Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 9/96 tsamba 2
  • Misonkhano Yautumiki ya September

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Misonkhano Yautumiki ya September
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Timitu
  • Mlungu Woyambira September 2
  • Mlungu Woyambira September 9
  • Mlungu Woyambira September 16
  • Mlungu Woyambira September 23
  • Mlungu Woyambira September 30
Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
km 9/96 tsamba 2

Misonkhano Yautumiki ya September

Mlungu Woyambira September 2

Nyimbo Na. 98

Mph. 12: Zilengezo zapamalopo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu Waufumu. Limbikitsani aliyense, ndipo makamaka ochititsa Phunziro la Buku la Mpingo, kupendanso nkhani ya mu Utumiki Wathu Waufumu wa May 1993 yakuti “Kuphunzira Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako.” Sonyezani mfundo zazikulu za nkhaniyo.

Mph. 15: “Yendani mwa Chikhulupiriro.” Mafunso ndi mayankho.

Mph. 18: “Kulalikira Uthenga Wabwino ndi Maganizo Otsimikiza.” Kambanipo mawu otsegulira ozikidwa pa ndime 1. Ngati mpingo uli ndi mabuku a Moyo wa Banja alionse, ameneŵa ayenera kuwagwiritsira ntchito choyamba. Ndiyeno fotokozani kokha ndime 2-5 za nkhaniyi. Khalani ndi chitsanzo chokonzedwa bwino chosonyeza mmene tingagaŵirire buku la Kukhala ndi Moyo Kosatha ndi la Moyo wa Banja, kupanga ulendo wobwereza, ndi kuyambitsa phunziro m’buku la Chidziŵitso.

Nyimbo Na. 48 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira September 9

Nyimbo Na. 18

Mph. 12: Zilengezo zapamalopo. Lipoti la maakaunti. Kambitsiranani mutu wakuti “Lalikirani Ufumu.”

Mph. 18: Pendani Lipoti la Mpingo la Chaka Chautumiki cha 1996. Nkhani yomangirira ndi yosonkhezera ya woyang’anira utumiki. (Onani buku la Uminisitala Wathu, masamba 100-2.) Sonyezani pamene mpingo unachita bwino, ndipo uyamikireni. Sonyezani mmene ntchito ya apainiya okhazikika ndi othandiza yathandizira kupititsa patsogolo ntchitoyo kumaloko. Tchulani ziŵerengero za ofika pamisonkhano, mukumagogomezera kufunika kwa kupezekapo nthaŵi zonse. Fotokozani zonulirapo zofikika zimene mpingo ungakalimire kufikira chaka chikudzacho.

Mph. 15: “Kulalikira Uthenga Wabwino ndi Maganizo Otsimikiza.” Pendani ndime 6-8 zokha. Khalani ndi chitsanzo chimodzi kapena ziŵiri zosonyeza mmene maulaliki osonyezedwawo angagwiritsidwire ntchito. Limbikitsani onse kupanga maulendo awo obwereza mwamsanga.

Nyimbo Na. 123 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira September 16

Nyimbo Na. 10

Mph. 15: Zilengezo zapamalopo. Tchulani zotulukapo zabwino za kugwiritsira ntchito vidiyo ya Jehovah’s Witnesses—The Organization Behind the Name kutsogozera okondwerera ku gulu. Mwachidule simbani chokumana nacho chimodzi kapena ziŵiri zotengedwa mu Nsanja ya Olonda ya October 1, 1992, masamba 30-1.

Mph. 15: “Khalani Chitsanzo m’Mawu ndi m’Mayendedwe.” Mafunso ndi mayankho.

Mph. 15: Mayendedwe Achikristu Kusukulu. Atate akulankhula kwa mwana wawo wamwamuna kapena wamkazi kumsonyeza mbuna zowopsa zimene zili kusukulu; agogomezera kufunika kwa kusamala mayanjano ndi kupeŵa machitachita okayikitsa. Apenda bokosi lili patsamba 24 m’brosha la Maphunziro ndi kufotokoza kufunika kwa kupereka chitsanzo chabwino monga Mboni. Atatewo atchula ziyeso zina zimene zimabuka zophatikizapo anamgoneka, kupita kokacheza, kupezeka ku macheza, kapena kutenga mbali m’maseŵero; akambitsirana mmene angapeŵere mavuto. Atatewo akulimbikitsa wachichepereyo kusazengereza kuwauza pamene ali ndi zothetsa nzeru—amafuna kudziŵa ndi kuthandiza.

Nyimbo Na. 32 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira September 23

Nyimbo Na. 21

Mph. 10: Zilengezo zapamalopo. Kumbutsani amene akhoza kuti apereke zopereka za magazini ndi mabuku opatsidwa kwa abale osoŵa. Kambitsiranani nkhani yakuti “Kodi Mungayankhe?”

Mph. 15: Zosoŵa zapamalopo. Kapena nkhani yozikidwa pa mutu wakuti “Yang’anani Kupyola pa Zinthu Zimene Mukuona!” mu Nsanja ya Olonda ya February 15, 1996, masamba 27-9.

Mph. 20: “Lalikirani Uthenga Wabwino Paliponse.” Mafunso ndi mayankho. Kambitsiranani ndime 1-15 zokha. Ŵerengani ndime 3 ndi 5. Phatikizanipo zokumana nazo zakumaloko za aja amene apeza chipambano kuchitira umboni m’makwalala kapena m’zoyendera za onse.

Nyimbo Na. 215 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira September 30

Nyimbo Na. 171

Mph. 12: Zilengezo zapamalopo. Kambitsiranani Bokosi la Mafunso.

Mph. 20: “Lalikirani Uthenga Wabwino Paliponse.” Mafunso ndi mayankho. Kambitsiranani ndime 16-35. Sonyezani mmene malingalirowo angagwiritsidwire ntchito kumaloko. Sonyezani zitsanzo m’ndime 23-5. Ŵerengani ndime 34-5.

Mph. 13: Pendani Mabuku Ogaŵira m’October. Tidzagaŵira masabusikripishoni a magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Kambitsiranani mfundo zosiyanasiyana, zonga: (1) Chifuno chimene magazini amafalitsidwira, chofotokozedwa pamasamba otsegulira. (2) Amafalitsidwa m’zinenero zambiri, kupereka chidziŵitso cha Baibulo padziko lonse. (3) Nsanja ya Olonda yalinganizidwa kaamba ka phunziro laumwini, la banja, ndi la timagulu. (4) Anthu amene amapita ku zipembedzo zina zambiri amawaŵerenga. (5) Ife mwachindunji tidzapereka makope atsopano kwa aliyense amene akufunadi kuwaŵerenga. (6) Alinganizidwa makamaka kaamba ka anthu otanganitsidwa. (7) Nsanja ya Olonda yakhala ikufalitsidwa kuyambira 1879; Galamukani! kuyambira 1919. Malizani mwa kusimba ndemanga zoperekedwa ndi oŵerenga oyamikira.—Onani Nsanja ya Olonda yachingelezi ya April 15, 1986, tsamba 32.

Nyimbo Na. 3 ndi pemphero lomaliza.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena