‘Yendani mwa Chikhulupiriro, Osati mwa Zooneka ndi Maso’
Paulo ananena kuti Akhristu ali ngati asilikali abwino a Yesu ndipo ayenera kukonzekera mavuto osati zinthu zosangalatsa. (2 Tim. 2:3, 4, w13 7/15 tsamba 3-7) Iye ananena zimenezi mzinda wa Yerusalemu utatsala pang’ono kuzunguliridwa ndi asilikali komanso kuwonongedwa. Panopa, mapeto ali pafupi kwambiri choncho tiyenera kukhala ndi chikhulupiriro cholimba komanso kuganizira kwambiri ubwenzi za wathu ndi Yehova. (2 Akor. 4:18; 5:7) Mukamaonera vidiyo yakuti ‘Yendani mwa Chikhulupiriro, Osati mwa Zooneka ndi Maso,’ onani mavuto amene Nahamu ndi Abitali anakumana nawo chifukwa cha mtima wokonda chuma. Kenako yesani kuyankha mafunso awa.
(1) M’nthawi ya atumwi, kodi ‘chinthu chonyansa chowononga chimene chinaimirira m’malo oyera’ chinali chiyani, nanga Akhristu a ku Yerusalemu anayenera kuchita chiyani? (Mat. 24:15, 16, w13 7/15 tsamba 3-7) (2) N’chifukwa chiyani panafunika chikhulupiriro cholimba kuti Akhristu athawe mumzindawo? (3) Kodi iwo anafunika kulolera kusiya chiyani pothawa? (4) Kodi Nahamu ndi Abitali anachedwa chifukwa chiyani? (Mat. 24:17, 18) (5) Kodi Rakele anakumananso ndi vuto liti pochoka ku Yerusalemu? (Mat. 10:34-37; Maliko 10:29, 30) (6) Kodi Etani anasonyeza bwanji kuti ankakhulupirira kwambiri Yehova? (7) Kodi Akhristu anakumana ndi mavuto ati ku Pela? (8) Kodi Nahamu ndi Abitali anasonyeza bwanji kuti chikhulupiriro chawo chinayamba kufooka? (9) Kodi Yehova ankasamalira bwanji Akhristu ku Pela? (Mat. 6:33; 1 Tim. 6:6-8) (10) Kodi tingatsanzire bwanji Abulahamu ndi Sara pa nthawi yamapeto ino? (Aheb. 11:8-10) (11) N’chiyani chinachititsa kuti Nahamu ndi Abitali aganize zobwerera ku Yerusalemu, nanga n’chifukwa chiyani maganizo awowa anali olakwika? (Luka 21:21) (12) Kodi Nahamu ndi Abitali atabwerera ku Yerusalemu anapeza zinthu zili bwanji? (13) N’chifukwa chiyani tiyenera kulimbitsa chikhulupiriro chathu panopa mapeto asanafike?—Luka 17:31, 32; 21:34-36.
Munthu amene akuyenda mwa chikhulupiriro (1) sakayikira malangizo a Yehova, (2) amatsatira malangizowo, ndiponso (3) amaona kuti ubwenzi wake ndi Yehova ndi wofunika kwambiri kuposa chuma. Choncho tiyeni tonse tiziyenda mwa chikhulupiriro ndipo tisamakayikire zoti “dziko likupita limodzi ndi chilakolako chake, koma wochita chifuniro cha Mulungu adzakhala kosatha.”—1 Yoh. 2:17.