Kulemba Chizindikiro Kodzetsa Chipulumutso
1 Asanapereke ziweruzo zake zolungama, nthaŵi zonse Yehova amapereka chenjezo ndi kupatsa ofatsa njira yopulumukira. M’nthaŵi ya Ezekieli, panali aja amene anali kulira ndi kubuula chifukwa cha zonyansa zonse zimene zinali kuchitika. Yehova anachititsa kuti oyenerera amenewo alembedwe chizindikiro cha chipulumutso. (Ezek. 9:4-6) Lerolino ntchito yathu yolalikira imakwaniritsa chifuno chimenecho. Tingachite mbali yaikulu.
2 Kupeza anthu oona mtima ndiko chiyambi chabe. Timalinganiza ulendo wobwereza. Timakonzekera ulendo wobwereza paulendo woyamba mwa kulemba chogaŵiracho ndi nkhani imene takambitsirana. Chipambano chathu paulendo wobwereza chidzadalira makamaka pa zimene takonzekera kukanena ndi kukachita pobwererako.
3 Pobwerera kumene munagaŵira “Nsanja ya Olonda,” mukhoza kusumika maganizo pa mutu wake waukulu motere:
◼ “Taonani kuti pachikuto cha Nsanja ya Olonda pali mawu akuti ‘Yolengeza Ufumu wa Yehova.’ Chimene chimachititsa magaziniwa kukhala apadera nchakuti amachirikiza Ufumu wa Mulungu monga njira yokha yothetsera mavuto a dziko. Amafotokoza zimene Ufumu wa Mulungu udzachita pamene chifuniro cha Mulungu chichitidwa pa dziko lapansi. Umenewu ndiwo uthenga wabwino umene Yesu anati uyenera kulalikidwa pa dziko lonse lapansi.” Ŵerengani Mateyu 24:14, ndi kufotokoza mmene angazilandirira Nsanja ya Olonda nthaŵi zonse ndi kuigwiritsira ntchito paphunziro laumwini la Baibulo.
4 Mwina mungangofuna kusumika maganizo pa Baibulo lokha ndi kugogomezera kufunika kwa kuliŵerenga nthaŵi zonse. Mukhoza kunena kuti:
◼ “Ndikhulupirira kuti pafupifupi aliyense amene tikudziŵa angayamikire uphungu wonena za kulimbana ndi zothetsa nzeru za moyo wa tsiku ndi tsiku. Kodi muganiza kuti tingaupeze kuti uphungu umene tingadalire? [Yembekezerani yankho.] Anthu ambiri amene aika chidaliro chawo mu uphungu wa mabwenzi kapena amene alipirira uphungu wa akatswiri agwiritsidwa mwala kwambiri. Komabe, anthu ambirimbiri apeza kuti Baibulo ndilo magwero okha a uphungu umene angadalire kwenikweni. Baibulo limapereka malangizo a mmene tingalimbanire ndi zothetsa nzeru zimene tingayang’anizane nazo. [Ŵerengani 2 Timoteo 3:16, 17.] Ngakhale kuti mwina munapeza Baibulo kukhala lovuta kumva, lekani ndikusonyezeni mmene mungaligwiritsire ntchito kutsegulira nkhokwe ya uphungu wanzeru.” Pitirizani mwa kutsegula pa 1 Yohane 4:8 kapena lemba lina lililonse limene limanena za chikondi. Mutaliŵerenga, sonyezani mmene chikondi chingatithandizire kuthetsa kusamvana kwathu ndi ena.
5 Ndi cholinga choyambitsa phunziro la Baibulo, mwina mungasankhe kugwiritsira ntchito buku la “Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi,” mukumagwiritsira ntchito mawu oyamba otsatirawa:
◼ “Timakonda mabanja athu ndipo timawafunira zabwino. Kodi banja lanu lingapindule motani mwa kukhala m’dziko longa ili?” Sonyezani zithunzi pamasamba 156-7. Ŵerengani lemba limodzi kapena aŵiri ogwidwa mawu pamasamba amenewo, ndi kufotokoza kuti awa ali malonjezo operekedwa ndi Yehova Mulungu, amene sanama. Tsegulani pampambo wa mitu yake pamasamba 5-6, ndi kufunsa mwininyumba nkhani imene angakonde kwambiri kudziŵa; tsegulani pamutu umene wasankha, ndi kukambitsirana naye ndime imodzi kapena ziŵiri.
6 Kodi mukufuna kuthandiza munthu wina kulembedwa chizindikiro cha chipulumutso? Chinsinsi chake ndicho ‘kukwaniritsa utumiki wanu’ mwa kukonzekera bwino ndi kubwerera mwamsanga kumene munapeza munthu wokondwerera.—2 Tim. 4:5.