Thandizani Ophunzira Baibulo Kukhala Ofalitsa Uthenga Wabwino wa Ufumu
1 Yesu anapatsa ophunzira ake ntchito yaikulu kwambiri. Ntchitoyi yafotokozedwa pa Mateyo 28:19, 20. Palembali, ophunzira a Khristu anauzidwa kuti apange ophunzira, omwe nawonso adzagwire ntchito yopanga ophunzira. Mwa kuchita zimenezi, iwo anayala maziko a ntchito yomaliza yolengeza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu padziko lonse, yomwe ikuchitika m’masiku otsiriza ndiponso apadera kwambiri amene tikukhala ano.—Mat. 24:14.
2 Anthu amene tikuphunzira nawo Baibulo angathe kukhala ana athu kapena anthu ena. Timafunitsitsa kuwathandiza anthu amenewa kuzindikira udindo umene ali nawo wothandiza ena kukhala ophunzira a Yesu Khristu.—Luka 6:40.
3 Akonzekeretseni Kulalikira: Tizilimbikitsa anthu amene timaphunzira nawo Baibulo kuti aziuza ena zimene akuphunzira. Tiziwafokozera zokumana nazo zolimbikitsa za muutumiki wakumunda. Tiziphunzitsa ana athu kuyambira ali aang’ono kuchita nafe utumiki malinga ndi zimene angakwanitse kuchita. (Sal. 148:12, 13) Zolankhula ndi zochita zathu zizisonyeza kuti timayamikira utumiki.—1 Tim. 1:12.
4 Yehova amagwiritsa ntchito anthu okhawo amene amavomereza ndi kutsatira zofuna zake zomwe ndi zolungama. N’zodziwikiratu kuti ofalitsa atsopano sadziwa zinthu zambiri ngati olengeza Ufumu obatizidwa ndi odzipereka kwa Mulungu. Komabe, iwo ayenera kukhulupirira ziphunzitso zoyambirira za m’Baibulo ndi kutha kuzifotokoza. (Onani buku la Gulu, tsa. 79 mpaka 82.) Iwo ayenera kuti anatuluka mu “Babulo Wamkulu,” sachita nawo ndale ndipo amafika pa misonkhano ya mpingo nthawi zonse.—Chiv. 18:2, 4; Yoh. 17:16; Aheb. 10:24, 25.
5 Mukaona kuti munthu amene mumaphunzira naye Baibulo akuyenerera kukhala wofalitsa wosabatizidwa, muyenera kudziwitsa woyang’anira wotsogolera zimenezo. Iye adzapeza akulu awiri oti mukumane nawo limodzi ndi wophunzira wanuyo. Cholinga chawo n’chakuti aone ngati akuyenerera kuyamba kufalitsa uthenga wabwino wa Ufumu pamodzi ndi mpingo monga wofalitsa wosabatizidwa. Kenako mudzakhala ndi mwayi wapadera wopitiriza kuthandiza wophunzira wanuyo poyenda naye limodzi muutumiki wakumunda.