Thandizani Osoŵa Chidziŵitso Kuti Azindikire
1 Mwa ntchito yopanga ophunzira, timaphunzitsa ena zimene Mulungu amafuna kwa iwo. (Mat. 28:19, 20) Mboni zoposa mamiliyoni asanu padziko lonse zikuyesetsa mwamphamvu kuchita zimenezo. Zimene zimasonyeza chipambano sindizo kuchuluka kwa maola, mabuku ogaŵiridwa, kapena maphunziro a Baibulo omwe ayambidwa ayi. Timakwaniritsa cholinga chathu pamene anthu azindikira ndi kulabadira zimene akuphunzira.
2 Kuthandiza ena mwauzimu kumaphatikizapo “kuzindikiritsa osoŵa chidziŵitso.” (Sal. 119:130, NW) Anthu amakhudzika mtima ndi kusonkhezereka kokha ngati ‘amvetsa lingaliro lake.’ (Mat. 15:10, NW) Pamene ntchito yathu ikuwonjezeka ndi kukula, timaona kwambiri kufunika kwa kulankhula ndi kuphunzitsa m’njira yosavuta kumva. Ndiye chifukwa chake Sosaite yafalitsa brosha lakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? Ilo lili ndi maphunziro a kosi yonse ya ziphunzitso zoyambirira za Baibulo. Maphunziro ake ngaafupi, mawu ake ngosavuta kumva, ndipo zilangizo zake nzosavuta kumvetsa, zinthu zimene zimachititsa brosha limeneli kukopa anthu ambiri.
3 Tidzagaŵira broshali limodzi ndi magazini m’miyezi ya April ndi May. Kungakhale bwino ngati polinganiza ntchito zanu za mlungu ndi mlungu za utumiki, mulinganiza kugaŵira magazini pamasiku a Loŵeruka koma kugaŵira broshali mu utumiki wanu mkati mwa mlungu wonse. Perekani broshali kwa anthu amene kumbuyoku alandira mabuku mofunitsitsa. Kumbukirani kuti lingagwire ntchito bwino kwambiri pophunzitsa ana, anthu a chinenero cha kwina, ndi aja osatha kuŵerenga bwino.
4 Gwiritsirani Ntchito Mafikidwe Osavuta: Pogaŵira brosha la Mulungu Amafunanji, pitani patsamba 2, pamene limafotokoza kuti “brosha lino lakonzedwa monga kosi yophunzira Baibulo.” Pitani pa ndime 3 ya patsamba 3 kuti musonyeze chifukwa chake munthuyo afunikira kuphunzira Baibulo. Dzutsani chidwi chake ndi mitu ya maphunziro ena imene ivumbula choonadi cha Baibulo chapafupi. Sonyezani mmene broshali limasangalatsira pophunzira, ndipo funsani ngati angafune kuti inuyo muzimthandiza.
5 Chititsani Phunziro Lopita Patsogolo: Cholinga chathu sindicho kungochititsa maphunziro—tikufuna kupanga ophunzira amene adzakhala achirikizi olimba a kulambira koona. Brosha limeneli mungalimalize m’milungu yochepa yokha ndipo liyenera kukuloŵetsani m’phunziro la buku la Chidziŵitso. (Onani mawu amtsinde patsamba 31.) Kungoyambira pachiyambi, thandizani wophunzira kuzindikira gulu la Yehova. (Onani buku la Kukambitsirana, tsamba 143.) Gogomezerani kufunika kwa misonkhano ya mpingo, ndipo fotokozani kuti kupezekapo kumapereka chidziŵitso chonse cha mmene angachitire kulambira koona.—Aheb. 10:24, 25.
6 Kukhala ndi phande lokwanira pantchito yapadera imeneyi mu April ndi May kudzatipatsadi chimwemwe chimene chimadza ndi kuthandiza anthu oona mtima ‘kutenga luntha’ lotsogolera ku moyo.—Miy. 4:5.