Nyimbo 150
Timadzipereka
Yehovatu watipatsa
zomwe timafunikira.
Kuti tizisangalala
pomwe tikum’tumikira.
(KOLASI)
Timadzipereka,
pom’tumikira.
Ndipo kulikonse tipita,
mofunitsitsa.
Padzikoli pali ntchito.
Kosowa tidzapitako.
Tikatero tisonyeza.
kuti ena timakonda.
(KOLASI)
Timadzipereka,
pom’tumikira.
Ndipo kulikonse tipita,
mofunitsitsa.
Komwe tili kuli ntchito,
inde, zofunika luso.
Zinenero taphunzira.
Ena tikulalikira.
(KOLASI)
Timadzipereka,
pom’tumikira.
Ndipo kulikonse tipita,
mofunitsitsa.
(Onaninso Yoh. 4:35; Mac. 2:8; Aroma 10:14.)