Nyimbo 92
Lalikirani Molimba Mtima
1. Atumiki’nu a Yehova,
Limbani Satana apsinja.
Tipeza chilimbikitsochi,
Mu Mawu a Mulungu ndi m’kumva.
Mawu a Mulungu apatsa
Mphamvu nathandiza kumvera.
Monga atumwi akalewo,
Tikondwere ndi kukhazikika.
2. Pakuti tikhulupilira
Mawu a M’lungu m’mbali zonse,
Sitimawopa konse anthu
Tikhulupilira molimbadi.
Tisamalire ntchito yathu
Ya kulalika m’dziko lonse.
Mwa kulalika molimbika,
Tikhalabe abwenzi a M’lungu.
3. Thandizani ofo’ka onse,
Kuti anene molimbika.
Musasiyetu atsopano;
Athandizeni kuchotsa mantha.
Tonthozani onse olira;
Ndi kudalira pa Mulungu.
Adzalamula m’dziko lonse
Kuti anthu onse amtamande.