Ufumu.
Mph. 15: Zosoŵa za pamalopo. Kapena nkhani yakuti “Mmene Akristu Amachitira ndi Chitonzo Chofalitsidwa” ya mu Nsanja ya Olonda ya April 1, 1995, masamba 26-9.
Mph. 15: “Kodi Nkusungiranji Cholembapo cha Osapezeka Panyumba?” Mafunso ndi mayankho.
Nyimbo Na. 60 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira May 15
Mph. 10: Zilengezo za pamalopo. Lipoti la maakaunti.
Mph. 15: “Kutsatira Wotipatsa Chitsanzo Monga Onyamula Kuunika.” Mafunso ndi mayankho.
Mph. 20: “Kumbukirani Mlengi Wanu Wamkulu Muunyamata Wanu.” Nkhani yolimbikitsa yokambidwa ndi mkulu yozikidwa pa Nsanja ya Olonda ya May 15, 1990, masamba 27-9.
Nyimbo Na. 45 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira May 22
Mph. 10: Zilengezo za pamalopo. Limbikitsani upainiya wothandiza m’nyengo ya chilimwe imene ikudzayi. Fotokozani ziyeneretso zondandalikidwa m’buku la Olinganizidwa Kutsiriza Uminisitala Wathu, masamba 113-14.
Mph. 15: “Kulemba Chizindikiro Kodzetsa Chipulumutso.” Kukambitsirana ndi omvetsera. Phatikizanimo chitsanzo chimodzi kapena zitsanzo ziŵiri kuti musonyeze mmene maulendo obwereza angapangidwire.
Mph. 20: “Kodi Ndiyenera Kubatizidwa?” Nkhani yosonkhezera maganizo yozikidwa pa Nsanja ya Olonda ya October 1, 1992, masamba 20-3. Thandizani achichepere amene ali mwa omvetsera kuzindikira kufunika kwa kupatulira miyoyo yawo kwa Yehova pausinkhu waung’ono. Funsani achichepere achitsanzo chabwino aŵiri. Funsani aliyense wa iwo kuti anabatizidwa liti, chimene chinawasonkhezera, mmene akumvera tsopano ponena za kutumikira Yehova ndi chilimbikitso chimene angapereke kwa achichepere ena. Malizani ndi chilimbikitso.
Nyimbo Na. 74 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira May 29
Mph. 15: Zilengezo za pamalopo. Perekani malingaliro amene adzalimbikitsa ofalitsa kuyesa kuŵerenga Lemba monga mbali ya ulaliki wawo pamakomo. Anthu ambiri amalemekeza Baibulo ndipo amafuna kumvetsera pamene liŵerengedwa. Uphungu wake uli ndi mphamvu ndipo umasonkhezera munthu amene ali woona mtima. Kungakhale koyenera kugwiriza Baibulo m’manja pofika pakhomo. Mavesi ayenera kuŵerengedwa mwaumoyo ndiponso mosadodoma.—Onani Bukhu Lolangiza la Sukulu, masamba 32-3, ndime 12-15.
Mph. 12: Bokosi la Mafunso. Mafunso ndi mayankho. Fotokozani chifukwa chake timapindula kwambiri ndi misonkhano pamene tikonzekera pasadakhale ndi kunyamula mabuku onse ophunziridwa.
Mph. 18: Gaŵirani Buku la Mawu a Mulungu m’June. Simbani za ndemanga zonenedwa ndi anthu okondwerera amene anachita chidwi ndi buku la Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? (Onani Nsanja ya Olonda ya November 1, 1991, tsamba 32; October 15, 1990, tsamba 32.) Sonyezani mmene zimenezi zingagwiritsiridwire ntchito kuyambitsa makambitsirano. Linganizani kuti wofalitsa waluso achitire chitsanzo ulaliki umene ukufotokoza zifukwa zogwiritsirira ntchito uphungu wa Baibulo, akumagwiritsira ntchito malingaliro ndi malemba a pamasamba 186-7. Kumbutsani aliyense kudzipezera makope ogwiritsira ntchito mu utumiki pakutha kwa mlungu uno.
Nyimbo Na. 63 ndi pemphero lomaliza.