Nyimbo 70
Khalani Monga Yeremiya
1. Utumiki wa ’fumu
Uli wosangalatsa.
Pakutumikirako,
M’lungu asamalira.
Baibulo nlowona—
Litichenjeza ife—
Potumikira Mulungu
Tidzavutitsidwanso.
2. Pamene Yeremiya,
Akalitu mnyamata
Anatumikira Ya,
Kodi Ya anatani?
‘Ngakhale akumenye,
Ndi mphamvu zawo zonse,
Sadzakulakatu konse,
Ndiwe nsanja yolimba.’
3. Yeremiya anati
M’lungu ali wowona.
Nkana anavutika,
Anatsiriza ntchito.
Dalirani Mulungu,
Ngati Yeremiyayo.
Lalikirani molimba
Ufumu wa Mulungu.