MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Muziwaphunzitsa Kuti Azitumikira Yehova Mosalekeza
Nthawi zambiri, ofalitsa atsopano amene aphunzitsidwa kuyambira pachiyambi kuti azigwira nawo ntchito yolalikira mwakhama, amadzakhala ofalitsa aluso. (Miy. 22:6; Afil. 3:16) Malangizo otsatirawa akusonyeza mmene tingathandizire wophunzira kuti azigwira bwino ntchito yolalikira:
Wophunzira wanu akavomerezedwa kukhala wofalitsa, yambani nthawi yomweyo kumuphunzitsa. (km 8/15 1) Muthandizeni kuti aziona kufunika kogwira ntchito yolalikira mlungu uliwonse. (Afil. 1:10) Muzilankhula zabwino za anthu a m’gawo lanu. (Afil. 4:8) Mulimbikitseni kuti azilowa mu utumiki ndi woyang’anira kagulu komanso ofalitsa ena n’cholinga choti apeze luso.—Miy. 1:5; km 10/12 6 ¶3
Wophunzira wanu akabatizidwa, musasiye kumulimbikitsa komanso kumuthandiza mmene angachitire zinthu mu utumiki, makamaka ngati simunamalize kuphunzira naye buku lakuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani.’—km 12/13 7
Mukayenda limodzi ndi wofalitsa watsopano mu utumiki, muzigwiritsa ntchito ulaliki wosavuta. Mukaona mmene akulalikirira, muzimuyamikira. Kenako mufotokozereni mfundo zina zimene zingamuthandize kuti azilalikira mogwira mtima.—km 5/10 7