Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 7/1 tsamba 7-12
  • “Dzisonyezeni Inueni Kukhala Akuyamika”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Dzisonyezeni Inueni Kukhala Akuyamika”
  • Nsanja ya Olonda—1988
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zopangitsa Zochuluka za Kuyamikira
  • Mmene Tingasonyezere Kuyamikira
  • Kuolowa Manja kwa Mtima
  • Kufanana Kwamakono
  • Njira Zosonyezera Kuyamikira
  • Chitsanzo Chabwino cha Mkazi Wamasiye Wosowa
  • Zikumbutso ku Kuyamikira Ziri Zopindulitsa
  • ‘Khalani Oyamikira’
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Zifukwa Zowonjezereka za Kukhalira Oyamikira
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Nchifukwa Ninji Kukhala Oyamikira?
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Sonyezani Kuyamikira Kwanu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1988
w88 7/1 tsamba 7-12

“Dzisonyezeni Inueni Kukhala Akuyamika”

“Lolani mtendere wa Kristu ulamulire mitima yanu . . . Ndipo dzisonyezeni inueni kukhala akuyamika.”​—AKOLOSE 3:15, NW.

1. Kodi Akristu ayenera kukhala ogalamuka molimbana ndi chiyani m’dziko iri losayamikira?

ZANA lovutitsidwa la 20’li lafika ku mlingo umene anthu ambiri aiwala kukhala oyamikira. Mawu oyamikira “chonde” ndi “zikomo” amamvedwa mochepera ndi kutha kwa chaka chirichonse. Kusayamikira kwakhala mbali ya “mpweya,” mzimu wa dyera womwe ukulamulira anthu a dziko iri. (Aefeso 2:1, 2) Ngakhale kuti Akristu “sali mbali yadziko,” iwo ayenera kukhala mu ilo kufikira ku utali umene dongosolo la kachitidwe ka zinthu liripoli lidzakhala. (Yohane 17:11, 16) Chotero, iwo ayenera kusamalira kuti mzimu wosayamikira umenewu sukuwakhudza iwo, kupangitsa kuyamikira kwawo kuzimiririka.

2. (a) Kodi ndi njira zina ziti m’zimene atumiki a Yehova angasonyezere kuyamikira kwawo kwa iye? (b) Nchiyani chikufunika koposa kulongosola kwa pakamwa kwa chiyamiko?

2 Chiyamikiro kaamba ka ubwino wa Mulungu chingasonyezedwe kaŵirikaŵiri m’kukambitsirana ndi akhulupiriri anzathu. Akristu ambiri odzipereka mwinamwake amayamikira Atate wawo wa kumwamba, Yehova, kaamba ka ubwino wake nthaŵi zambiri pa tsiku, akumachita tero m’pemphero laumwini. Kuyamikira kumasonyezedwanso m’mapemphero a mpingo ndi pamene akuimba nyimbo za Ufumu pa misonkhano ya Chikristu. Ndithudi, chiri chopepuka kusonyeza chiyamikiro m’mawu. Mtumwi Paulo, ngakhale kuli tero, analimbikitsa abale ake ku Kolose kusangonena kokha kuti anali oyamikira komanso kusonyeza kapena kuchitira chitsanzo kuyamikira m’moyo wawo wa tsiku ndi tsiku. Iye analemba kuti: “Lolani mtendere wa Kristu ulamulire mitima yanu, popeza inu munaitanidwa, m’chenicheni, ku iwo m’thupi limodzi. Ndipo dzisonyezeni inu eni kukhala akuyamika.”​—Akolose 3:15, NW.

Zopangitsa Zochuluka za Kuyamikira

3. Nchifukwa ninji tonsefe tiyenera kukhala oyamikira kwa Mulungu?

3 Aliyense wokhala ndi moyo ali ndi chifukwa chachikulu cha kuyamikira. Chifukwa chachikulu koposa chiri kusangalala ndi moyo weniweniwo, popeza chirichonse chimene tiri nacho kapena chimene tingakonzekere mwadzidzidzi chingakhale chopanda phindu ngati titaya moyo wathu. Wamasalmo Davide anasonkhezera anthu onse kukumbukira kuti “chitsime cha moyo chiri ndi inu [Yehova Mulungu].” (Masalmo 36:9) Ndipo mtumwi Paulo anakumbutsa amuna a ku Atene za chowonadi chosatha chofananacho pamene analankhula pa Areopagi. (Machitidwe 17:28) Inde, kungokhala kokha ndi moyo chiri chifukwa chokulira chakuyamikira. Ndipo chiyamikiro chathu chimazama pamene tikumbukira mphamvu zimene Mulungu watipatsa ife​—lingaliro la kulaŵa, la kukhudza, la kununkhiza, la kuwona, ndi la kumva​—kotero kuti tingasangalale ndi moyo ndi kukongola kwa chilengedwe chotizungulira.

4. Nchiyani chimene chidzatichinjiriza ife ku kutenga madalitso a moyo mosasamala?

4 Komabe, ambiri amatenga zinthu zabwino zimenezi mosasamala. Kokha pamene iwo amanidwa mphamvu, monga ngati kuwona kapena kumva, ndi pamene anthu ambiri amazindikira madalitso amene iwo analephera kuyamikira pamene anali m’moyo wabwino. Akristu odzipereka mokhazikika afunikira kukhala osamalira kusakokedwera m’kusoweka kwa chiyamikiro kofananako. Iwo ayenera kugwira ntchito molimbika kusungilira kawonedwe kofananako ka kuyamikira monga komwe kanasonyezedwa ndi wamasalmo amene ananena kuti: “Inu Yehova, Mulungu wanga, zodabwiza zanu mudazichita nzambiri, ndipo zolingalira zanu za pa ife; palibe wina wozifotokozera inu; ndikazisimba ndi kuzitchula, zindichulukira kuziŵerenga.”​—Masalmo 40:5.

5. Mosasamala kanthu za madalitso owonjezereka a Israyeli ochokera kwa Yehova, ndi njira yochititsa manyazi yotani imene iwo analondola?

5 Salmo 106 limapereka kufupikitsa kwa ndakatulo kwa zochita zamphamvu zimene Yehova anazichita m’malo mwa anthu ake, Israyeli. Zochita za Mulungu ndi iwo zinali m’kuwonjezera ku ubwino ndi madalitso a nthaŵi zonse a moyo amene iye anatsanulira pa mtundu wa anthu mwachisawawa. Mosasamala kanthu za mwaŵi umenewu, ngakhale kuli tero, wamasalmoyo akuloza kuti Aisrayeli sanapitirize kusonyeza chiyamikiro kaamba ka madalitso awo apadera. Versi 13 likunena kuti: “Koma anaiwala ntchito zake msanga; sanalindira uphungu wake.” Ayi, sikunali kupita kwa nthaŵi kumene mwapang’onopang’ono kunatha kuyamikira kwawo, kotero kuti zaka makumi pambuyo pake iwo sanakumbukire zimene Mulungu anachita kaamba ka iwo. M’malomwake, iwo anaiwala mwamsanga​—mkati mwa milungu ya zozizwitsa zowonekera za Yehova m’malo mwawo pa Nyanja Yofiira. (Eksodo 16:1-3) Momvetsa chisoni, zochitika za mtsogolo zikusonyeza kuti kusayamikira kunakhala chitsanzo chokhazikika m’moyo wawo.

Mmene Tingasonyezere Kuyamikira

6. Nchifukwa ninji chifuno cha kupereka chachikhumi chinali chosavuta?

6 Mwatsatanetsatane, Yehova anatchula njira zitatu zachindunji m’zimene Aisrayeli anayenera kusonyeza chiyamikiro chowona mtima kaamba ka ubwino wake. Imodzi inali kusunga chifuno chake cha chachikhumi mwakupereka kwa Yehova chachikhumi cha mbeŵu ndi ziweto. (Levitiko 27:30-32) Ichi sichikakhala chovuta, popeza Mulungu anali wathayo kaamba ka dzuŵa, nthaka ya chonde, mvula, ndi chozizwitsa cha kukula. Chotero, kupereka chachikhumi kwa ansembe pa malo opatulika a Yehova chinali chisonyezero chogwira ntchito cha chiyamikiro kwa Yehova iyemwini.

7. (a) Ndi kusiyana kokulira kotani kumene kunalipo pakati pa kupereka chachikhumi ndi kupanga zopereka kwa Yehova? (b) Nchiyani chimene ichi chinawalola Aisrayeli kuvumbula ponena za iwo eni?

7 Chifuno china chinali kupanga zopereka kwa Mulungu m’zimene unyinji wake unagamulidwa ndi mkhalidwe wa mtima wa m’Israyeli aliyense. Pamene kuli kwakuti panalibe unyinji wokhazikitsidwa woperekedwa, zoperekazo zinayenera kukhala zoyamba kucha​—zoyamba za chimanga, vinyo, ndi umbweya wa nkhosa. (Numeri 15:17-21; Deuteronomo 18:4) M’kuwonjezerapo, Yehova anasonyeza kuti anthu ake ‘sanayenere kupereka mokaikira’ ndipo anayenera kupereka “zabwino koposa za zipatso zoyamba kucha.” (Eksodo 22:29; 23:19, NW) Ichi chinawapatsa Aisrayeli mwaŵi wa kusonyeza chiyamikiro chawo kwa Yehova m’njira yokhoza kukhudzika. Iwo akanavumbula kuzama kwa chiyamikiro chawo mwa unyinji wa zopereka. Kodi iwo akapereka kokha mkoko wa mphesa? Kapena kodi mtima woolowa manja ukawasonkhezera iwo kupereka mtanga wodzala? Chotero munthu, aliyense kapena banja akanasonyeza chiyamikiro popanda kukakamizidwa.

8. (a) Ndi mapindu aŵiri ati amene makonzedwe akufunkha anapereka? (b) Kodi ndimotani mmene kuolowa manja ndi kuyamikira kunasonyezedwera ndi onse amene anadzilowetsa m’makonzedwe ofunkha?

8 Njira yachitatu yachindunji yosonyezera chiyamikiro inali m’chigwirizano ndi chopereka cha Mulungu cha kufunkha. Panthaŵi yokolola, mbali zina zinayenera kusiidwa zosakololedwa kaamba ka osowa. Ichi sichinawaphunzitse iwo kokha kukhala achifundo ndi olingalira kaamba ka osauka komanso chinatsimikizira kuti sanadalire pa zoperekedwa zonyazitsidwa zomwe sizinafunikire kuyesetsa kulikonse ku mbali yawo. (Levitiko 19:9, 10) Kokha kuti ndi unyinji wotani umene unayenera kusiidwa kaamba ka osowa sikunaperekedwe. Koma alimi a Chiisrayeli anasonyeza mzimu woolowa manja mwa kusiya zambiri m’mphepete mwa minda yawo ndipo mwakutero kusonyeza chiyanjo kwa osauka, iwo akakhala akulemekeza Mulungu. (Miyambo 14:31) Chinasiidwa kwa iwo kugamulapo kuti kaya asiye mbali yaing’ono kapena yaikulu yosakololedwa. Koma Mulungu anapereka zitsogozo zamphamvu kulinga ku kuolowa manja mwa kuwalangiza iwo kuti mtolo uliwonse wosawonedwa m’munda kapena chipatso chirichonse chosiidwa mu mtengo kapena mphesa ziyenera kusiidwa kaamba ka ofunkha. (Deuteronomo 24:19-22) Kenaka, ofunkhawo akasonyeza kuyamikira kwawo kwa Yehova kaamba ka chopereka chimenechi mwakupereka chachikhumi cha chofunkha chawo pa malo ake olambirira.

Kuolowa Manja kwa Mtima

9. Nchifukwa ninji awo amene anali kusonyeza mkhalidwe wadyera m’chenicheni anali kudzivulaza iwo eni?

9 Ngati Aisrayeli anapanga zopereka zaufulu, dalitso la Yehova likakhala panyumba zawo. (Yerekezani ndi Ezekieli 44:30; Malaki 3:10.) Mosasamala kanthu za kuchuluka kwa zotuta, ngakhale kuli tero, iwo kaŵirikaŵiri analephera kupanga zopereka. Kenaka Mulungu anagwiritsira ntchito zokumbutsa kupyolera mwa mafumu ndi aneneri kudzutsanso kuyamikira kwawo. M’chenicheni, Aisrayeli adyera anali awo amene sanapeze phindu, popeza Yehova sanadalitse awo amene sanapereke chopereka m’chigwirizano ndi kulambira kwake kapena kwa osauka.

10. (a) Nchiyani chimene chinali zotulukapo za chimwemwe za zikumbutso za Mfumu Hezekiya ponena za kuyamikira? (b) Kodi mikhalidwe imeneyo inakhala kwa nthaŵi yaitali?

10 Pa chochitika chimodzi, zokumbutsa za Mfumu Hezekiya zinatulukapo m’chikondwerero cha chisangalalo cha masiku 14 m’Yerusalemu. Anthuwo anadzutsidwanso mwauzimu. Choyamba, iwo anawononga zogwirizanitsa zonse za kulambira mafano ndipo kenaka “anapereka miyulu pa miyulu. . . . Pamene Hezekiya ndi akulu ake anadza, nawona miyuluyi, analemekeza Yehova, nadalitsa anthu ake Aisrayeli.” (2 Mbiri 30:1, 21-23; 31:1, 6-8) Momvetsa chisoni, ngakhale kuli tero, pambuyo pa nyengo zodzutsanso zoterozo, anthuwo anagweranso m’kusayamikira. Pomalizira pake, kuleza mtima kwa Mulungu kunatha, ndipo iye analola anthu ake kutengedwa andende ku Babulo. Mzinda wawo ndi kachisi wawo wokongola zinawonongedwa. (2 Mbiri 36:17-21) Pambuyo pake, pamapeto pa kubwezeretsanso, mkhalidwe kachiŵirinso unafikira kukhala woipa kwambiri kotero kuti Yehova anayerekeza kuwuma dzanja kwa Ayudawo ndi kuba kuchokera kwa iye, kumlanda iye!​—Malaki 3:8.

11. Ndi prinsipulo lotani lophunziridwa kuchokera ku mbiri ya Israyeli limene lingapindulitse Akristu okhala m’nthaŵi ino?

11 Ndi prinsipulo lotani limene lingaphunziridwe kuchokera ku mbiri yophophonya ya Aisrayeli? Iri: Kokha ngati kuyamikira kunakhaladi kwamphamvu m’mitima yawo, iwo mwachimwemwe anasonyeza ichi mwakupereka “miyulu pa miyulu” kwa Yehova. Koma pamene kuyamikira kunaiwalidwa kapena kunabwera ku malo otsika, kupereka kwa chimwemwe kwa zinthu zakuthupi kenaka kunalekeka. Kodi mkhalidwe woipa umenewu ungasonyezedwe ndi Akristu odzipereka lerolino? Inde, chifukwa kupanda ungwiro kwa munthu kudakali ndi ife. Tiyenera kukhala oyamikira chotani nanga kuti Mulungu analemba zochita zake ndi Aisrayeli kotero kuti ife, amene tikukhala kumapeto kwa dongosolo iri la kachitidwe ka zinthu, tingaphunzire ndi kupindula kuchokera ku izo!​—Aroma 15:4; 1 Akorinto 10:11.

12. (a) Ndimotani mmene anthu a Yehova lerolino aliri m’mkhalidwe wofanana ndi uja wa Aisrayeli? (b) Ndi mafunso otani amene tiyenera kufunsa?

12 Mofanana ndi Aisrayeli, anthu a Yehova lerolino ali ndi zifukwa zambiri za kukhalira oyamikira. Ifenso tiri olandira a madalitso ambiri kuposa awo amene akusangalalidwa ndi anthu anzathu. M’chenicheni, timadziŵa zambiri koposa ponena za zifuno za Yehova kuposa mmene anachitira anthu a Israyeli. Taphunzira mmene Mulungu mofunitsitsa anaperekera nsembe Mwana wake, ndipo tiri ozindikira za madalitso amene ichi chikabweretsa kwa awo okhala ndi chivomerezo chaumulungu. Ndipo lerolino tiri ndi mwaŵi wa kukhala m’paradaiso wauzimu, popeza chiyambire 1919, Yehova walenga mkhalidwe wauzimu wokulira kaamba ka anthu ake. Inde, Mboni za Yehova ziri ndi zifukwa zambiri zowonjezereka za kukhalira zoyamikira. Tifunikira kufunsa kuti: Kodi kuyamikira kwathu kuli kozama motani kulinga kwa Mulungu? Ndipo kodi ndimotani mmene tingasonyezere ife eni kukhala oyamikira m’zana lino la 20?

Kufanana Kwamakono

13, 14. Ngakhale kuti Akristu sali pansi pa Lamulo la Mose, kodi kufanana kulikonse kungachitidwe kaamba ka iwo kuchokera ku lamulo la chachikhumi?

13 Akristu sali pansi pa Lamulo la Mose lomwe linandandalitsa mmene angasonyezere kuyamikira kwa Mulungu. (Agalatiya 3:24, 25) “Nsembe” yathu ya chilemekezo kwa Yehova iri “chipatso cha milomo yovomereza dzina lake.” (Ahebri 13:15) Ichi, chotero, chiri njira yokulira imene Akristu odzipereka angasonyezere kuyamikira kwa Mulungu. Koma kufanana kosangalatsa kungatengedwe kuchokera ku malamulo a chachikhumi, zopereka, ndi kufunkha.

14 Chachikhumi chinatanthauza kupereka unyinji wachindunji wa gawo limodzi la khumi​—ndipo panalibe kusiyana pakati pa ichi. Mofananamo, lerolino pali malamulo achindunji amene ali pa onse a atumiki a Yehova, popandanso kusiyanitsa. Tonse tiyenera kukumana pamodzi mokhazikika, ndipo tiyenera kulalikira mwapoyera mbiri yabwino ya Ufumu wa Yehova ndi kuthandiza ena kukhala ophunzira a Kristu.​—Ahebri 10:24, 25; Mateyu 24:14; 28:19, 20.

15. Kodi ndi zisonyezero za mtundu wanji za mitima yoolowa manja m’masiku amakono ano zimene zimafanana ndi zija zovumbulidwa ndi makonzedwe a zopereka ndi kufunkha m’Israyeli wakale?

15 Kumbukirani, kachiŵirinso, makonzedwe a zopereka ndi zofunkha. Unyinji wachindunji sunasonyezedwe. Mofananamo, Malemba samakhazikitsa unyinji wachindunji wa nthaŵi kaamba ka aliyense wa Mboni za Yehova kuthera mu utumiki wopatulika. Unyinji wa nthaŵi yoperekedwa ku kuphunzira Mawu a Mulungu ndi kulalikira kwa ena wasiidwa ku chisonkhezero cha mitima yoolowa manja, yopanda dyera. Mofananamo, unyinji wa zopereka zakuthupi kaamba ka kupititsa patsogolo zikondwerero za Ufumu zasiidwa ku kulamulira kwa mtima wa aliyense. Kuzama kwa chiyamikiro kudzagamulapo kuti kaya mmodzi wa atumiki a Mulungu lerolino adzabweretsa “miyulu pa miyulu” kapena kokha zokha zokwanira kuti apulumuke. (2 Mbiri 31:6) Mofanana ndi nkhani ya Israyeli, ngakhale kuli tero, ukulu umene mmodzi anasonyezera chiyamikiro, kunali kuchuluka kwa madalitso olandiridwa kuchokera kwa Mulungu.

Njira Zosonyezera Kuyamikira

16-18. Ndi m’njira zachindunji zotani zimene Akristu odzipereka angadzisonyezere iwo eni oyamikira?

16 Imodzi ya njira zachindunji kwambiri za kusonyezera kuyamikira kwa Yehova iri kudzilowetsa mu utumiki wa nthaŵi zonse. Kodi kuyamikira kwanu kuli kokulira mokwanira kaamba ka mtima wanu kukhala wofuna chimenecho? Chawonedwa bwino kuti mpainiya wa chipambano amafunikira choyamba kukhala ndi chikhumbo cha kutumikira ndipo kenaka mikhalidwe yoyenera. Pamene kuyamikira kuli kwamphamvu, chikhumbo chosonkhezera cha kutumikira Mulungu mokwanira chimakula mu mtima woyamikira. Kodi mmenemu ndi mmene mumamverera? Ngakhale ngati mkhalidwe wanu wa panthaŵi ino sumalola kugawanamo kwanu mu utumiki wa nthaŵi zonse, ichi sichifunikira kuthetsa mzimu wa upainiya. Mungapereke chirikizo la mtima wonse ndi chilimbikitso kwa apainiya.

17 Ngati muli wosakhoza kuchita upainiya tsopano, kodi inu mungachite upainiya wothandizira kwa nthaŵi ndi nthaŵi? Pali nyengo zapadera chaka chirichonse pamene mpingo Wachikristu umalimbikitsa kuyesayesa koposa kwanthaŵi zonse mu ntchito yolalikira. Miyezi ya chirimwe, mwachitsanzo, iri yabwino kwa ambiri, ndipo mu October muli ntchito yowonjezereka m’chigwirizano ndi ndawala ya kulembetsa magazini. M’chigwirizano ndi kuwonjezereka kwa nthaŵi mu utumiki wopatulika, lamulolo limakhala lowona lakuti kuyamikira kumatulutsa kupereka koolowa manja.

18 Njira ina yachindunji ya kusonyezera kuyamikira iri kuchirikiza programu yomanga ya teokratiki yomwe ikuchitika kuzungulira pa dziko lapansi. M’maiko ambiri, Nyumba za Ufumu zatsopano ziri kumangidwa, ndipo nyumba zomwe ziripo zikukulitsidwa chifukwa cha kudzazidwa koposa muyezo. Maholo Osonkhanira Atsopano akumangidwa, ndipo kufutukula ku kuwonjezereka ku Nyumba za Beteli ndi mafakitale. Iyo iri njira yogwira ntchito yotani nanga ya kusonyezera chiyamikiro kwa Yehova​—kugawira kwathu ntchito kapena chuma kuti zisamalire maprojekiti omanga amenewa!

Chitsanzo Chabwino cha Mkazi Wamasiye Wosowa

19. Nchiyani chimene chimakusangalatsani inu koposa ponena za mkazi wamasiye wosowa pa kachisi?

19 Chitsanzo chodziŵika kwambiri cha m’Baibulo cha kusonyeza kuyamikira mwa kupereka koolowa manja kwa zinthu zakuthupi chiri chija cha mkazi wamasiye wolongosoledwa ndi Yesu. (Luka 21:1-4) Iye angakhale anazindikira kuti ndalama zake ziŵiri za mtengo wochepa choterozo zikanachita kusiyana kochepera ponena za ubwino wa zinthu zakuthupi wa kachisi ndi awo otumikira kumeneko. Koma iye sanayang’ane pa kachisi ndi ansembe omwe anali kutumikira kumeneko ndi kulingalira kwa iyemwini: ‘Iwo amakhala bwino koposa mmene ndimachitira ndipo ali ndi nyumba yabwino kuposa yanga yonyozeka.’ Zowona, kachisi anali womangidwa mwa mtengo wapatali ndi wokongola. “Anakonzedwa ndi miyala yokoma ndi zopereka.” (Luka 21:5) Koma chimenecho sichinaletse mkazi wamasiyeyo kupanga chopereka. Iye anafuna kudzisonyeza iyemwini kukhala woyamikira kwa Yehova, osati kwa anthu omwe anali kutumikira pa kachisi.

20. Ndimotani mmene tingasonyezere mkhalidwe wokhumbirika wonga uja wosonyezedwa ndi mkazi wamasiye wosauka?

20 Anthu a Yehova lerolino aphunzira kuchokera ku chitsanzo ichi. Mofanana ndi mkazi wamasiye wosowayu, iwo amadziŵa kuti zopereka zawo, zochuluka kapena zochepa, zimaperekedwa kwa Mulungu. Ndipo iwo ali otsimikiziridwa za kudziŵa kuti gulu la padziko lapansi la Yehova linakonzedwa motero kotero kuti palibe munthu ndi mmodzi yemwe amapeza phindu mwa chuma. Malo a Sosaite amangidwa ndi kugwiritsiridwa ntchito kotero kuti akonzekeretse ogwira ntchito amphamvu kupeza chotulukapo chokulira mu mtundu wotulutsidwa wa maBaibulo ndi zothandizira Baibulo ndi m’kutumikira zikondwerero za Ufumu. Uku kuli kusiyana kotheratu ndi kugwiritsira ntchito molakwa kochititsa manyazi kwa ndalama zoperekedwa komwe kunasimbidwa posachedwapa m’chigwirizano ndi alengezi ena a pa wailesi ya kanema.

Zikumbutso ku Kuyamikira Ziri Zopindulitsa

21, 22. Kodi ndi chotulukapo chotani chimene zikumbutso zachikondi za kudzisonyeza ife eni oyamikira zimatulutsa m’mitima yoyamikira?

21 Aisrayeli anafunikira zikumbutso zokhazikika za thayo lawo kulinga kwa Yehova, makamaka la chifuno cha kusonyeza mzimu woyamikira. Mwachisawawa, pamene nkhani zimenezi zinabweretsedwa ku chisamaliro chawo, kuyamikira kunadzutsidwanso m’mitima yawo, ndipo ichi chinatulukamo m’kusonyeza koposa kwa mawu chiyamikiro chawo chotokosa. Iwo anali ofunitsitsa kupereka “miyulu pa miyulu” ya zokolola kwa Yehova kuti zigwiritsiridwe ntchito pa nyumba ya kulambira kwake.

22 Chotero lolani “Israyeli wa Mulungu” wa dziko lino ndi “khamu lalikulu” la anzawo nthaŵi zonse kudzimva m’njira yofananayo. (Agalatiya 6:16; Chivumbulutso 7:9) Lolani kuti mitima yawo yoyamikira iwasonkhezere iwo kupereka “miyulu pa miyulu” ya chitamando kwa Yehova. Kenaka iwo anganene mowonadi kuti: “Tikudzisonyeza ife eni oyamikira kwa Mulungu wathu wachikondi ndi woolowa manja, Yehova.”

Kodi Mumakumbukira?

◻ Nchifukwa ninji Akristu mokhazikika amafunikira kufufuza ukulu wa kuyamikira kwawo?

◻ Nchifukwa ninji anthu a Yehova nthaŵi zonse akhala ndi chopangitsa chowonjezereka kaamba ka chiyamikiro?

◻ Ndi m’njira zachindunji zotani zimene Aisrayeli akasonyezera kuyamikira kwawo kwa Yehova?

◻ Mofanana ndi Aisrayeli, ndi zinthu zachindunji zotani zimene tingachite kuti tisonyeze kuyamikira?

◻ Nchiyani chimene tingaphunzire kuchokera kwa mkazi wamasiye wosowa pa kachisi?

[Chithunzi patsamba 7]

Aisrayeli anasonyeza kuyamikira mwa kupereka chachikhumi ndi zoyamba kucha ndi mwa kupanga makonzedwe kaamba ka osauka kufunkha m’minda yawo

[Chithunzi patsamba 8]

Wamasalmo anayamikira Yehova kaamba ka ntchito Zake zodabwitsa ndi malingaliro kulinga kwa anthu Ake

[Zithunzi patsamba 10]

Mboni za Yehova lerolino zimasonyeza kuyamikira mwakugawana mu utumiki wa m’munda ndi m’maprojekiti omanga a teokratiki, limodzinso ndi kupanga mphatso zakuthupi

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena