Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu
MAY 6-12
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 AKORINTO 4-6
“Sitikubwerera M’mbuyo”
it-1 724-725
Kupirira
N’zofunikanso kwambiri kuti tisamaiwale chiyembekezo chathu chodzakhala ndi moyo wosatha popanda kuchimwa. Chiyembekezochi ndi chodalirika ngakhale anthu amene amatizunza atatipha. (Aroma 5:4, 5; 1 Ates. 1:3; Chiv. 2:10) Tikamaganizira kwambiri madalitso amene tikuyembekezera m’tsogolomu, mavuto amene tikukumana nawo panopa samaoneka ngati kanthu. (Aroma 8:18-25) Ngakhale mayesero atakhala aakulu bwanji, timawaona kuti ndi ‘akanthawi komanso opepuka’ tikawayerekeza ndi moyo wosatha. (2 Akor. 4:16-18) Kuzindikira mfundo imeneyi, kungatithandize kuti tisamagonje tikamayesedwa kuti tichite zimene Yehova Mulungu amadana nazo.
MAY 13-19
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 AKORINTO 7-10
“Utumiki Wothandiza Anthu pa Nthawi ya Mavuto”
“Mulungu Amakonda Munthu Wopereka Mokondwera”
Choyamba, Paulo anauza Akorinto za anthu a ku Makedoniya omwe anasonyeza chitsanzo chabwino pa nkhani yothandiza ena pa nthawi yamavuto. Ponena za anthu a ku Makedoniya, Paulo anafotokoza kuti: “Pamene iwo anali kuyesedwa kwambiri chifukwa cha mavuto, anali achimwemwe kwambiri ndiponso anasonyeza kuwolowa manja kwakukulu, ndipo anachita zimenezi ngakhale kuti anali pa umphawi wadzaoneni.” Anthu a ku Makedoniya sanachite kukakamizidwa kuti apereke. Paulo ananena kuti iwo anachita kuchonderera kuti “tiwapatse mwayi wopereka nawo mphatso zachifundo.” N’zochititsa chidwi kuti anthu a ku Makedoniya anasonyeza mtima woolowa manjawu chonsecho nawonso anali “pa umphawi wadzaoneni.”—2 Akorinto 8:2-4.
Kufufuza Mfundo Zothandiza
Kodi Kudzitamandira N’kulakwa?
M’Malemba Achigiriki, mawu akuti kau·khaʹo·mai, omwe anawamasulira kuti “kunyada, kudzitamandira kapena kudzikuza,” angasonyeze mtima woipa kapena wabwino. Mwachitsanzo, Paulo ananena kuti tikhoza “tikondwere [kapena kuti tidzitamandire] chifukwa cha chiyembekezo cha ulemerero wa Mulungu.” Iye ananenanso kuti: “Amene akudzitamandira, adzitamande mwa Yehova.” (Aroma 5:2; 2 Akorinto 10:17) Zimenezi zikutanthauza kunyadira kuti Yehova ndi Mulungu wathu zomwe zingatichititse kuti tizimulemekeza kwambiri.
MAY 20-26
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 AKORINTO 11-13
“Paulo Anali ndi ‘Munga M’thupi’”
Kufufuza Mfundo Zothandiza
it-2 177
Kupsompsonana
“Kupsompsonana Kwaubale.” Mawu akuti “kupsompsonana kwaubale” (Aroma 16:16; 1 Akor. 16:20; 2 Akor. 13:12; 1 Ates. 5:26) kapena kuti ‘kupsompsonana mwachikondi’ (1 Pet. 5:14) anali odziwika kwa Akhristu oyambirira. Zikuoneka kuti anthu amene ankapsompsonana mwamtundu umenewu anali abale kapena alongo okhaokha. Zimene Akhristu oyambirirawa ankachita ndi zofanana ndi zimene Aheberi ankachita akamapatsana moni. Malemba sanena zambiri zokhudza “kupsompsonana kwaubale” komanso ‘kupsompsonana mwachikondi.’ Komabe, zimenezi zikusonyeza kuti Akhristu oyambirirawa ankakondana komanso kugwirizana kwambiri.—Yoh. 13:34, 35.
MAY 27–JUNE 2
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | AGALATIYA 1-3
“Ndinamutsutsa Pamasom’pamaso”
Kufufuza Mfundo Zothandiza
it-1 880
Kalata Yopita kwa Agalatiya
Mawu omwe Paulo ananena akuti “Agalatiya opusa inu,” sakusonyeza kuti mtumwiyu ankanena za anthu ena okha omwe anachokera m’dera lakumpoto omwe ankadziwika kuti ndi Agalatiya. (Agal. 3:1) Komabe iye ankadzudzula anthu ena a mumpingomo omwe ankatengera zochita za Ayuda ena. Ayudawo ankaona kuti Mulungu amaona munthu kukhala wolungama chifukwa cha Chilamulo cha Mose osati chifukwa cha “chikhulupiriro” malinga ndi pangano latsopano. (2:15–3:14; 4:9, 10) Zikuoneka kuti “mipingo ya ku Galatiya” (1:2) yomwe Paulo ankailembera kalatayi, inapangidwa ndi Ayuda ndi ena omwe sanali Ayuda. Pa anthu omwe sanali Ayudawo, panali ena omwe anatembenukira ku Chiyuda ndipo anali odulidwa komanso ena osadulidwa. (Mac. 13:14, 43; 16:1; Agal. 5:2) Onsewa ankangotchulidwa kuti Agalatiya potengera dzina la dera limene ankakhala. Mawu amene Paulo anagwiritsa ntchito polemba kalatayi, amasonyeza kuti ankalankhula ndi Akhristu omwe ankawadziwa bwino omwe ankakhala m’chigawo chakum’mwera cha Ufumu wa Roma. Iye sankalankhula ndi anthu achilendo a m’chigawo chakumpoto, komwe pa nthawiyi anali asanafikeko.