Dziŵani Abale Anu
1 Baibulo limati bwenzi lenileni ndi munthu amene amakukakamira kusiyana ndi mbale wako, amene nthaŵi zonse amakukonda ndipo amakhala wokhulupirika, ndiponso amakuthandiza pakaoneka tsoka. (Miy. 17:17; 18:24) Ngati tikuyesetsa kuti tidziŵane ndi kukondana, mabwenzi oterowo sadzatisoŵa mumpingo.—Yoh. 13:35.
2 Timakhala ndi mipata yabwino yoti tingazoloŵerane ndi abale athu misonkhano isanayambe ndiponso pambuyo pake. Bwanji osafika mofulumira ndi kutsalira pang’ono misonkhano itatha kuti musangalale ndi mayanjano abwino ndi ena? Chezani ndi abale osiyanasiyana, kuphatikizapo achikulire, okhala ndi chidziŵitso chochuluka ndi achichepere kapena amantha.
3 Yambitsani Makambitsirano: Musangopereka moni kwa abale anu. Mungayambitse makambitsirano mwa kuwafotokozera zimene mwakumana nazo mu utumiki wakumunda, nsonga yosangalatsa ya m’magazini atsopano, kapena munganene za misonkhano yomwe yangotha kumeneyo. Mungaphunzire zambiri za abale anu mwa kukhala womvetsera wabwino, kuwalimbikitsa kusimba zokumana nazo zawo ndi zimene akuphunzira. Kungofunsa mmene wina anadziŵira Yehova kungavumbule zochuluka. Ena anakumanapo ndi zochitika zolimbitsa chikhulupiriro, pamene ena panopa akupirira mikhalidwe imene ambiri sangailingalire. Kuzindikira zimenezi kudzatithandiza, ife monga mabwenzi enieni, kukhala atcheru ndi ofuna kuthandiza pa zosoŵa za ena.
4 Khalani Aubwenzi kwa Wina ndi Mnzake: Mwana wake atamwalira, mlongo wina anali kuvutika kuimba nyimbo za Ufumu zimene zimanena za chiukiriro. Anakumbukira kuti: “Nthaŵi ina mlongo wina amene anali kumbali ina ya mipando anandiona ndikulira. Iye anabwera pomwe ine ndinali nandikupatira, ndi kuimba nane nyimbo yonseyo. Ndinadzazidwa ndi chikondi cha abale ndi alongo ndipo ndinali wachimwemwe chifukwa chakuti tinafika pamisonkhanopo, pozindikira kuti nkumene chithandizo chathu chili, ku Nyumba ya Ufumu kumeneko.” Tikhale aubwenzi kwa abale athu mwa kuwatonthoza pamene kuli kofunika ndi kuwalimbikitsa nthaŵi zonse.—Aheb. 10:24, 25.
5 Pamene dziko lakaleli likupitirizabe kukhala lotsendereza, tiyeni titsimikize mtima pa kudziŵa bwino abale athu. Kulimbikitsana koona kumeneku kudzakhaladi dalitso kwa aliyense.—Aroma 1:11, 12.