CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MATEYU 6-7
Pitirizani Kufunafuna Ufumu Choyamba
M’pemphero lachitsanzo, Yesu anasonyeza kuti zinthu zokhudza kukwaniritsidwa kwa cholinga cha Yehova komanso Ufumu wa Mulungu ndi zimene ziyenera kukhala zofunika kwambiri pamoyo wathu.
Dzina la Mulungu
Ufumu wa Mulungu
Chifuniro cha Mulungu
Chakudya cha tsiku ndi tsiku
Kukhululukidwa machimo
Kupulumutsidwa pa mayesero
Zinthu zina zokhudza Ufumu zimene ndiyenera kupempherera:
Ntchito yolalikira ipite patsogolo
Mzimu woyera uthandize anthu amene akuzunzidwa
Mulungu adalitse ntchito yomanga kapena ntchito yolalikira imene yakonzedwa mwapadera
Mulungu azipereka nzeru komanso mphamvu kwa anthu amene akutsogolera m’gulu lake
Zina