Khalani Chitsanzo m’Mawu ndi m’Mayendedwe
1 Mtumwi Paulo analangiza Timoteo kukhala chitsanzo m’mawu ndi m’mayendedwe. (1 Tim. 4:12) Nafenso tiyenera kusonyeza chitsanzo chabwino m’mawu ndi m’mayendedwe, makamaka pamene tili mu utumiki, pakuti kuchita motero kungasonyeze ngati timafika kapena sitimafika mitima ya amene timakumana nawo.
2 Tifunikira kusonyeza mbali zonse za khalidwe labwino, kuphatikizapo ulemu, kulingalira ena, kukoma mtima, ndi luso. Mwa kusonyeza mikhalidwe imeneyi, timasonyeza kuti tikudziŵa mmene zochita zathu zimakhudzira mtima wa ena. Khalidwe labwino mu utumiki lingayerekezeredwe ndi zokoleretsa zimene zimagwiritsiridwa ntchito kukometsera chakudya. Ngati palibe, chakudya chabwino chingamveke chosukuluka ndi chosakoma. Kulephera kusonyeza khalidwe labwino pochita ndi ena kungakhale ndi zotulukapo zonga zimenezo.—Akol. 4:6.
3 Khalani Chitsanzo m’Mawu: Kumwetulira kwaubwenzi ndi moni wachikondi ndizo mbali zofunika pa ulaliki wathu wa uthenga wabwino. Pamene tikometsera mawu athu oyamba ndi chikondi ndi kuona mtima, timadziŵitsa mwini nyumba kuti tili ndi chikondwerero mwa iye. Pamene iye akulankhula, mvetserani mosamalitsa ndi kusonyeza ulemu woyenera pa zolingalira zake. Pamene mulankhula, teroni mwaluso ndi mwachisomo.—Yerekezerani ndi Machitidwe 6:8.
4 Nthaŵi zina timakumana ndi munthu amene saali waubwenzi, ngakhale wandewu. Kodi tiyenera kuchita motani? Petro anatilimbikitsa kulankhula mwa njira imene imasonyeza “chifatso ndi [ulemu waukulu, NW].” (1 Pet. 3:15; Aroma 12:17, 18) Yesu anati ngati mwini nyumba mwachipongwe akana uthenga wa Ufumu, tiyenera ‘kungosansa fumbi m’mapazi athu.’ (Mat. 10:14) Kusonyeza kwathu khalidwe labwino m’mikhalidwe yotero m’kupita kwa nthaŵi kungafeŵetse mtima wa wotsutsayo.
5 Khalani Chitsanzo m’Mayendedwe: Kulalikira uthenga wabwino m’makwalala apiringupiringu ndi poyera kumafuna kuti tikhale olingalira ena, osalankhula mofuula kapena moumiriza, ndi kuti tisatsekereze odutsa m’njira. Pamene tili m’nyumba za anthu okondwerera, tifunikira kukhala ndi khalidwe labwino ndi kudzisunga monga alendo aulemu, tikumasonyeza chiyamikiro kaamba ka kuchereza kwawo. Ana alionse otsagana nafe ayenera kusonyeza ulemu kwa mwini nyumba ndi chuma chake ndipo ayenera kudzisunga ndi kutchera khutu pamene tikulankhula. Ngati ana ali osaweruzika, zimenezi zidzapereka chithunzi choipa.—Miy. 29:15.
6 Kaonekedwe kathu kaumwini kayenera kusonyeza ena kuti ndife atumiki a Mawu a Mulungu. M’kavalidwe kathu ndi kapesedwe, sitiyenera kukhala auve kapena osapesa kapena opambanitsa. Kaonekedwe kathu nthaŵi zonse kayenera kukhala koyenera uthenga wabwino. (Yerekezerani ndi Afilipi 1:27.) Mwa kusamala kwambiri kaonekedwe kathu ndi zipangizo, sitidzapatsa ena chifukwa chokhumudwira kapena chonenezera utumiki wathu. (2 Akor. 6:3, 4) Chitsanzo chathu chabwino m’mawu ndi m’mayendedwe chimawonjezera kukopa kwake kwa uthenga wa Ufumu, chikumabweretsa ulemu kwa Yehova.—1 Pet. 2:12.