Misonkhano Yautumiki ya September
Mlungu Woyambira September 7
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu Waufumu. Pendani bokosi lakuti “Lingaliro.”
Mph. 15: “Tingachite Ntchito Zoposa.” Mafunso ndi mayankho. Limbikitsani onse kukhala ndi zolinga zabwino za chaka chatsopano chautumiki ndi kuyesetsa kuzikwaniritsa.—Onani Uminisitala Wathu, masamba 116-18.
Mph. 20: “Apainiya Athandiza Ena.” Mkulu alongosole kuti kuwonjezera pa kuphunzitsidwa m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki, makonzedwe apangidwa oti apainiya azithandiza ena paokhapaokha mu utumiki. Afunse mafunso ozikidwa pankhaniyo ndi kupempha omvetsera kuikapo ndemanga, makamaka apainiya ndi ofalitsa amene aloŵetsedwa m’programuyo. Pendani mmene mungakhalire ndi zotulukapo zabwino kwambiri. Apainiya angafotokoze mmene asangalalira ndiponso kupindula mwakuthandiza nawo ofalitsa ena. Ofalitsa amene athandizidwa angasimbe mmene akuyamikirira makonzedwe achikondi ameneŵa ndi kutchula malingaliro amene anawathandiza kupeza chipambano ndi chimwemwe mu utumiki.
Nyimbo Na. 172 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira September 14
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti.
Mph. 15: Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? Nkhani. Tidzayamba kuphunzira brosha limeneli mlungu wamaŵa paphunziro la buku. Limbikitsani onse kuti azikonzekera pasadakhale ndi kufika paphunziro lililonse kotero kuti azoloŵerane nalo ndi kuphunzira mmene angaphunzitsire ena. Ŵerengani ndime yomwe ili pansi pa kamutu kakuti “Mmene Mungagwiritsire Ntchito Brosha Lino.” Gwiritsirani ntchito mfundo za mu Nsanja ya Olonda ya January 15, 1997, masamba 16-17, kuti mugogomezere kufunika kwa kuphunzitsa ndi mafunso, malemba, ndi zithunzi zomwe zili m’broshalo. Ochititsa maphunziro a buku ayenera kupatsa chitsanzo amene amachititsa maphunziro a Baibulo a panyumba mwa kusalankhulapo kwambiri ndiponso mwa kusaloŵetsamo nkhani zina.—Onani Utumiki Wathu Waufumu wa June 1996, tsamba 3, ndime 5.
Mph. 20: Kodi Tinachita Bwanji Chaka Chatha? Mlembi ndi woyang’anira utumiki akupenda lipoti la utumiki la mpingo ndi chiŵerengero cha ofika pamisonkhano m’chaka chapitachi. Akutchula mbali zolimbikitsa za lipotilo ndi kusumika malingaliro pa mbali zofunika kuwongolera. Kodi munali ndi 100 peresenti ya ofalitsa ochita nawo utumiki mu August? Fotokozani zimene akulu adzagwirirapo ntchito kwambiri m’miyezi imene ikubwerayi, kuphatikizapo kuthandiza onse kukhala ofalitsa okhazikika. Kambiranani nsonga zoyenerera kuchokera palipoti lapapitapo la woyang’anira dera.
Nyimbo Na. 144 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira September 21
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Mbiri Yateokrase.
Mph. 15: Zosoŵa za pampingo.
Mph. 20: “Dziŵani Abale Anu.” Mafunso ndi mayankho. Phatikizanipo nsonga za mu Nsanja ya Olonda ya October 1, 1988, masamba 10-11. Limbikitsani onse kuti aziyamba ndiwo kufuna kuzoloŵerana ndi ena.
Nyimbo Na. 34 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira September 28
Mph. 12: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kuti apereke malipoti autumiki a September. Limbikitsani onse kulingalira zogwira ntchito ya kunyumba ndi nyumba mokulirapo m’October kuti agaŵire magazini ochuluka. Onani Utumiki Wathu Waufumu wa October 1996 tsamba 8, kaamba ka malingaliro a mmene mungakonzere maulaliki. Chitirani chitsanzo cha kugaŵira magazini pogwiritsa ntchito magazini atsopano, ndipo sonyezani mmene mungauzire mwininyumba za chopereka cha magaziniwo. Tengani magazini oti mugwiritsire ntchito pamapeto a mlungu.
Mph. 20: “Oyang’anira Amene Amatitsogolera—Woyang’anira Utumiki.” Nkhani ya woyang’anira utumiki. Atafotokoza za ntchito yake, iye alongosole zimene mpingo ungachite kuti uwonjezere utumiki pampingopo ndi kukhala ogwira mtima kwambiri mu utumikiwo.
Mph. 13: Nchiyani Chimapanga Wofalitsa Wabwino Wampingo? Nkhani, ndi kukambapo kwa omvetsera. Si koyenerera kuti munthu akhale ndi maluso kapena matalente apamwamba; m’malo mwake, nkofunika kwambiri kuti tonsefe tikhale ndi mzimu wofunitsitsa umene umasonyeza chikondi, kudzichepetsa, changu, ndi kuyamikira. Pemphani omvetsera kuti apereke zifukwa zake mikhalidwe iyi ili yofunika: (1) mzimu wachimwemwe, (2) kufika nthaŵi zonse ndi kutengamo mbali m’misonkhano, (3) kufunitsitsa kuvomera ndi kugwira ntchito, (4) kugwirizana ndi akulu ndi makonzedwe opangidwira mpingo, (5) kukhaladi wofunitsitsa kuthandiza ena, ndi (6) kuchita utumiki wakumunda mokhazikika ndi kumapereka lipoti mwachangu mwezi uliwonse.
Nyimbo Na. 25 ndi pemphero lomaliza.