Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 9/15 tsamba 8-11
  • Kodi N’kusungiranji Malonjezo Anu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi N’kusungiranji Malonjezo Anu?
  • Nsanja ya Olonda—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Yehova Amakwaniritsa Malonjezo Ake
  • Malonjezo a Yehova ndi Tsogolo Lathu
  • Kusunga Malonjezo Athu kwa Mulungu
  • Kusunga Malonjezo Athu Kumalimbikitsa Ena Kutikhulupirira
  • Njira Zina Zosungira Malonjezo Athu
  • Madalitso Ochuluka Kuchokera kwa Mulungu
  • Kodi Mungadalire Malonjezo a Ndani?
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Malonjezo Amene Mungadalire
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Kodi Mumakwaniritsa Zimene Mwalonjeza?
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2017
  • Yehova Amakwaniritsa Zomwe Walonjeza
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1999
w99 9/15 tsamba 8-11

Kodi N’kusungiranji Malonjezo Anu?

“SANKHANI munthu amene amalonjeza zochepa; iye adzakukhumudwitsani pang’ono,” anatero malemu Bernard Baruch yemwe anali mlangizi wa pulezidenti ku America. M’dziko lamakonoli zikukhala ngati malonjezo amangonenedwa kuti aswedwe. Atha kukhala malumbiro a ukwati, mapangano a zamalonda, kapena malonjezo okhala panyumba ndi ana nthaŵi yaitali. Ambiri amaiŵala tanthauzo la mawu akuti “munthu wabwino ndi amene amasunga malonjezo ake.”

Inde, anthu ambiri safuna kusunga malonjezo awo. Ena amangofulumira kulonjeza zinthu zoti sangazikwaniritse kapena kungophwanya lonjezolo chifukwa kuchita zimenezi n’kosavuta.

Kunena zoona, kusunga lonjezo kungakhale kovuta ngati pangachitike zinthu zina zosayembekezereka. Koma kodi kuswa lonjezo kumabweretsadi mavuto? Kodi muyenera kuona malonjezo anu kukhala nkhani yaikulu? Kupenda mwachidule chitsanzo cha Yehova Mulungu kudzatithandiza kuzindikira chifukwa chake tiyenera kuiona nkhaniyi kukhala yofunika.

Yehova Amakwaniritsa Malonjezo Ake

Timalambira Mulungu amene dzina lake lokhalo limaphatikizapo kukwaniritsa malonjezo ake. M’nthaŵi za Baibulo dzina kaŵirikaŵiri linkafotokoza za munthuyo. Ndi mmene zilili ndi dzina lakuti Yehova, lomwe limatanthauza kuti “Amachititsa Kukhalako.” Choncho dzina la Mulungu limeneli limaphatikizapo mfundo yakuti Mulungu adzakwaniritsa malonjezo ake ndi kuchita zolinga zake.

Mogwirizana ndi dzina lake, Yehova anasunga lonjezo lililonse lomwe anauza mtundu wa Israyeli wakale. Ponena za malonjezo ameneŵa, Mfumu Solomo anavomereza kuti: “Wolemekezeka ndi Yehova amene anapumulitsa anthu ake Aisrayeli, monga mwa zonse analonjezazo; sanatayika mawu amodzi a mawu ake onse abwino, amene analankhula ndi dzanja la Mose mtumiki wake.”​—1 Mafumu 8:56.

Yehova n’ngwodalirika kwambiri moti mtumwi Paulo ananena kuti: “Pamene Mulungu analonjezana naye Abrahamu, popeza analibe wamkulu woposa kum’lumbira, analumbira pa Iye yekha.” (Ahebri 6:13) Inde, dzina lokhalo la Yehova ndi umunthu wake zimatitsimikizira kuti iye sadzabweza maganizo pa malonjezo ake, ngakhale kuti kuchita zimenezo kungam’tayitse zambiri. (Aroma 8:32) Pokhala kuti Yehova amakwaniritsa malonjezo ake, ifeyo tili ndi chiyembekezo chimene chili nangula wa moyo wathu.​—Ahebri 6:19.

Malonjezo a Yehova ndi Tsogolo Lathu

Chiyembekezo chathu, chikhulupiriro chathu, ndi moyo wathu weniweniwo zimadalira pa kukwaniritsidwa kwa malonjezo a Yehova. Kodi n’chiyembekezo chiti chimene tili nacho? “Monga mwa lonjezano lake [la Mulungu] tiyembekezera miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano mmenemo mukhalitsa chilungamo.” (2 Petro 3:13) Malemba amatipatsanso maziko a chikhulupiriro kuti “kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.” (Machitidwe 24:15) Ndipo tingathe kutsimikiza kuti kudzakhala zochuluka kuposa moyo uno. Inde, chomwe mtumwi Yohane ankatchula kuti “lonjezano” ankanena “moyo wosatha.” (1 Yohane 2:25) Komabe, malonjezo a Yehova amene ali m’Mawu ake sakhudza za m’tsogolo zokha ayi. Ngakhale tsopano amachititsa kuti moyo wathu wa tsiku ndi tsiku ukhale watanthauzo.

Wamasalmo anaimba kuti: “Yehova ali pafupi ndi onse akuitanira kwa Iye, . . . nadzamva kufuula kwawo.” (Salmo 145:18, 19) Mulungu akutitsimikiziranso kuti, “iye alimbitsa olefuka, nawonjezera mphamvu iye amene alibe mphamvu.” (Yesaya 40:29) Ndipo n’kotothozadi kudziŵa kuti Mulungu ‘sadzalola ife kuyesedwa koposa kumene tikhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo’! (1 Akorinto 10:13) Ngati ife eni taona kukwaniritsidwa kwa maulosi ameneŵa, tikudziŵa kuti Yehova titha kumukhulupirira kotheratu. Tikaganiza za mapindu amene talandira kuchokera ku malonjezo ambirimbiri amene Mulungu amanena ndi kuwasunga, kodi tiyenera kuona motani malonjezo athu kwa iye?

Kusunga Malonjezo Athu kwa Mulungu

Kudzipatulira kwathu kwa Mulungu mosakayika ndilo lonjezo lofunika kwambiri lomwe tingapange. Mwa kuchita zimenezi, timasonyeza kuti tikufuna kutumikira Yehova mpaka kalekale. Ngakhale kuti malamulo a Mulungu sali olemetsa, kuchita chifuniro chake nthaŵi zina kungakhale kovuta chifukwa chakuti tikukhalabe m’dongosolo loipa la zinthu. (2 Timoteo 3:12; 1 Yohane 5:3) Koma ‘tikangogwira chikhasu’ ndi kukhala atumiki odzipatulira a Yehova komanso ophunzira a Mwana wake, Yesu Kristu, sitiyeneranso kuyang’ana kumbuyo pa zinthu za dziko zomwe tinazisiya kale.​—Luka 9:62.

Pamene tipemphera kwa Yehova, tingafunitsitse kum’lonjeza kuti tidzayesetsa kulimbana ndi zofooka zathu, kukulitsa makhalidwe achikristu, ndiponso kulimbikira pa zochitika zina zateokalase. Kodi chidzatithandiza n’chiyani kuchitadi zomwe talonjeza?​—Yerekezani ndi Mlaliki 5:2-5.

Malonjezo oona amachokera mumtima ndi m’maganizo. Choncho, tiyeni titsimikizire malonjezo athu kwa Yehova mwa kuulula zakukhosi m’pemphero, kulongosola moona mtima nkhaŵa zathu, zolinga zathu, ndiponso zofooka zathu. Kupempherera lonjezo lathu kudzathandiza kuti tithe kulisunga. Tiyenera kumaona malonjezo athu kwa Mulungu ngati ngongole. Ngongole ikakhala yaikulu, imafunika kumabwezako pang’onopang’ono. Mofananamo, malonjezo athu ambirimbiri omwe timalonjeza Yehova, adzatenga nthaŵi kuti tiwakwaniritse. Koma mwa kupereka kwa iye zomwe tingathe kaŵirikaŵiri, timasonyeza kuti tikunenadi zoona, ndipo iye adzatidalitsa.

Tingasonyezenso kuti timaona malonjezo athu kukhala ofunika mwa kuwatchula m’pemphero, mwinamwake tsiku lililonse. Zimenezi zidzasonyeza Atate wathu wakumwamba kuti ndife oona mtima, ndipo zidzakhala ngati chikumbutso nthaŵi ndi nthaŵi. Davide anatisiyira chitsanzo chabwino pankhani imeneyi. M’nyimbo, iye anapempha Yehova kuti: “Imvani mfuu wanga, Mulungu, mverani pemphero langa . . . Ndidzaimba zolemekeza dzina lanu ku nthawi zonse, kuti ndichite zoŵinda zanga tsiku ndi tsiku.”​—Salmo 61:1, 8.

Kusunga Malonjezo Athu Kumalimbikitsa Ena Kutikhulupirira

Ngati timapeputsa malonjezo athu kwa Mulungu, ndiye kuti timateronso ndi malonjezo athu kwa Akristu anzathu. Sitiyenera kumachita zina kwa Yehova kwinaku n’kumachita zosiyana kwa abale athu. (Yerekezani ndi 1 Yohane 4:20.) Pa Ulaliki wake wa pa Phiri, Yesu anati: ‘Koma manenedwe anu akhale, Inde, inde; Iyayi, iyayi.’ (Mateyu 5:37) Kuonetsetsa kuti mawu athu nthaŵi zonse amakhala okhulupirika, ndi njira imodzi ‘yochitira chokoma iwo apabanja la chikhulupiriro.’ (Agalatiya 6:10) Lonjezo lililonse lomwe timasunga limalimbikitsa ena kutikhulupirira.

Vuto lomwe kuphwanya lonjezo kumabweretsa limakula makamaka ngati ndi pankhani yokhudza ndalama. Kaya akubweza ngongole, kugwirira ena ntchito, kapena kukwaniritsa pangano la zamalonda, Mkristu ayenera kuchitadi zomwe analonjeza. Zimenezi zimakondweretsa Mulungu ndipo zimalimbitsa kukhulupirirana kumene kuli kofunika kwambiri kuti abale “akhale pamodzi.”​—Salmo 133:1.

Choncho, kulephera kukwaniritsa pangano, kungabweretse mavuto mumpingo ndiponso kwa anthu amene akukhudzidwa. Woyang’anira woyendayenda wina anati: “Mikangano ya zamalonda, imene kaŵirikaŵiri imachitika chifukwa cha mapangano omwe penapake wina amaganiza kuti mnzakeyo sanakwaniritse mbali ina ya panganolo, nthaŵi zambiri imadziŵika kwa anthu ambiri. Zikatero, abale amagaŵikana pofuna kukhalirana mbali, ndipo mtendere umasokonekera pa Nyumba ya Ufumu.” Taonani tsono kufunika kwake koyamba taganiza mozama tisanachite pangano lililonse, ndiyeno n’kuchita cholilemba!a

Tiyeneranso kukhala osamala pamene tigulitsa zinthu zokwera mtengo kapena kulimbikitsa kuikiza ndalama, makamaka ngati ife eni tikupezapo phindu pa malondawo. Mofananamo, tiyenera kukhala osamala kwambiri kuti tisakokomeze mapindu a zinthu zina, mankhwala kapena kulonjeza kuti tidzabweza ndalama zochuluka koposa zomwe tinabwereka. Chikondi chiyenera kusonkhezera Akristu kufotokoza mosabisa mavuto alionse amene angakumane nawo. (Aroma 12:10) Pokhala kuti abale ambiri alibe chidziŵitso chokwanira m’zamalonda, iwo angakhulupirire malangizo athu chabe chifukwa chakuti ndife abale awo m’chikhulupiriro. Zingakhale zachisoni zedi ngati kukhulupirirana kumeneku kwawonongeka!

Monga Akristu, sitingatengere machitachita a malonda amene ali osaona mtima ndiponso amene amanyalanyaza zofuna za ena. (Aefeso 2:2, 3; Ahebri 13:18) Kuti tikhale ndi chiyanjo cha Yehova monga ‘ogonera m’chihema chake,’ tiyenera kukhala okhulupirika. Ngakhale ngati ‘talumbira kwa tsoka lathu, sitisintha ayi.’​—Salmo 15:1, 4.

Yefita, woweruza wa Israyeli anaŵinda kuti ngati Mulungu adzam’thandiza kupambana nkhondo yake ndi Aamoni, adzapereka monga nsembe yopsereza kwa Yehova aliyense yemwe adzayamba kukumana naye pochokera kunkhondoyo. Zinachitika kuti munthu amene anayamba kukumana naye anali mwana wake wamkazi yekhayo, koma Yefita sanasinthe maganizo. Mwana wakeyo atagwirizana nazo kuchokera pansi pa mtima, anam’perekadi nsembe kuti azitumikira pakachisi wa Mulungu nthaŵi zonse, nsembe yomwe inali yopweteka komanso yamtengo wapatali m’njira zambiri.​—Oweruza 11:30-40.

Makamaka oyang’anira mumpingo ali ndi udindo womamatira ku mapangano awo. Pa 1 Timoteo 3:2, pamanena kuti woyang’anira ayenera kukhala “wopanda chilema.” Mawu ameneŵa ndi matembenuzidwe a mawu achigiriki otanthauza kuti “wosagwidwa chifukwa chopalamula, wosaimbidwa mlandu, kapena wosapezeka ndi mlandu.” Komanso “samangotanthauza munthu wa mbiri yabwino chabe, koma munthu amene mbiri yakeyo imamuyenera.” (A Linguistic Key to the Greek New Testament) Pokhala kuti woyang’anira ayenera kukhala wopanda chilema, malonjezo ake ayenera kukhalanso odalirika nthaŵi zonse.

Njira Zina Zosungira Malonjezo Athu

Kodi tiyenera kuwaona motani malonjezo athu kwa anthu amene sali Akristu anzathu? Yesu anati: “Muwalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuona ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa Kumwamba.” (Mateyu 5:16) Mwa kutsimikiza kuti timachitadi zomwe timanena, tingakope anthu ena kukhala ndi chidwi ndi uthenga wathu wachikristu. Mosasamala kanthu za kuchepa kwa anthu oona mtima padziko lonse lapansi, anthu ambiri amakondabe kukhulupirika. Kusunga malonjezo athu ndi njira imodzi yosonyeza kuti timakondadi Mulungu ndi anzathu ndi yokopera okonda chilungamo.​—Mateyu 22:36-39; Aroma 15:2.

M’chaka chawo chautumiki cha 1998, Mboni za Yehova zinathera maola oposa biliyoni imodzi kulengeza poyera uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. (Mateyu 24:14) Uthenga wina ungakhale utaloŵa m’makutu ogontha ngati ife sitinasunge mapangano athu m’zamalonda kapena pa zinthu zina. Popeza kuti timaimira Mulungu wa choonadi, anthu amayembekezera ife kuchita zinthu mokhulupirika. Mwa kukhala odalirika ndi oona mtima, ‘timakometsera chiphunzitso cha Mpulumutsi wathu Mulungu m’zinthu zonse.’​—Tito 2:10.

Mu utumiki wathu, tili ndi mwayi wosunga malonjezo athu pamene tibwererako kukachezera aja omwe anaonetsa chidwi mu uthenga wa Ufumu. Tikanena kuti tidzabweranso, tiyenera kuchitadi zomwezo. Kubwererako tikalonjeza ndiyo njira ‘yosamana oyenera kulandira zabwino.’ (Miyambo 3:27) Mlongo wina analongosola zimenezi motere: “Nthaŵi zambiri, ndakumana ndi anthu achidwi amene amandiuza kuti Mboni ina inalonjeza kuti idzabweranso koma sinabwerenso. Inde, ndimadziŵa kuti nthaŵi zina eninyumbawo sapezeka panyumba kapena kuti zinthu zina zimalepheretsa Mbonizo kubwererako. Koma sindifuna kuti wina adzachite kufika ponena zimenezi ndili ine, chotero ndimayesetsa kuchita zotheka kuti ndim’pezenso panyumba. Ndimakhulupirira kuti ndikagwiritsa mwala munthu, zidzapereka chithunzi choipa ponena za Yehova ndi abale anga onse.”

Nthaŵi zina, sitingafune kubwererako chifukwa chakuti tikuganiza kuti munthuyo sakufuna. Mlongo yemweyo analongosola kuti: “Sindiweruza munthu malinga ndi chidwi chake. Zomwe zakhala zikundichitikira zandithandiza kuzindikira kuti kaŵirikaŵiri zimene umaganiza poyamba n’zolakwika. Chotero ndimayesetsa kukhala wodekha, ndikumaona munthu aliyense monga mbale ndi mlongo wam’tsogolo.”

Mu utumiki wathu wachikristu ndi m’zinthu zina zambiri, tiyenera kusonyeza kuti mawu athu ali odalirika. N’zoonadi kuti zinthu zina n’zosavuta kunena kusiyana ndi kuzichita. Munthu wanzeru anati: “Anthu ambiri abukitsa yense kukoma mtima kwake; koma ndani angapeze munthu wokhulupirika?” (Miyambo 20:6) Motsimikiza, tingathe kukhala okhulupirika komanso ochitadi zomwe tanena.

Madalitso Ochuluka Kuchokera kwa Mulungu

Kulonjeza dala zinthu zomwe sitingazikwanitse ndi kusaona mtima ndipo kungafanizidwe ndi kulemba cheke pamene munthuwe ulibe ndalama kubanki. Koma eti mphotho ndi madalitso ake kuchuluka zomwe timalandira chifukwa chosunga malonjezo athu! Dalitso lina lomwe timalandira chifukwa chokhulupirika ndilo chikumbumtima chabwino. (Yerekezani ndi Machitidwe 24:16.) M’malo movutika mtima, timakhala okhutira ndi amtendere. Komanso, mwa kusunga malonjezo athu, timathandizira mgwirizano mumpingo, womwe umadalira kukhulupirirana kwathu. ‘Mawu athu a choonadi’ amatitsimikizira kukhala atumiki a Mulungu wa choonadi.​—2 Akorinto 6:3, 4, 7.

Yehova amachitadi zomwe wanena, ndipo amadana ndi “lilime lonama.” (Miyambo 6:16, 17) Mwa kutsanzira Atate wathu wakumwamba, timayandikira kwa iye. Ndithudi, tili ndi chifukwa chabwino chosungira malonjezo athu.

[Mawu a M’munsi]

a Onani nkhani ya mutu wakuti “Lembani!” mu Galamukani! yachingelezi ya February 8, 1983, masamba 13-15.

[Zithunzi patsamba 10]

Yefita anasunga lonjezo lake, ngakhale kuti kuchita zimenezo kunali kopweteka

[Zithunzi patsamba 11]

Ngati mwalonjeza kuti mudzabweranso, konzekerani bwinobwino kudzaterodi

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena