Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 7/06 tsamba 3-4
  • Dikirani Yehova

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Dikirani Yehova
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • Nkhani Yofanana
  • Nthawi ya Chakudya Chauzimu Ndiponso Yosangalala
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
  • Tsatirani Khristu Podzisungira Ulemu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
  • Yamikani Yehova mu Msonkhano Waukulu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
  • Misonkhano Yachigawo Ndi Nthawi Imene Timalambira Mulungu Mosangalala
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2010
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
km 7/06 tsamba 3-4

Dikirani Yehova

1. Kodi mutu wa msonkhano wachigawo ndi wakuti chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani uli woyenerera?

1 “Yehova ndiye Mulungu wa chiweruzo,” analemba motero Yesaya. “Odala ali onse amene am’dikira Iye.” (Yes. 30:18b) Pali nkhani zambiri za m’Baibulo zimene zimanena za chiweruzo cha Mulungu pa adani ake ndi mmene anapulumutsira atumiki ake okhulupirika. Kodi nkhani zimenezo zimawaphunzitsa chiyani anthu olambira Yehova masiku ano? Kodi tingachite chiyani tsopano kuti tikonzekere “tsiku la Yehova lalikulu loopsa”? (Yow. 2:31, 32) Msonkhano wathu wachigawo umene ukubwera wakuti, “Chipulumutso Chayandikira” udzatilimbikitsa kuganizira za mafunso amenewa ndi kudziyesa tokha. Udzatithandiza kudikira Yehova.

2. Kodi tingasonyeze bwanji kuyamikira msonkhano wathu wachigawo?

2 Kodi mwakonza kale zokapezekapo ndi kukapindula kwa masiku onse atatu a msonkhanowo? Mwachitsanzo, kodi mwapempha kale tchuthi kwa abwana anu cha masiku atatu amenewo, kuti mukapezeke pamsonkhanowo? Musaganize kuti zimenezi zidzangochitika zokha ayi. Pempherani za nkhaniyi. Kenaka, pemphani kwa abwana anu. (Neh. 2:4, 5) M’pofunikanso kuti tisakonze mochedwa za mmene tidzayendere, malo amene tidzagone, ndi zinthu zina zofunika. Kukonzekera bwino kotereku kumasonyeza kuti tikuyamikira kwambiri chakudya chauzimu chimene Yehova amatikonzera. Akulu ayenera kudziwa za anthu amene akufunikira kuti awathandize kukonzekera msonkhano umenewu, makamaka anthu okalamba a mumpingo mwawo.—Agal. 6:10.

3. Kodi anthu a Yehova ayenera kusonyeza makhalidwe otani ku malo omwe kukuchitikira msonkhano?

3 Khalidwe Labwino Limalemekeza Mulungu: Tikasonkhana anthu ambiri pa misonkhano yachigawo, khalidwe lathu labwino limapereka umboni wabwino kwa anthu a m’dera la msonkhanowo. Kodi timafunikira kuchita chiyani? Ngati tili ku mahotela, malesitilanti ndi malo ena amalonda kufupi ndi malo amene kukuchitikira msonkhano, anthu amene tikuchita nawo zinthu ayenera kulimbikitsidwa ndi makhalidwe athu achikristu, monga kuleza mtima, kufatsa, kudziletsa, ndi kuganizira ena. (Agal. 5:22, 23; Afil. 2:4) Tonsefe tiyenera kusonyeza chikondi chimene “sichichita zosayenera, sichitsata za mwini yekha, sichipsa mtima.” Ngakhale ngati patachitika zovuta zina, tidzafunikira ‘kuchita zonse ku ulemerero wa Mulungu.’—1 Akor. 10:31; 13:5.

4. Kodi makolo angathandize bwanji ana awo kukhala ndi khalidwe limene limalemekeza Yehova?

4 Msonkhano wina wachigawo utatha, mkulu wa pa hotela ina anachita chidwi kwambiri ndi khalidwe komanso maonekedwe a achinyamata athu, moti anafotokoza kuti akanakonda kuti “alendo a pa hotelapo azikhala a Mboni za Yehova basi.” Zimenezi ndi zosangalatsa kwambiri. Ndiponso zikusonyeza kuti makolo mumaphunzitsa bwino ana anu ndiponso mumawayang’anira bwino. Ana ayenera kuyang’aniridwa bwino nthawi zonse. (Miy. 29:15) Timafuna kuti khalidwe labwino la ana athu lilemekeze Yehova ndi kukondweretsa mtima wake.—Miy. 27:11.

5. Kodi tingalemekeze bwanji Yehova pa kavalidwe ndi kudzikongoletsa kwathu?

5 Kuvala ndi Kudzikongoletsa Mwaulemu: Aliyense angathandizire kuti msonkhano wathu upereke chithunzi chabwino kwa anthu, mwa kupewa kuvala ndi kudzikongoletsa motsatira kwambiri masitayelo, mopanda ulemu, kapena mooneka ngati tikupita kocheza. Zimenezi zikutanthauza popita ndi pochokera ku malo a msonkhano, pothandiza kukonza malo a msonkhano, ndiponso pomvetsera msonkhanowo. Monga atumiki a Mulungu, nkhawa yathu yaikulu ndi dzina la Yehova ndi mmene anthu angamuonere, osati zofuna zathu kapena mmene timaonekera ayi. Mitu ya mabanja ili ndi udindo woonetsetsa kuti anthu a m’banja mwawo akuoneka bwino ndiponso avala modzilemekeza nthawi zonse.—1 Tim. 2:9.

6. N’chifukwa chiyani tifunikabe kuoneka mwaulemu pa nthawi imene tikupuma pambuyo pa msonkhano?

6 Timafunikanso kuoneka chimodzimodzi pa nthawi imene tikupuma ku mahotela, ku masitolo ndi ku malesitilanti. Ndi bwino kuvala zovala zimene tinavala ku msonkhano ngati tikukadya kwinakwake titamaliza misonkhano. Kuvala mabaji a msonkhano kungatipatse mpata wolalikira mwamwayi.—2 Akor. 6:3, 4.

7. Kodi tingathandizire bwanji kuti msonkhano wathu ukhale wadongosolo ndi wachimwemwe? (Onani “Zofunika Kukumbukira pa Msonkhano Wachigawo.”)

7 Yesaya ananeneratu kuti: “Yehova adzadikira, kuti akukomereni mtima, ndipo chifukwa chake Iye adzakuzidwa, kuti akuchitireni inu chifundo.” (Yes. 30:18a) Kuyamikira chifundo cha Yehova ndi chisomo chake kutipangitse kum’lemekeza ndi khalidwe lathu komanso maonekedwe athu pamene tikukasonkhana pa misonkhano yathu yachigawo. Msonkhano wachigawo wakuti “Chipulumutso Chayandikira” ulemekeze Mulungu wathu ndipo utithandize kum’dikira!

[Bokosi patsamba 4]

Zofunika Kukumbukira pa Msonkhano Wachigawo

◼ Nthawi ya Mapulogalamu: Kwa masiku onse atatu msonkhano uzidzayamba 8:30 m’mawa. Kutatsala mphindi zochepa kuti chigawo cha msonkhano chiyambe, tcheyamani azidzakhala papulatifomu, nyimbo zamalimba za Ufumu zikuimbidwa. Panthawi imeneyi, tonse tiyenera kukhala pansi kuti msonkhano uyambe. Tsiku loyamba msonkhano udzatha 4:45 madzulo, lachiwiri udzatha 4:05 madzulo, ndipo tsiku lachitatu udzatha 3:10 madzulo.

◼ Koimika Magalimoto: Kulikonse komwe kudzachitikire msonkhano kudzakhala malo okwanira oimikapo magalimoto ndi njinga. Tikukulimbikitsani nonse kudzamvera zimene akalinde amene aikidwa kusamalira utumiki umenewu angakuuzeni. Eniake a magalimoto afunikira kudzaonetsetsa kuti zitseko za magalimoto azitseka bwinobwino, ndipo nawonso eniake a njinga adzaonetsetse kuti njinga zawo ndi zokhoma, asanakakhale pansi.

◼ Kusunga Malo: Tingasungire malo anthu okhawo amene tidzapite nawo pagalimoto imodzi kapena amene timakhala nawo nyumba imodzi.

◼ Zopereka: Pokonzekera msonkhano wachigawo pamapita ndalama zambiri. Tingasonyeze kuyamikira mwa kupereka ndalama mwaufulu zothandiza pa ntchito ya padziko lonse, ku Nyumba ya Ufumu yathu kapena pamsonkhanopo. Macheke operekedwa pamsonkhano wachigawo azilembedwa kuti ndalamazo apatse “Watch Tower.”

◼ Ovutika Kumva: Nkhani za msonkhanowu adzazimasulira m’chinenero cha manja cha ku America, ku misonkhano yachigawo ya Chingelezi ku Blantyre ndi ku Lilongwe. Zimenezi zidzalengezedwa pachiyambiyambi pa chigawo choyamba.

◼ Chakudya cha Masana: Chonde mudzabwere ndi chakudya chanu cha masana m’malo mochoka pamalo a msonkhano kukagula chakudya panthawi yopuma. Mungatenge zakudya zimene ena amakonda kutenga akakhala ndi zochita zina zapadera ngati zimenezi. Mungatenge zinthu monga sangweji, tchipisi, mabisiketi, zipatso, mpunga wophika, mbatata, chinangwa, mtedza wokazinga, ndi zakumwa.

◼ Kujambula Mawu: Musadzalumikize zipangizo zilizonse zojambulira mawu ku magetsi kapena ku zokuzira mawu za pamsonkhano ndipo muyenera kudzazigwiritsa ntchito m’njira yoti zisasokoneze ena.

◼ Kujambula Zithunzi: Ngati mukujambula zithunzi, musagwiritse ntchito fulashi msonkhano uli m’kati.

◼ Foni za M’manja: Muyenera kuzitchera kuti zisalire, n’kusokoneza ena.

◼ Ngozi Ndiponso Matenda Amwadzidzidzi: Ngati mwadzidzidzi pangafunike thandizo lililonse lokhudza zachipatala, dziwitsani kalinde aliyense amene mulinaye pafupi, iye adzadziwitsa Dipatimenti ya Zachipatala mwamsanga kotero kuti abale amene aphunzitsidwa kusamalira mavuto amenewa angaone kukula kwake kwa vutolo ndi kupereka thandizo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena