Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 7/99 tsamba 2
  • Misonkhano ya Utumiki ya July

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Misonkhano ya Utumiki ya July
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
  • Timitu
  • Mlungu Woyambira July 5
  • Mlungu Woyambira July 12
  • Mlungu Woyambira July 19
  • Mlungu Woyambira July 26
Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
km 7/99 tsamba 2

Misonkhano ya Utumiki ya July

CHIDZIŴITSO: Utumiki Wathu wa Ufumu udzakhala ndi ndandanda ya Msonkhano wa Utumiki wa mlungu uliwonse panthaŵi yamsonkhano. Mipingo ingasinthe mofunikira kuti ikapezeke pa Msonkhano Wachigawo wa “Mawu Aulosi a Mulungu” ndi kupenda mfundo zazikulu za pologalamuyo kwa mphindi 30 pa Msonkhano wa Utumiki wa mlungu wotsatira. Kupenda pologalamu ya msonkhano wachigawo ya tsiku lililonse kuyenera kugaŵiridwa msonkhanowo usanafike kwa abale oyenerera atatu, amene adzakhoza kugogomezera mfundo zofunika. Kupenda kokonzekeredwa bwino kumeneku kudzathandiza mpingo kukumbukira mfundo zazikulu zogwiritsa ntchito aliyense payekha ndi zogwiritsa ntchito m’munda. Ndemanga za omvetsera ndi zokumana nazo zimene zinasimbidwa ziyenera kukhala zachidule.

Mlungu Woyambira July 5

Nyimbo Na. 6

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu. Simbani lipoti la utumiki wakumunda la April la dziko lino ndi la mpingowo. Mbiri Yateokalase.

Mph. 20: “Pemphererani Thandizo la Yehova.” Kambani mawu oyamba m’mphindi yosapitilira imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Fotokozani mmene mapemphero alionse oona amathandizira utumiki wachipambano. Pemphani omvetsera kusimba zokumana nazo zosonyeza mmene mapemphero apanthaŵi yake athandizira utumiki wawo.—Onani Nsanja ya Olonda ya October 15, 1996, tsamba 32.

Mph. 15: Gwiritsani Ntchito Bwino Mabolosha. Nkhani ndi zitsanzo. Fotokozani chifukwa chake mabolosha ali zida zabwino mu utumiki wathu. Amafotokoza bwino nkhani zimene zimakopa chidwi anthu ambiri, amasimba mutu umodzi wa nkhani mwachidule, ndipo amafotokoza ziphunzitso za Malemba mosavuta. Tchulani mabolosha ogaŵiridwa mwezi uno, ndipo sonyezani amene mpingo wanu uli nawo ambiri. Onetsani zitsanzo ziŵiri kapena zitatu zachidule za maulaliki.

Nyimbo Na. 181 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira July 12

Nyimbo Na. 103

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti.

Mph. 15: “Kukonzekereratu Kumadzetsa Chimwemwe.” Nkhani ndi kufunsa ena. Fotokozani chifukwa chake kukonzekera kuli kofunika m’ntchito ya utumiki wakumunda ndi mmene kumatithandizira kupeza chimwemwe chachikulu mu zimene timachita. (Onani Bukhu Lolangiza la Sukulu, tsamba 39, ndime 1-3.) Funsani ofalitsa odziŵa aŵiri kapena atatu anene mmene amakonzekerera asanapite mu utumiki ndi mmene zawathandizira. Simbani zokumana nazo za mu Nsanja ya Olonda ya April 15, 1993, tsamba 30, zosonyeza kagwiritsidwe ntchito kabwino ka buku la Kukambitsirana pokonzekera utumiki.

Mph. 20: “Tiyeni ‘Tinene Mfundo Yathu Mwachidule!’” Kukambirana ndi omvetsera komanso zitsanzo. Pendani lingaliro lililonse loyenera kunena kuti tidzutse chidwi cha mwininyumba. Khalani ndi ofalitsa ozoloŵera achite zitsanzo za mawu oyamba angapo othandiza. Pemphani omvetsera kupereka malingaliro ena komanso kusimba zokumana nazo zolimbikitsa zosonyeza zimene zimagwira ntchito kumaloko.

Nyimbo Na. 183 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira July 19

Nyimbo Na. 31

Mph. 10:  Zilengezo za pampingo.

Mph. 15: Zosoŵa za pampingo.

Mph. 20: “Misonkhano Yachigawo ya 1999 ya ‘Mawu Aulosi a Mulungu.’” (Ndime 1-10) Mafunso ndi mayankho. Werengani ndime 4, 5, 6 ndi 10. Gogomezerani chifukwa chake kuli kofunika kupezeka pamsonkhano wonse, kuphatikizapo mapologalamu a Lachisanu. Tsimikizani kufunika kotsatira malangizo a Sosaite otenga chakudya chathu kumsonkhano tsiku lililonse.

Nyimbo Na. 189 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira July 26

Nyimbo Na. 184

Mph. 15: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani onse kupereka malipoti a utumiki wakumunda a July. Bokosi la Mafunso.

Mph. 10: “Pologalamu Yatsopano ya Msonkhano Wadera.” Nkhani. Lengezani tsiku la msonkhano wadera wotsatira. Limbikitsani achatsopano kuganizira zokabatizidwa. Pemphani onse kupezeka papologalamu yonse.

Mph. 20: “Misonkhano Yachigawo ya 1999 ya ‘Mawu Aulosi a Mulungu.’” (Ndime 11-20) Mafunso ndi mayankho. Werengani ndime 15-19. Gwiritsani ntchito malemba operekedwawo pogogomezera chifukwa chake kavalidwe, kapesedwe, ndi khalidwe lathu zili nkhani zofunika kuzisamalira.

Nyimbo Na. 14 ndi pemphero lomaliza.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena