Nyimbo 31
Changu Kaamba ka Nyumba ya Yehova
1. Yesu anali wachangu
Panyumba ya Yehova.
Monga moto womayaka,
Povumbula choipa.
Anadza kupulumutsa,
Nasonyeza cho’nadi.
Ka’mba ka ulemu wa Ya
Anadyedwa ndi changu.
2. Atumwi ndi ophunzira
Analinso achangu.
Mothandizidwa ndi mzimu,
Mipingo inakula!
Sanaleke kulalika,
Namka kunyumba zonse.
Adati chipulumutso,
Nati anthu alape.
3. Lero tikuwona anthu
Achangu m’chilungamo.
Palibe chowabwevutsa
M’dziko loipa lino.
M’lungu awalimbikitsa;
Amtumikira iye.
Alalikabe Ufumu,
Ngachangube, ngolimba.