Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 1/15 tsamba 16-17
  • Chiŵiya Chatsopano Chothandiza Nacho Anthu Kuphunzira Zimene Mulungu Amafuna

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chiŵiya Chatsopano Chothandiza Nacho Anthu Kuphunzira Zimene Mulungu Amafuna
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Nkhani Yofanana
  • Gwiritsani Ntchito Kabuku Kakuti Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Thandizani Osoŵa Chidziŵitso Kuti Azindikire
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
  • Mmene Mungagwiritsire Ntchito Kabuku Kakuti, Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Kodi Mukugwiritsa Ntchito Bulosha la Mulungu Amafunanji Kuyambitsira Maphunziro?
    Utumiki wathu wa Ufumu—2002
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 1/15 tsamba 16-17

Chiŵiya Chatsopano Chothandiza Nacho Anthu Kuphunzira Zimene Mulungu Amafuna

“MALONGOSOLEDWE ake osavuta, olunjika, ndi achikondi adzabala zipatso zosayembekezereka. Nkhani zake zalongosoledwa m’njira yosavuta ndi yokoma yoti munthu woona mtima aliyense, wofunitsitsa kudziŵa zinthu adzasonkhezereka kunena kuti, ‘Mulungu ali ndithu mwa inu.’” (1 Akorinto 14:25) Anatero mmodzi wa Mboni za Yehova wa ku Thailand polongosola brosha latsopano lakuti, Kodi Mulungu Amafunanji Kwa Ife? Linatulutsidwa ndi Watch Tower Society pa Misonkhano Yachigawo yakuti “Amithenga a Mtendere Waumulungu” mu 1996/97.

Cholinga cha broshali la masamba 32 la maonekedwe onse nchakuti likhale lophunzirira Baibulo. Limafotokoza ziphunzitso zoyambirira za Baibulo. Mawu ake ndi osavuta kumva ndi olondola, kulongosola momveka bwino zimene Mulungu amafuna kwa ife. Oliŵerenga adzalimvetsa popanda vuto lililonse. Kodi phunziro la Baibulo mungalichititse motani m’brosha latsopanoli?

Gwiritsirani ntchito mafunso. Kuchiyambi cha phunziro lililonse kuli mafunso. M’mabulaketiwo otsatira funso lililonse, muli manambala a ndime zopezamo mayankho. Mafunsoŵa mungawafunse koyambirira kupereka chithunzi cha nkhaniyo ndi pambuyo pake monga kubwereramo. Mwachitsanzo, poyamba phunziro la Baibulo lapanyumba, mungafunse wophunzirayo mafunsowo kuti mumve chonena chake. M’malo mowongolera pompo mayankho alionse olakwika, mungangopitiriza ndi phunziro. Mutamaliza phunzirolo, mungabwerere ku mafunsowo kuti muone ngati wophunzirayo tsopano atha kuwayankha mogwirizana ndi Baibulo.

Ŵerengani malemba. M’phunziro lililonse, mawu achidule onena za choonadi cha Baibulo ali ndi malemba owachirikiza. Pakuti malemba ambiri angosonyezedwa, osagwidwa mawu, nkofunika kulimbikitsa wophunzirayo kuŵerenga malembawo m’Baibulo lake. Afunikira kumaŵerenga ndi kusinkhasinkha pa Mawu a Mulungu asanayambe kuwagwiritsira ntchito pamoyo wake.​—Yoswa 1:8.

Sonyezani Zithunzi. Broshalo lili ndi zithunzi zochuluka ndi zifaniziro​—pamodzi zoposa 50. Zimenezi zaikidwamo osati kuti zisangalatse maso chabe komanso kuti zithandizire kuphunzitsa. Mwachitsanzo, maphunziro omalizira aŵiri (limodzi patsamba limodzi, pamasamba oyang’anizana) ali ndi mitu yakuti “Kuthandiza Ena Kuchita Chifuniro cha Mulungu” ndi “Chosankha Chanu cha Kutumikira Mulungu.” Zithunzi zomwe zili pamasambawo zikusonyeza kupita patsogolo kwa munthu mmodzimodzi, kumsonyeza pamene akuchitira umboni wamwamwaŵi, akukhala ndi phande m’ntchito ya kunyumba ndi nyumba, kudzipatulira kwake, ndiyeno kubatizidwa. Mwa kusonyeza wophunzira zithunzi zimenezi, mumamthandiza kuona masitepe ofunikira kuti munthu atumikire Mulungu.

Bwanji ngati munthu wokondwerera saŵerenga bwino kapena satha kuŵerenga mpang’ono pomwe? Sosaite ikuika brosha latsopano limeneli pa kaseti m’zinenero zingapo. Kasetiyo idzakhala ndi mawu a broshali ndi malemba ambiri osagwidwa mawu. Lajambulidwa motere: Funso loyamba liŵerengedwa, ndiyeno ndime yotsatirapo (kapena zotsatirapo) yopereka yankho, pamodzi ndi malemba ena osagwidwa mawu. Ndiyeno funso lotsatira liŵerengedwa, kenako ndime ndi malemba opereka yankho, tero basi. Wophunzirayo angamvetsere kasetiyo pokonzekera phunziro. Kasetiyo ingagwiritsidwenso ntchito pochititsa phunziro.

Opezekapo pamsonkhano wachigawo anali ofunitsitsa kugwiritsira ntchito brosha latsopano limeneli mu utumiki wawo wakumunda. Mwachitsanzo, masiku oŵerengeka chabe atalandira broshalo, apainiya aŵiri (alaliki anthaŵi zonse) a ku United States analigaŵira kwa mwamuna ndi mkazi ongokhalira limodzi achichepere omwe iwowo ankawachezera. Pamene aŵiri okhalira limodziwo anayang’ana pa mpambo wa zamkati, anakopeka ndi phunziro lakuti “Machitachita Amene Mulungu Amadana Nawo.” “Nthaŵi zonse ndaphunzitsidwa kuti sikutheka kuti Mulungu ade chinthu​—iye ndi chikondi,” anatero mkazi wachichepereyo. “Ndiyamba ndi yomweyi kuŵerenga.” Pamene apainiya aŵiriwo anabwererako mlungu wotsatira, mkazi wachichepereyo anati: “Ndakhala ndikuŵerenga brosha latsopano lija. Komatu nkovuta kwenikweni kuchita zonse zomwe tiyenera kuchita. Yehova sali wokondwera nafe ayi​—sitili okwatirana. Komano tapanga chosankha. Tapanga makonzedwe akuti tikakwatirane pa Lachisanu mlungu wamaŵa.” Atakumbatira apainiya okwatiranawo, iwo anaonjezera nati: “Tikupepesa kuti phunziro lathu lakhala lophonyaphonya, koma tsopano zinthu zidzatipepukira kwambiri.”

Yesetsani mwakhama kugwiritsira ntchito brosha latsopano lakuti Mulungu Amafunanji. Lili chiŵiya chabwino kwambiri chothandizira ena kudziŵa zimene Mulungu amafuna.

[Zithunzi patsamba 17]

Kodi mudzaligwiritsira ntchito motani brosha latsopanolo?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena