Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 7/08 tsamba 4-6
  • Nthawi ya Chakudya Chauzimu Ndiponso Yosangalala

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nthawi ya Chakudya Chauzimu Ndiponso Yosangalala
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mwakonzekera Phwando Lauzimu?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
  • Tsatirani Khristu Podzisungira Ulemu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
  • Dikirani Yehova
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • Misonkhano Yachigawo Ndi Nthawi Imene Timalambira Mulungu Mosangalala
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2010
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
km 7/08 tsamba 4-6

Nthawi ya Chakudya Chauzimu Ndiponso Yosangalala

1. Kodi Yehova amapereka motani zosowa zauzimu za atumiki ake?

1 Yehova amapereka zosowa zauzimu za atumiki ake mwachikondi. Anthu ambiri m’dzikoli ali ndi njala yauzimu, koma ife timadya bwino mwauzimu. (Yes. 65:13) Njira imodzi imene Yehova amatidyetsera mwauzimu ndi misonkhano yathu yachigawo chaka chilichonse. Kodi mwayamba kale kukonzekera kuti mudzakhale nawo pa zigawo zonse za Msonkhano Wachigawo womwe ukubwerawu, wakuti “Mzimu wa Mulungu Umatitsogolera”? Pamsonkhanowu pakonzedwa chakudya chauzimu chokoma ndi chopatsa thanzi.

2. Kodi tikufunika kuchita chiyani pokonzekera msonkhano wachigawo?

2 Yambani Kukonzekera: “Zoganizira za wakhama zichulukitsadi katundu.” (Miy. 21:5) Choncho pofuna kutsimikizira kuti mwakonzekera kudzapezeka pa msonkhanowu masiku onse atatu, musalephere kulankhula ndi abwana anu kuti mudzatenge tchuthi. Ngati mudzafune malo ogona, kodi mwakonzeratu zimenezi? Mudzafunikiranso kukonzeratu chakudya chamasana kuti mudzadyere pa malo a msonkhanowo limodzi ndi abale anu. Konzani zoti tsiku lililonse muzidzafika pa malo a msonkhanowu mwamsanga kuti mupeze malo okhala ndiponso mukhale nawo poimba nyimbo ndi papemphero lotsegulira.

3. Kodi tikonzekere kudzavala zovala zotani?

3 Tionetsetse kuti zovala zathu zidzakhale zaulemu ndi zoyenera. (1 Tim. 2:9, 10) Misonkhano yachigawo imatipatsa mpata wabwino kwambiri wochitira umboni kwa anthu a m’dera la msonkhanowo. Mwa kuvala bwino pamene tili m’deralo ndiponso kuvala mabaji athu a msonkhano, timasiyana kwambiri ndi osakhulupirira ndipo anthu otiona amachita chidwi.

4. Kodi n’chiyani chingadzatithandize kuti tidzapindule kwambiri ndi msonkhano wachigawo limodzi ndi mabanja athu?

4 Dzamvetsereni Mwatcheru: Sitikufuna kudzaphonya mfundo ngakhale imodzi paphwando lauzimu limeneli. (Miy. 22:17, 18) Kuwerenga nawo malemba akamawerengedwa m’Baibulo ndiponso kulemba mfundo zachidule, kudzatithandiza kuika maganizo athu pa msonkhanowo. Ndiyeno madzulo tingamakambirane ndi abale athu mfundo zimene zatisangalatsa. Masiku ano zaoneka kuti achinyamata ena amakonda kukhala pamodzi n’kumacheza kapena kutumizirana mauthenga pafoni zam’manja msonkhano uli mkati. Ngati tili ndi ana aang’ono komanso achinyamata, zingakhale bwino kukhala nawo pamodzi n’kumamvetsera msonkhano m’malo mowalola kukakhala paokha ndi anzawo.

5. Kodi tidzachite chiyani kuti tidzasangalale kwambiri ndi msonkhano wachigawo?

5 Dzasangalaleni ndi Macheza: Chakudya chabwino chimakoma kwambiri kudyera limodzi ndi anzathu. (Miy. 15:17) Msonkhano wachigawo nawonso umasangalatsa kwambiri tikamacheza ndi abale ndi alongo athu. Choncho, ndi bwino kuti msonkhano usanayambe, panthawi yopuma ndiponso msonkhano utatha, tizidzacheza ndi anthu amene abwera pa msonkhanowo. (Sal. 133:1) Tcheyamani akadzatipempha kuti tikhale pansi nyimbo zamalimba zisanayambe, tidzasiye macheza athu n’kukhala pansi pokonzekera kuti msonkhano uyambe.

6. Fotokozani zimene munakumana nazo zosonyeza mmene tingalalikirire anthu a m’dera limene mukuchitikira msonkhano.

6 Dzakhaleni Atcheru Kuti Mudzalalikire: Nthawi zonse misonkhano yachigawo imatipatsa mpata wabwino wolalikira. Anthu ambiri obwera kumsonkhano amene amakadya ku lesitilanti msonkhano ukatha, amafunsidwa ndi ogwira ntchito m’malesitilantiwo ndiponso anthu ena za mutu wa msonkhano umene uli pa baji. Izi zimawapatsa mwayi wolalikira za choonadi. Anthu ena atafunsa za mutu wa msonkhano, anaitanidwa kuti abwere kudzamvera chigawo china cha msonkhanowo, ndipo anabweradi.

7. N’chifukwa chiyani tiyenera kudzakhala nawo pamsonkhano wachigawo ukubwerawu?

7 Zimatenga nthawi yaitali kukonza misonkhano, malo odzachitirapo misonkhanoyi, madipatimenti a msonkhano ndiponso kukonzekera nkhani. Ntchito yonseyi, imene abale ndi alongo amagwira chifukwa cha chikondi chawo pokonza phwando lauzimu limeneli, ikusonyeza kuti Yehova amakonda kwambiri anthu ake. Tiyeni tonse tidzakhalepo ndi kudzadya zonse zimene Yehova watikonzera. Tikadzatero, mosiyana ndi anthu a dzikoli, ‘tidzaimba ndi mtima wosangalala.’—Yes. 65:14.

[Bokosi patsamba 4]

Zofunika Kukumbukira pa Msonkhano Wachigawo

◼ Nthawi ya Mapulogalamu: Kwa masiku onse atatu msonkhano uzidzayamba nthawi ya 8:20 m’mawa. Kutatsala mphindi zochepa kuti pulogalamu iyambe, tcheyamani wa chigawo adzakhala pa pulatifomu pamene nyimbo zamalimba za Ufumu zikuimba. Tonse tiyenera kukhala pansi panthawi imeneyo kuti msonkhano uyambe mwadongosolo. Tsiku loyamba ndi lachiwiri msonkhano udzatha nthawi ya 3:55 madzulo, ndipo tsiku lachitatu udzatha nthawi ya 3:00 madzulo.

◼ Koimika Galimoto ndi Njinga: Kulikonse komwe kudzachitikire msonkhano kudzakhala malo okwanira oimikapo magalimoto ndi njinga. Tikukulimbikitsani nonse kudzamvera zimene akalinde amene aikidwa kuchita utumiki umenewu angakuuzeni. Eniake a magalimoto afunikira kudzaonetsetsa kuti zitseko za magalimoto azikhoma bwinobwino, ndipo nawonso eniake a njinga adzaonetsetse kuti njinga zawo ndi zokhoma, asanakakhale pansi.

◼ Kusungirana Malo: Tingasungire malo anthu okhawo amene tabwera nawo pagalimoto imodzi kapena amene timakhala nawo nyumba imodzi.

◼ Chakudya Chamasana: Mudzabwere ndi chakudya chanu chamasana m’malo mochoka pa malo a msonkhano kukagula chakudya panthawi yopuma. Mungatenge zakudya zimene ena amakonda kutenga akakhala ndi zochita zina zapadera ngati zimenezi. Mungatenge zinthu monga sangweji, tchipisi, mabisiketi, zipatso, mpunga, mbatata, chinangwa, mtedza wokazinga, ndi zakumwa. Mowa suloledwa pa malo a msonkhano.

◼ Zopereka: Pokonzekera msonkhano wachigawo pamapita ndalama zambiri. Timasonyeza kuyamikira mwa kupereka ndalama mwaufulu zothandiza pa ntchito ya padziko lonse, ku Nyumba ya Ufumu kapena kumsonkhano komweko. Macheke operekedwa pamsonkhano wachigawo azilembedwa kuti ndalamazo apatse “Watch Tower.”

◼ Ngozi Ndiponso Matenda Amwadzidzidzi: Ngati munthu pamsonkhano wadwala mwadzidzidzi, dziwitsani kalinde amene ali pafupi, ndipo iye mwamsanga adzadziwitsa a Dipatimenti ya Zachipatala kuti anthu odziwa bwino zachipatala amene alipo adzathe kuona mmene zinthu zilili ndiponso thandizo limene angapereke.

◼ Ovutika Kumva: Nkhani za msonkhanowu adzazimasulira m’chinenero cha manja, kumisonkhano yachigawo ya Chingelezi ku Blantyre ndi ku Lilongwe. Zimenezi zidzalengezedwa pachiyambi pa chigawo choyamba.

◼ Kujambula Mawu: Musadzalumikize zipangizo zanu zojambulira ku magetsi kapena ku zokuzira mawu za pamsonkhano ndipo muyenera kudzazigwiritsa ntchito m’njira yoti zisasokoneze ena.

◼ Mafomu Odziwitsira Ena za Munthu Wachidwi: Pofotokoza za munthu aliyense amene anaonetsa chidwi mutamulalikira mwamwayi panthawi ya msonkhano, gwiritsani ntchito mafomu a Kaonaneni ndi Wachidwi Uyu (S-43). Ofalitsa angabweretse fomu imodzi kapena awiri kumsonkhano. Mungapereke mafomu olembedwa bwinobwino ku Chipinda cha Mabuku kuti awasamalire kapena kwa mlembi wa mpingo wanu mukabwerako ku msonkhanowo.—Onani Utumiki Wathu wa Ufumu wa February 2005, tsa. 6.

◼ Kujambula Zithunzi: Ngati mukujambula zithunzi, musagwiritse ntchito fulashi msonkhano uli mkati.

◼ Foni za M’manja: Muyenera kuzitchera kuti zisalire n’kusokoneza

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena