Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • be phunziro 44 tsamba 236-tsamba 239 ndime 5
  • Kugwiritsa Ntchito Mafunso Mwaluso

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kugwiritsa Ntchito Mafunso Mwaluso
  • Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Nkhani Yofanana
  • Kukulitsa Luso Lophunzitsa
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Kugwiritsa Ntchito Mafunso
    Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
  • Kuwonjezera Luso Lathu Mu Utumiki​—Muzigwiritsa Ntchito Mafunso Mwaluso
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
  • Tsanzirani Mphunzitsi Wamkulu
    Nsanja ya Olonda—2002
Onani Zambiri
Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
be phunziro 44 tsamba 236-tsamba 239 ndime 5

PHUNZIRO 44

Kugwiritsa Ntchito Mafunso Mwaluso

Kodi muyenera kuchita motani?

Gwiritsani ntchito mafunso m’njira yothandiza kukwaniritsa chimene mukufuna. Cholinga chanu chingakhale chakuti munthuyo ayankhe; kapena mungafune kungothandiza ena kuganiza. Kupita kwanu patsogolo m’mbali imeneyi kumadalira mtundu wa mafunso amene mumafunsa ndi kafunsidwe kake.

N’chifukwa chiyani kuli kofunikira?

Mafunso ogwira mtima amathandiza omvera kunena maganizo awo. Mayankho a mafunso osankhidwa bwino angathandize wokamba nkhani kuzindikira zinthu zina zofunika.

POPEZA mafunso amafuna mayankho—kaya m’mawu kapena a m’mtima—amathandiza omvera kulankhulapo. Mafunso angakuthandizeni kuyambitsa makambirano ndi kusangalala popatsana nzeru ndi ena. Monga wokamba nkhani komanso mphunzitsi, mungagwiritse ntchito mafunso kuti mukope chidwi, muthandize munthu wina kuganizira nkhaniyo, kapena kuti mutsindike zimene mukunena. Pamene mugwiritsa ntchito bwino mafunso, mumalimbikitsa ena kulingalira mozama m’malo mongomvera mwachisawawa. Khalani ndi cholinga. Funsani mafunso m’njira yothandiza kukwaniritsa cholingacho.

Mafunso Olimbikitsa Kukambirana. Pamene muli mu utumiki wa kumunda, funani mipata yolimbikitsira anthu kulankhula za kukhosi ngati akufuna kutero.

Mboni zambiri zimayambitsa makambirano osangalatsa mwa kungofunsa kuti, “Kodi munayamba mwaganizirapo . . . ?” Pamene apereka funso limene anthu ambiri amakonda kufunsa, nthaŵi zambiri amakhala ndi ulaliki wabwino kwambiri mu utumiki wa kumunda. Ngakhale funsolo litakhala loti munthuyo sanaliganizirepo, lingakopebe chidwi chake. Nkhani zambiri tingaziyambitse ndi mafunso ngati aŵa “Kodi muganiza bwanji . . . ?,” “Kodi mukuona bwanji . . . ?,” “Kodi mukukhulupirira . . . ?”

Pamene mlaliki Filipo anakumana ndi nduna ya ku Etiopiya imene inali kuŵerenga mokweza ulosi wa Yesaya, anangofunsa kuti: “Kodi muzindikira chimene muŵerenga?” (Mac. 8:30) Funsoli linam’patsa mpata Filipo kuti afotokoze zenizeni zokhudza Yesu Kristu. Pogwiritsa ntchito funso ngati limenelo, Mboni zambiri masiku ano zapeza anthu omwe anali kulakalakadi kumvetsa choonadi cha m’Baibulo.

Anthu ambiri mutawapatsa mpata woti alankhule za kukhosi kwawo, iwonso amamvetsera kwa inu. Mukapereka funso, mvetserani mwachidwi. M’malo mosuliza zimene munthu wayankha, mumvereni chifundo. Muyamikireni moona mtima. Nthaŵi ina, mlembi wina ‘atayankha mwanzeru,’ Yesu anam’yamikira ndi kunena kuti: “Suli kutali ndi Ufumu wa Mulungu.” (Marko 12:34) Ngakhale simukuvomereza maganizo a munthu wina, mungamuyamikire chifukwa chonena zimene akukhulupirira. Zimene wanenazo zingakuthandizeni kuzindikira maganizo ake amene muyenera kuwasamala pokambirana naye choonadi cha m’Baibulo.

Mafunso Oyambira Mfundo Zofunika Kwambiri. Pamene mukulankhula ku gulu kapena kukambirana ndi munthu wina, yesani kugwiritsa ntchito mafunso pofuna kufika pa mfundo zofunika kwambiri. Onetsetsani kuti mafunso anu akukhudza nkhani zimene omvera anu angafunedi kuzimva. Mungaperekenso mafunso odzutsa chidwi amene mayankho ake si apafupi. Ngati mupereka funso kenako n’kuima kaye pang’ono, omvera anu adzatchera khutu ndi chidwi chachikulu pofuna kumva yankho.

Nthaŵi ina, mneneri Mika anagwiritsa ntchito mafunso angapo. Atafunsa zimene Mulungu amafuna kwa alambiri ake, mneneriyo anaperekanso mafunso ena anayi, lililonse linali lotheka kuliyankha. Mafunso onsewo amapatsa chidwi oŵerenga chakuti amvetse yankho limene mneneriyo anamaliza nalo nkhaniyo. (Mika 6:6-8) Kodi inunso mungachite zofanana ndi zimenezi pamene mukuphunzitsa? Kayeseni.

Mafunso Othandiza Kuganizapo pa Nkhaniyo. Tingagwiritse ntchito mafunso pofuna kuthandiza ena kuti aone mfundo ya zimene tikunena. N’zimenenso Yehova anachita popereka chilengezo champhamvu kwa Israyeli, cholembedwa pa Malaki 1:2-10. Choyamba anawauza kuti: “Ndakukondani.” Iwo sanayamikire chikondi chimenecho, choncho anawafunsa kuti: “Esau si mkulu wake wa Yakobo kodi?” Ndiyeno Yehova anatchula chipasuko cha Edomu monga umboni wakuti Mulungu sanakonde mtunduwo chifukwa cha ntchito zawo zoipa. Kenako anapereka mafanizo ndi mafunso posonyeza kuti Israyeli sanayamikire chikondi chake. Mafunso ena anafunsidwa ngati kuti ofunsa anali ansembe osakhulupirikawo. Ena ndi mafunso amene Yehova anafunsa ansembewo. Kukambiranako kumakhudza mtima kwambiri; mfundo zake n’zosatsutsika; uthenga wake n’ngosaiŵalika.

Okamba nkhani ena amagwiritsa ntchito mafunso m’njira yaluso imeneyi. Ngakhale kuti iye sangayembekezere yankho la pakamwa, omverawo amayankha m’maganizo, ngati kuti akukambirana naye.

Pochititsa maphunziro a Baibulo, timagwiritsa ntchito njira yolimbikitsa wophunzira kulankhulapo. Koma zimakhala zopindulitsa kwambiri ngati wophunzirayo sakungobwereza mayankho olembedwawo. Mwa mawu aubwenzi, perekani mafunso owonjezera othandiza wophunzira kulingalira. Mukafika pa mfundo zazikulu, mulimbikitseni kuyankha mochokera m’Baibulo. Mungafunsenso kuti: “Kodi mfundoyi ikugwirizana motani ndi nkhani imene tikukambirana? N’chifukwa chiyani ili yofunika? Kodi imakhudza motani miyoyo yathu?” Njira imeneyi imagwira mtima kwambiri kuposa kulongosola zimene mumakhulupirira kapena kuchita kum’fotokozera zambiri. Mwa njira imeneyinso, mudzathandiza wophunzirayo kugwiritsa ntchito ‘luntha lake la kulingalira,’ polambira Mulungu.—Aroma 12:1, NW.

Ngati wophunzira sakumvetsa mfundo inayake, lezani mtima. Mwina akuyesa kuyerekeza zimene mukunena ndi zimene wakhala akukhulupirira kwa zaka zambiri. Kufotokoza nkhaniyo m’njira yosiyanako kungakhale kothandiza. Komabe, nthaŵi zina n’kofunika kukambirana nkhani m’njira yosavuta. Gwiritsani ntchito Malemba kaŵirikaŵiri. Gwiritsaninso ntchito mafanizo. Limodzi ndi zimenezi, gwiritsaninso ntchito mafunso osavuta olimbikitsa munthu kuganizira umboni umene mwapereka.

Mafunso Olimbikitsa Munthu Kulankhula za Kukhosi. Anthu akamayankha mafunso, si nthaŵi zonse pamene amayankha zochokeradi pansi pa mtima. Nthaŵi zina amangoyankha zimene akuganiza kuti n’zimene mukufuna. Choncho kuzindikira n’kofunika. (Miy. 20:5) Monga mmene Yesu anachitira, mungafunse kuti: ‘Kodi mukukhulupirira kuti zimenezi n’zoona?’—Yoh. 11:26.

Pamene ophunzira a Yesu ambiri anakhumudwa ndi zimene iye ananena ndi kumusiya, Yesu anafunsa atumwi ake kunena zimene anali kuganiza. Iye anati: “Nanga inunso mufuna kuchoka?” Polankhuliranso anzake, Petro anati: “Ambuye, tidzamuka kwa yani? Inu muli nawo mawu a moyo wosatha. Ndipo ife tikhulupirira, ndipo tidziŵa kuti Inu ndinu Woyera wa Mulungu.” (Yoh. 6:67-69) Nthaŵi inayake, Yesu anafunsa ophunzira ake kuti: ‘Anthu anena kuti Mwana wa munthu ndiye yani?’ Ndiyeno anawonjezera funso lina lowapempha kuti alankhule za kukhosi kwawo. Iye anati: ‘Koma inu mutani kuti Ine ndine yani?’ Poyankha Petro anati: “Inu ndinu Kristu, Mwana wa Mulungu wamoyo.”—Mat. 16:13-16.

Pochititsa phunziro la Baibulo, njira imeneyi ingakhale yothandiza pokambirana nkhani zina. Mungafunse kuti: “Kodi anzanu kusukulu (kapena kuntchito) amaiona bwanji nkhaniyi?” Ndiyeno mungafunsenso kuti: “Nanga inuyo mukuganiza bwanji?” Monga mphunzitsi, mukadziŵa maganizo enieni a munthu, mumatha kum’thandiza bwino kwambiri.

Mafunso Othandiza Kutsindika Mfundo. Mafunso amathandizanso kutsindika mfundo. Mtumwi Paulo anachita zimenezi, monga tikuonera pa Aroma 8:31, 32 pamene anati: “Ngati Mulungu ali ndi ife, adzatikaniza ndani? Iye amene sanatimana Mwana wake wa iye yekha, koma anam’pereka chifukwa cha ife tonse, adzalekeranji kutipatsanso ife zinthu zonse kwaulere pamodzi ndi iye?” Onani kuti, funso lililonse likupitiriza mfundo imene yangotchulidwa kumene.

Mneneri Yesaya atalemba chiweruzo cha Yehova pa mfumu ya Babulo, anaonetsa kutsimikiza mtima kwake powonjezera mawu akuti: “Yehova wa makamu wapanga uphungu, ndani adzauleketsa? Ndi dzanja lake latambasulidwa, ndani adzalibweza?” (Yes. 14:27) Mmene mafunsoŵa akuwafunsira, akuonetseratu kuti palibe angatsutse mfundo zotchulidwazo. Si ofunanso mayankho ayi.

Mafunso Amavumbulanso Malingaliro Olakwika. Mafunso osankhidwa bwino amakhalanso chida champhamvu chovumbulira kalingaliridwe kolakwika. Yesu asanachiritse munthu wina wodwala, anayamba wafunsa Afarisi ndi akatswiri ena a Chilamulo kuti “Kodi n’kuloledwa tsiku la Sabata kuchiritsa, kapena iyayi?” Atam’chiritsa munthu uja, anaperekanso funso lina lakuti: “Ndani wa inu bulu wake kapena ng’ombe yake itagwa m’chitsime, ndipo sadzaitulutsa pomwepo tsiku la Sabata kodi?” (Luka 14:1-6) Palibe anayankha, ndipo Yesu sanayembekezere yankho. Mafunsowo anavumbula kalingaliridwe kawo kolakwika.

Nthaŵi zina, ngakhale Akristu oona akhoza kulingalira molakwa. Ena m’Korinto wa m’zaka 100 zoyambirira, anali kutengera abale awo kukhoti kuti akaweruzidwe milandu imene akanatha kukambirana okhaokha ndi kuithetsa. Kodi mtumwi Paulo anawathandiza motani pankhaniyi? Iye anapereka mafunso angapo powathandiza kusintha kalingaliridwe kawo.—1 Akor. 6:1-8.

Mwa kuyesetsa, inunso mungadziŵe kugwiritsa ntchito mafunso mwaluso. Komabe, kumbukirani kusonyeza ulemu, makamaka polankhula kwa anthu achikulire, anthu amene simukuwadziŵa, komanso anthu a maudindo. Perekani mafunso kuti muphunzitse choonadi cha m’Baibulo m’njira yosangalatsa.

MMENE MUNGACHITIRE ZIMENEZO

  • Kuti mulimbikitse kukambiranako, perekani mafunso pankhani zofunikadi kwa munthu winayo.

  • Musanatchule mfundo yofunika, yesani kupereka funso lopatsa chidwi ena kuti amve.

  • Perekani mafunso pothandiza anthu kuona maziko a zimene mukunena, nzeru yake ya mfundo zanu, ndi mmene zingawathandizire pa miyoyo yawo.

  • Perekani mafunso popempha wophunzirayo kunena mfundo zimene mwaphunzira ndi maganizo ake pa mfundozo.

ZOCHITA: (1) Poganizira malo amene mumalalikirako, konzekerani mafunso angapo amene mungagwiritse ntchito poyambitsa makambirano othandiza kwa anthuwo. (2) Ŵerengani Aroma chaputala 3, ndi kuona mmene Paulo anafunsira mafunso pomveketsa mfundo ya mmene Ayuda ndi Akunja omwe analili pamaso pa Mulungu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena