Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira July 14
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Gwiritsani ntchito mfundo zimene zili pa tsamba 4 kapena mfundo zina zothandiza m’gawo lanu, pochita zitsanzo za zimene tinganene pogawira Nsanja ya Olonda ya July 1 ndi Galamukani! ya July.
Mph.20: “Kuthandiza Ofalitsa Osakhazikika ndi Ofooka.”a Nkhani yokambidwa ndi woyang’anira utumiki.
Mph.15: “Pindulani Pophunzira Buku la Yandikirani kwa Yehova.”b Nkhani yokambidwa ndi woyang’anira Phunziro la Buku la Mpingo. Pofotokoza ndime 1, tchulani za ndandanda yophunzirira. Pofotokoza ndime 2, werengani ndi kukambirana ndime 23 patsamba 25 la bukulo.
Mlungu Woyambira July 21
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Musankhe zilengezo zina mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno. Kumbutsani omvera kuti pobwera ku Msonkhano wa Utumiki mlungu wamawa, adzatenge Nsanja ya Olonda ya August 1 ndi Galamukani! ya August ndiponso kuti akakonzekere kudzafotokoza ulaliki wogwirizana ndi gawo lanu.
Mph.10: Zosowa za pampingo.
Mph.25: “Nthawi ya Chakudya Chauzimu Ndiponso Yosangalala.”c Yokambidwa ndi mlembi wa mpingo. Tchulani msonkhano wachigawo umene mpingo wanu udzapitako. Kambiranani bokosi lakuti, “Zofunika Kukumbukira pa Msonkhano Wachigawo.”
Mlungu Woyambira July 28
Mph.8: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa onse kupereka malipoti a utumiki wa kumunda a mwezi wa July. Werengani lipoti la maakaunti ndi mawu oyamikira zopereka olembedwa pa sitetimenti yochokera ku ofesi. Tchulani mabuku ogawira mu August, ndipo chitani chitsanzo cha mmene tingagawire bukulo.
Mph.17: “Kukonzekera Ndi Chinsinsi cha Maulendo Obwereza Aphindu.”d Khalani ndi chitsanzo cha mphindi zinayi chosonyeza m’bale akulankhula yekha pokonzekera maulendo obwereza. Iye akuona zimene anakambirana ndi anthu ndipo akusankha kupanga maulendo obwereza kwa anthu awiri mlungu uno. Kenako m’baleyo akuona zimene anakambirana ndi anthuwo aliyense payekha, akukhala ndi cholinga ndipo akuganizira mmene angachikwaniritsire. Akukonza zakuti akapemphe munthu mmodzi kuyamba naye phunziro la Baibulo. Koma kwa munthu winayo, akukonza zakuti akakulitse chidwi chake pogwiritsa ntchito mfundo za m’ndime 5.
Mph.20: Konzekerani Kugawira Magazini Atsopano. Nkhani yokambirana ndi omvera. Mutafotokoza mwachidule zimene zili mu Galamukani! ya August ndi Nsanja ya Olonda ya August 1, funsani omvera kuti afotokoze nkhani zimene anthu a m’gawo lanu angachite nazo chidwi ndiponso chifukwa chake. Pemphani omverawo kuti atchule mfundo za m’nkhanizo zimene akufuna kukagwiritsa ntchito. Kodi angafunse funso lotani kuti ayambe kukambirana ndi munthu? Kodi ndi lemba liti m’nkhaniyo limene angawerenge? Pogwiritsa ntchito ulaliki wachitsanzo wa mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno kapena mfundo zimene zafotokozedwa ndi omvera, chitani chitsanzo cha zimene tingachite pogawira magaziniwa.
Mlungu Woyambira August 4
Mph.10: Zilengezo za pampingo.
Mph.15: Kodi Ana Anu Ndi Okonzeka Kulalikira ku Sukulu? Nkhani ndi kukambirana ndi omvera. Tchulani mavuto amene Akhristu achinyamata amakumana nawo kusukulu. Fotokozani mmene makolo ndi ana awo angagwiritsire ntchito Watch Tower Publications Index kuti apeze mfundo zothandiza. Perekani zitsanzo. (Onani mutu waukulu wakuti “Schools,” ndi kamutu kakuti “experiences.”) Pemphani omvera amene analeredwa ndi makolo achikhristu kuti afotokoze zimene makolo awo anachita powathandiza kukonzekera mavuto ndi kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo kusukulu. Angatchulenso za malipoti amene anapemphedwa ku sukulu kuti alembe ndipo anagwiritsa ntchito nkhani za mu Galamukani! pokonzekera malipotiwo. Apempheni kuti afotokoze mmene kulalikira ku sukulu kunawatetezera.
Mph.20: “Tikugwetsa Zinthu Zozikika Molimba.”e Pemphani omvera kuti afotokoze mmene munthu amene ankawaphunzitsa Baibulo anawathandizira moleza mtima kusiya zikhulupiriro zonama za chipembedzo chawo zimene zinali zozikika mu mtima mwawo.
a Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
b Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
c Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
d Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
e Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.