Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 7/99 tsamba 1
  • Kukonzekereratu Kumadzetsa Chimwemwe

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kukonzekereratu Kumadzetsa Chimwemwe
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
  • Nkhani Yofanana
  • Kukonzekera—Mfungulo ya Chipambano
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Ngati Umagwira Mtima, Ugwiritsireni Ntchito!
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
  • Phindu la Kukonzekera
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • ‘Tumikirani Yehova Mokondwera’
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
km 7/99 tsamba 1

Kukonzekereratu Kumadzetsa Chimwemwe

1 Kutenga mbali mu utumiki wakumunda kumatipatsa chimwemwe chochuluka. (Sal. 89:15, 16) Ndithudi, kukonzekera ndi njira yaikulu yopezera chimwemwe chochulukacho. Ngati tikonzekera bwino, timakwaniritsa zambiri, ndipo tikakwaniritsa zambiri, chimwemwe chathu chimakhalanso chochuluka.

2 Gwiritsani Ntchito Zida Zimene Zimaperekedwa: Yambani kukonzekera kwanu mwa kuŵerenga ndi kupenda nkhani za mu Utumiki Wathu wa Ufumu. Nthaŵi zambiri umakhala ndi maulaliki olinganizidwa bwino amene amakonzedwa kuti akuthandizeni kulalikira uthenga wa Ufumu mosavuta ndi mogwira mtima. Mudzapeza zitsanzo zogonjetsera zigomeko zambiri zotsutsa zimene anthu amapereka. Umapereka malingaliro olunjika a mmene tingapangire ulendo wobwereza wogwira mtima, ndi cholinga choyambitsa phunziro la Baibulo. Muli ndi ufulu wogwiritsa ntchito malingaliro amenewa kumlingo umene mungathe. Kuphatikiza apo, muli ndi buku la Kukambitsirana, limene limapereka mayambidwe osiyanasiyana komanso mmene tingayankhire anthu oletsa makambitsirano, zikumakuthandizani kukhala wogwira mtima kwambiri m’mikhalidwe yambiri imene mumakumana nayo.

3 Pendani chofalitsa chimene muzikagaŵira, sankhani mfundo yodzutsa chidwi imodzi kapena ziŵiri zimene mungaonetse mwininyumba. Nkhani zodzutsa chidwi zimene mwamva kapena mwaŵerenga zingakutsegulireni mpata woyambitsa makambitsirano. Lingaliranitu zigomeko zotsutsa zimene anthu ambiri amene mumakumana nawo amapereka, ndipo khalani ndi mfundo zingapo m’maganizo za mmene mukayankhire. Kenako khalani ndi mphindi zingapo zoti muyesere zimene mukalankhule pakhomo.

4 Fikani pa Msonkhano Uliwonse wa Utumiki: Mvetserani mosamalitsa Msonkhano wa Utumiki pamene malingaliro olembedwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu akufotokozedwa, kupendedwa, ndi pamene akupanga zitsanzo. Onani malingaliro amene mukuona kuti mungawaphatikize pa ulaliki wanu. Kumbukirani mikhalidwe yofala imene mwakhala mukukumana nayo mu utumiki, ndipo ganizani za njira zimene mungaperekere umboni wogwira mtima kwambiri. Lankhulani zimenezi ndi ofalitsa ena musanayambe msonkhano ndi pamapeto pake.

5 Mungakhale otsimikiza kuti ngati muli ‘okonzekera ntchito yonse yabwino,’ mudzapeza chimwemwe ndi chipambano chochuluka pothandiza ena kupeza njira ya moyo.—2 Tim. 2:21.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena