Tikugwetsa Zinthu Zozikika Molimba
1 Kwa zaka mazana ambiri, Satana wagwiritsa ntchito ziphunzitso zonama ndi chinyengo kuumitsa mitima ndi maganizo a anthu ambiri. Iye wafalitsa ziphunzitso monga Utatu, kusafa kwa mzimu ndi moto wa helo. Amachititsa anthu kukayikira zakuti kuli Mlengi ndiponso kukayikira Baibulo. Zinthu monga kusankhana mitundu ndi kukonda dziko limene munthu anabadwira zimatchinga kuwala kwa choonadi. (2 Akor. 4:4) Kodi tingagwetse motani zikhulupiriro zozikika molimbazi?—2 Akor. 10:4, 5.
2 N’zozikika M’mitima Mwawo: Zikhulupiriro zimene munthu wakhala nazo kwa nthawi yaitali zimazikika molimba mu mtima mwake. Ena akhala akukhulupirira ziphunzitso zolakwika kungoyambira ali ana. Kuti tiwathandize anthu oterewa, tifunika kulankhula nawo mosonyeza kuti timalemekeza maganizo awo.—1 Pet. 3:15.
3 Tingasonyeze kuti timalemekeza anthu otero mwa kuwalola kufotokoza zimene amakhulupirira ndiponso chifukwa chake. (Yak. 1:19) Mwina amakhulupirira kuti mzimu sufa chifukwa chakuti abale awo anamwalira ndipo akulakalaka kuwaonanso. Kapenanso amakondwerera maholide chifukwa amawapatsa mpata wosangalala ndi achibale awo. Kumvetsera pamene iwo akufotokoza kungatithandize kudziwa maganizo awo ndi kuona mmene tingawayankhire mogwira mtima.—Miy. 16:23.
4 Tsanzirani Yesu: Yesu anatisiyira chitsanzo chabwino kwambiri pamene anayankha mafunso a munthu wodziwa Chilamulo. Poyankha, Yesu sanamuuze mayankho achindunji, amene mwina munthuyo akanawakana chifukwa cha zimene ankakhulupirira ndi mtima wake wonse. M’malomwake, Yesu anatchula Malemba, anafunsa munthuyo maganizo ake kenako anamuthandiza kuona mfundo yake pogwiritsa ntchito fanizo.—Luka 10:25-37.
5 Choonadi cha m’Mawu a Mulungu n’champhamvu kwambiri kuposa zikhulupiriro zonama zozikika m’mitima ya anthu a m’zipembedzo. (Aheb. 4:12) Ngati tikhala oleza mtima ndi kulankhula ndi anthu mowafika pa mtima, tingathandize anthuwo kusiya zikhulupiriro zonama ndi kulandira choonadi chomwe chingawamasule.—Yoh. 8:32.