Nyimbo 156
“Ndifuna”
1. Wona chikondi cha Yesu (chikondicho),
Anasiya m’mwamba malo (abwinodi),
Kukhala ndi anthu, Kupatsa cho’nadi.
Inde, cho’nadi ananena.
Anatonthozadi anthu (kalerodi),
Anachiritsa odwala.
Pantchitoyo anali wowona,
Chotero anati: “Ndifuna.”
2. O Ya anathandizadi (zowonadi)
Potumiza ‘kapoloyo (wanzeruyo)’
Titumika naye, Pomagwira ntchito,
Kupulumutsa ofooka!
Ndithu aŵa angadziŵe (chowonadi)
Ngati tiwakonda zedi.
Ngati amasiye akafunsa,
Kodi mudzanena: “Ndifuna”?
3. Chikondi chitisonkheza (kwambiridi),
Kulalika mopilira (kudzikoli)
Kwa obuulawo Ndi osukidwawo;
Tifike ofuna cho’nadi.
Nchimwemwe pomwe adziŵa (chowonadi)
Cho’nadi cha Baibulo,
Pochita utumiki wa M’lungu!
Chifukwa mwatitu: “Ndifuna.”