Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g99 7/8 tsamba 20-25
  • Mulungu Wakhala Mthandizi Wathu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mulungu Wakhala Mthandizi Wathu
  • Galamukani!—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuleredwa ndi Moyo Wopembedza
  • Kuphunzira ndi Kugwiritsa Ntchito Choonadi
  • Kugwiritsa Ntchito Nzeru Polalikira
  • Nthaŵi ya Chiyeso Chachikulu
  • Kukhala kwa M’misasa
  • Mmene Tinkalalikirira
  • Kumasulidwa, ndi Kubwerera ku Maputo
  • Kuchita Maudindo Onse Molingana
  • Madalitso Ochokera kwa Mulungu Apitirira
  • Kutumikira Yehova M’nyengo Yabwino ndi m’Nyengo Yovuta
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Yehova Amatisamalira Nthaŵi zonse
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Kusefukira kwa Madzi ku Mozambique—Momwe Akristu Anasamalira Anthu Ovutikawo
    Galamukani!—2001
Galamukani!—1999
g99 7/8 tsamba 20-25

Mulungu Wakhala Mthandizi Wathu

YOSIMBIDWA NDI FRANCISCO COANA

“Ngati muti mukane kumvera zimene a boma akukuuzani, muphedwa!” mkulu wanga anandichenjeza motero.

“Zitatero zingakhaleko bwino kusiyana ndi kuzunzika chonchi,” ndinayankha motero.

KUMENEKO kunali kukambiirana kwapakati pa ine ndi mkulu wanga mu September 1975. Iye anabwera kudzandipatsira chakudya pamene ndinali m’ndende ku Maputo (panthaŵiyo kumadziŵika ndi dzina lakuti Lourenço Marques), kum’mwera kwa Mozambique. Tinalipo anthu opitirira 180, amene tinatsekeredwa m’chipinda chimodzi chandende, ndipo ambiri tinali a Mboni za Yehova. Mkulu wangayo anakwiya nane kwabasi kotero kuti sanasiye n’komwe chakudya chimene anabweretsacho!

Kuti mumvetse chifukwa chimene tinakwiyitsana chonchi, ndibwerera m’mbuyo kuti ndikulongosolereni chifukwa chimene ndinapezekera kundende.

Kuleredwa ndi Moyo Wopembedza

Ndinabadwa mu 1955 m’banja la chipembedzo cha CCAP m’mudzi wa Calanga m’Boma la Manica. Kumeneku sikutali ndi mzinda waukulu wa Maputo. Ngakhale kuti atate wanga sanali kupita kutchalitchi, mayi ankapita, ndipo ankatenga ana awo asanufe popita kutchalitchi pa Lamlungu. Tidakali ana iwo anatiphunzitsa Pemphero la Ambuye, ndipo kaŵirikaŵiri ine ndinkalibwerezabwereza. (Mateyu 6:9-12) Ndili kamnyamata kachichepere, ndinkawafunsa amayi anga mafunso monga ngati “Kodi n’chifukwa chiyani timafa?” ndi kuti, “Kodi anthu azifa nthaŵi zonse?”

Mayi anandiuza kuti imfa ndi chifuno cha Mulungu—ndi kuti ochita zoipa adzapita kuhelo ndipo ochita zabwino adzapita kumwamba. Ngakhale kuti sindinanene chilichonse, yankho lawo linandikhumudwitsa. Kuopsa ndi kuwawa kwa imfa kunkandisokoneza maganizo, makamaka kuyambira nthaŵi imene atate anga anamwalira ine ndili ndi zaka khumi. Kenaka chikhumbo changa chofuna kudziŵa mkhalidwe wa anthu akufa ndi kudziŵa ngati panali chiyembekezo chilichonse chokhudza iwo, chinakula.

Kuphunzira ndi Kugwiritsa Ntchito Choonadi

Atate wanga atangomwalira, mmodzi wa aphunzitsi kusukulu kwathu, potiphunzitsa, anali kugwiritsa ntchito buku lakuti Kucokera Ku Paradaiso Wotayika Kunka Ku Paradaiso Wopezedwanso. Bukulo, lofalitsidwa ndi Watch Tower Bible and Tract Society, linali m’Chizulu, chiyankhulidwe cha ku South Africa. Mphunzitsiyo anandibwereka bukulo ndipo ngakhale kuti sindinkachidziŵa bwinobwino Chizulu, ndinasangalatsidwa nazo zimene ndinaphunzira poona Malemba osonyezedwamo.

Pamene ndinali ndi zaka 16 mkulu wanga amene anali kutipezera chakudya pakhomopo anatengedwa kuti akayambe ntchito ya usilikali. Apa m’pamene ine ndinayamba ntchito pa kampani ina ku Maputo yopanga mafuta onunkhiritsa thupi, ndipo ndinkapitanso kusukulu usiku. Kuntchito, panthaŵi yopuma masana, ndinkaona Teófilo Chiulele, wa Mboni za Yehova—nthaŵi zonse ankaŵerenga Baibulo. Pamene Teófilo anaona chidwi changa, anayamba kundiyankhulitsa.

Popita masiku, wa Mboni wina Luis Bila, anayamba kuphunzira nane Baibulo. Ndinaziziritsidwa mtima nditaphunzira kuti akufa sadziŵa kanthu kalikonse ndi kuti iwo ali ndi chiyembekezo chodzaukitsidwa ndi kukhalanso ndi moyo. (Mlaliki 9:5, 10; Yohane 5:28, 29) Nthaŵi yomweyo ndinawalembera kalata amayi ndikuwauza mayankho ochokera m’Baibulo a mafunso amene ndinawafunsa. Iwo anasangalala kwambiri podziŵa kuti tsopano ndapeza mayankho otsimikizirika.

Posangalala ndi zimene ndinali kuphunzirazi, ndinakonzeka kuti ndiuzeko anthu ena zimenezi. Anandilola kukamba nkhani za Baibulo kusukulu koma osati kutchalitchi. Posapita nthaŵi sankandilandiranso kutchalitchi. Ngakhale am’banja mwathu anayamba kundisautsa, ngakhale kuti mayi anali kusangalala ndi chikhulupiriro changa chatsopanocho. Mkulu wanga anandikwapula kwambiri. Ataona kuti zimenezi sizikundisintha maganizo, abale anga anayamba kundiseka, makamaka akandiona ndikupemphera nthaŵi yakudya. Choncho ndinkapemphereratu m’bafa ndisanapite pathebulo kukadya chakudya. Ndinkaona kuti “Mulungu ndiye [anali] mthandizi wanga.”—Salmo 54:4.

Kenako Luis analetsedwa kubwera kunyumba kwathu kudzaphunzira Baibulo ndi ine. Ndiyeno tinayamba kuphunzirira kunyumba kwake. Pamene ndinayamba kupita kumisonkhano ya mpingo ndi kulalikira pamodzi ndi ena, pobwerera kunyumba ndinkapeza kuti anditsekera panja. Choncho, ndinkagona kunyumba kwa Mboni zosiyanasiyana.

M’kupita kwa nthaŵi pa May 13, 1973, ndinasonyeza kudzipatulira kwanga kwa Yehova Mulungu mwa ubatizo wa m’madzi. Panthaŵi imeneyo, dziko la Mozambique linali pansi pa utsamunda wa Apwitikizi, umene unali kuletsa Mboni za Yehova ku Portugal ndi mayiko onse amene anali pansi pake. Pa October 1, 1974, ndinakhala mpainiya, monga momwe Mboni za Yehova zimatchulira alaliki a nthaŵi zonse. Chifukwa chakuti cholinga changa chinali chodzakhala mmishonale, ndinayamba kuphunzira Chingelezi kotero kuti ndidzathe kuyenera kupita ku Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower, ku United States kuti ndikaphunzire za umishonale.

Kugwiritsa Ntchito Nzeru Polalikira

M’nthaŵi za chiletso zimenezo, polisi ya Apwitikizizi achitaganya, yotchedwa PIDE, inamanga Mboni zambiri chifukwa cha kulalikira. Motero kuti asadziŵe, timagwiritsa ntchito nzeru. Mwachitsanzo, timati tikayankhula pa nyumba ina timachoka n’kupita kunyumba inanso ya kudera lina. Chinanso, timanyamuka anthu aŵiri kupita pamalo opumulirapo anthu mumzindamo panthaŵi ya nkhomaliro kapena chakumadzulo. Kenaka, mmodzi wa ife amakhala pansi moyandikana ndi munthu wina, n’kuyamba kuona nyuzi, ndi kunena mawu monga ngati aŵa: “Mayo ine, taonani kuchuluka kwa anthu amene afa! Koma kodi mukudziŵa kuti pansi pa ulamuliro wa Mulungu zimenezi sizidzachitikanso?”

Ndiye nkhani imayambika mpaka amene anali kuŵerenga nyuziyo ankafunsa kuti amutsimikizire kuchokera m’Baibulo, zimene wina uja wanena. Kenaka timapangana kuti tipezane maŵa lake kuti tidzapitirize nkhaniyo. Mwanjira imeneyi nthaŵi zambiri tinkatha kuloŵetsa munthu amene wakhala moyandikana nafe m’nkhani zathu zokhudza maulosi a Baibulo, ndipo tinayambitsa maphunziro ambiri a Baibulo. Tinkathokoza Mulungu chifukwa chotithandiza.

Nthaŵi ya Chiyeso Chachikulu

Pa April 25, 1974, ulamuliro wankhanza ku Portugal unatha, ndipo panali kusintha kwa ndale kosiyanasiyana m’mayiko olamulidwa ndi Portugal. Ku Mozambique akaidi a ndale, komanso Mboni zimene zinamangidwa chifukwa chokana kuloŵa nawo m’ndale, zinamasulidwa. Koma kenaka, pa June 25, 1975 patangotha miyezi 14 yokha, dziko la Mozambique linalengeza kuti tsopano lalandira ufulu kuchokamo m’manja mwa Portugal. Patangotha masiku angapo, kuzunzanso Mboni kunayamba. Anthu okhala m’dera limodzi anali kupanga timagulu kuti azimanga Mboni zonse zimene angazipeze. Amatinena kuti tinali “azondi osiyidwa ndi Utsamunda Wachipwitikizi.”

Mu September ndinakakamizidwa kuti ndikapezeke nawo pa msonkhano wa kagulu kena kopangidwa ndi anthu adera limodzi. Nditakafika, ndinapeza kuti onse amene ndinkaphunzira nawo Baibulo anali komweko. Anatilamula kuti tinene mofuula mawu andale otamanda chipani chimene chinkalamulira. Titakana mwaulemu, anatitengera kundende ndi kutitsekera m’chipinda chimene ndatchula pamayambiriro paja, chimene tinalimo anthu ambirimbiri.

M’chipindacho tinadzadzana kwabasi kotero kuti timalephera n’kuyenda komwe. Kuti anthu ochepa chabe apeze kampata pansi kuti agonepo, ndiye kuti ena amayenera kukhala pansi kapena kuimirira. Panali chimbudzi chimodzi chokha, ndipo nthaŵi zambiri chimakhala chodzaza. Ndipo chimasefukira, ndiye sikununkha kwake. Chakudya chathu chinali spagheti wodzaza mafuta, minga za nsomba ndi ntchentche zikuluzikulu ndipo timayenera kudya zimenezi osasamba m’manja. Tinalipo anthu opitirira 180 amene tinapirira zoopsa zimenezi kwa masiku okwanira 19. Kenaka anatisamutsira kumalo ena kumene kunali Mboni Yehova zokha, kuphatikizapo amuna, akazi, ndi ana. Miyezi ingapo yotsatirapo, ana ambiri anafa chifukwa cha mikhalidwe yoipitsitsa ya kundendeko.

Mpaka kenaka, boma linalingalira kuti lithamangitsire Mbonizo ku Carico, dera lakutali chakumpoto. Cholinga chawo chinali chakuti atilekanitse ndi anthu ena. Panthaŵi imeneyo n’kuti ku Mozambique kuli Mboni 7,000, zambiri zinali zobatizidwa mu 1974 ndi 1975. Pozindikira kuti tidzafuna mabuku ophunzirira Baibulo panthaŵi yotipatula kwa tokha imeneyi, ndinapempha kuti ndibwerere kunyumba kuti ndikatenge zakudya ndi zinthu zina kaamba ka ulendowo. Ndinachotsa zakudya m’makatoni ena ndipo pansi pake ndinaikapo mabuku onena za Baibulo. Ndinatha kuchita zimenezo wapolisi amene anandiperekeza osaona. Nthaŵi ngati zimenezi, sitinali kuopa ayi. Timadalira Mulungu kuti atithandize.—Ahebri 13:6.

Kukhala kwa M’misasa

Tinafika ku Carico mu January 1976 ndipo tinapeza a Mboni ambiri ochokera ku dziko lochita nalo malire la Malaŵi akukhala m’misasa imene anamanga. Kuchokera 1972 mpaka 1975, anthu opitirira 30,000, kuphatikizapo ana, anathaŵa ku Malaŵi kumene anali kuzunzidwa koopsa chifukwa cha chipembedzo. Anawalola kuloŵa chakumpoto kwa Mozambique monga anthu othawa kwawo. Ndipo pamene ife tinafika, iwo anatisunga m’nyumba zawo ndipo anatigawirako chakudya chochepa chimene anali nacho.

Chifukwa chakuti ambirife sitinkadziŵa kumanga nyumba, abale athu a ku Malaŵi anatisonyeza mmene tingamangire nyumba zathu poumba njerwa ndi kuzigwiritsa ntchito pamodzi ndi zomera zina zamthengo. Anatisonyezanso mmene tingalimire zakudya ndi kuchita zinthu zina kuti tikhale bwino. Motero ine ndinaphunzira ukalipentala, ulimi, ndi kusoka. Maluso amene tinaphunzirawa ambirife anatithandiza kwambiri titabwereranso ku mizinda imene tinachokera.

Chinthu chimene tinkada nacho nkhaŵa kwambiri chinali uzimu wathu, ndipo kunena zoona sitimasoŵa chakudya chauzimu. Kodi zimenezi zimatheka bwanji? Monga mmene ndanenera kale, pamene timathamangitsidwa ambiri a ife tinagwiritsa ntchito nzeru, kutenga mabuku onena za Baibulo ndi zinthu zina. Ndiponso, makope ang’onoang’ono a Nsanja ya Olonda ankasindikizidwa ndi Mboni za Yehova ku South Africa. Zimenezi zinachititsa kuti kukhale kosavuta kuwabweretsa m’misasa.

Pa December 1, 1978, ukwati woyamba m’misasa unaloledwa kuchitika, pambuyo pa mapempho ambirimbiri. Tsiku limenelo ndinakwatira Alita Chilaule, amene atate wake anali mmodzi wa anthu oyamba kubatizidwa ku Maputo mu 1958. Pamene ana athu Dorcas ndi Samuel anabadwa, tinawaphunzitsa kukonda Yehova, ndipo tinkapita nawo mokhazikika kumisonkhano yachikristu. Kenaka tinakhala ndi mwana wina amene timamutcha kuti Jaimito.

Mmene Tinkalalikirira

Mbonizo zinalolezedwa kumachoka pa misasayo ndi kumakagulitsa zinthu, komanso zakudya zimene zinkalima. Ambirife timagwiritsa ntchito mwayi umenewu kukalalikira. Ine ndinakwezera dala mtengo wa mchere umene ndinkagulitsa kuti pasapezeke wougula. Komabe, anthu angapo amene ndinawapeza anamvetsera uthenga wa Ufumu, ndipo ndinayambitsa maphunziro a Baibulo angapo.

Mmodzi wa ophunzira Baibulo anga anayankhula ndi mkulu wa kampani inayake pa tauni ina yapafupi yotchedwa Milange ndipo iye anachita chidwi ndi Baibulo. Atandidziŵitsa zimenezi, ndinamulembera kalata mkulu wa kampaniyo. Iye anayankha pondiuza kuti ndidzapite kunyumba kwake. Motero ndinatenga mobisa mabuku a Baibulo ndi kunyamuka, koma oona amangoti ndikukamugulitsa mipando imene ndinam’khomera.

Nditakafika, ndinapeza kuti asilikali akulondera nyumbayo; ndipo ndinachita mantha. Komabe, munthuyo anatuluka ndi kuwauza asilikaliwo kuti sakufuna aliyense kumusokoneza. Tinayamba phunziro lathu la Baibulo 55 koloko madzulo, ndipo anasonyeza chidwi chachikulu mwakuti tinakhala mpaka 5 koloko ya m’maŵa wa tsiku lotsatira! Kenaka, anafuna kuti azilandira mabuku athu kuchokera ku Portugal, chifukwa chakuti panalibe lamulo lililonse lokhudza makalata limene linkamukhudza iye. Ankati akalandira amandipatsa mabukuwo, ndipo ine ndimawatenga kupita nawo ku misasa.

N’zoona kuti enafe tinawopsezedwa ndiponso tinamangidwa nthawi zingapo chifukwa cha kulalikira. Koma, anthu ambiri akamamvetsera uthenga wa Ufumu, tinkakhala ndi chidaliro chakuti Mulungu akutithandiza, monga mmene anathandiziranso Akristu a zaka za zana loyamba.—Machitidwe, machaputala 3-5.

Kumasulidwa, ndi Kubwerera ku Maputo

Mu September 1985, pambuyo pa kupemphera kaamba ka chitsogozo, tinaganiza kuti tonse tichoke m’misasa. Ngakhale kuti ena anatsalira ku misasa ya Carico ndi kukhala olekanitsidwa ndi Mboni za Yehova zina zonse kwa zaka zisanu ndi ziŵiri zotsatirapo, ena anathaŵira m’Malaŵi ndi m’Zambia. Mkazi wanga ndi ine tinaganiza kuti pamodzi ndi ana athu tipite ku tauni imene inali chapafupi yotchedwa Milange. Kumeneko ndinapeza ntchito ndi malo okhala, ndipo tinapitirizabe utumiki wathu. Chaka chotsatira tinabwerera ku Maputo.

Poyamba, tinkakhala ndi achibale. Ntchito inali yovuta kupeza, koma m’kupita kwa nthaŵi ndinaipeza. Alita ankagulitsa mtedza wokazinga kuti awonjezere pa tindalama tochepa timene timapeza. Chifukwa chakuti tsopano ndinali kudziŵa bwinoko chingerezi, ndinafunsira ntchito ku ofesi ya kazembe wa Britain. Ndinayesedwa ndipo ndinakhoza mayeso kenaka anandilemba ntchito yolandira malipiro owirikiza nthaŵi 20 kuposa zimene ndinkapeza! Ndinaona kuti Yehova wandithandizadi ndipo ndinam’thokoza mwapemphero.

Kuchita Maudindo Onse Molingana

Potsirizira pake, pa February 11, 1991, boma la Mozambique linavomereza Mboni za Yehova mwalamulo. Limeneli ndi tsiku limene ife tidzalikumbukira mpaka kalekale! Chaka chotsatira anandiitana kuti ndikatumikire m’komiti yoyang’anira ntchito yolalikira ya Mboni za Yehova mu Mozambique. Panthaŵi imeneyi, n’kuti ana athu ali ndi zaka wina 12, wina 9, ndi winanso 6. Ndinapemphera usiku wonse kwa Yehova kuti andipatse nzeru zoti zindithandize kusankha njira imene idzandipangitsa kusamalira bwino maudindo onse aŵiri, wa banja komanso wa gulu.

Tinapeza ngolo ya galimoto, imene tinayamba kugwiritsa ntchito pochita bizinesi mogwirizana ndi ena. Tinalemba ntchito apainiya angapo kuti azipanga ndi kugulitsa masikono, ndipo malondawo ankayenda bwino. Motero ndinapeza nthaŵi yokwanira kuti ndisamalire utumiki wanga m’gululi. Tinali kufunanso nyumba, chifukwa chakuti sitikanakwanitsa kulipira ndalama za nyumba imene tinkakhala. Motero ndinalemba kalata kubomayolongosola vuto la banja lathu la nyumba. Mosachedwa tinavomerezedwa kuti tingathe kupatsidwa nyumba. Nkhani imeneyi inatchuka ndi kufalitsidwa kwambiri, chifukwa chakuti ine ndinali munthu woyamba wa ku Mozambique kugula nyumba kuchokera ku boma.

Alita ndi ine tadalitsidwa ndi ana amene akhala omvera malangizo athu auzimu. (Deuteronomo 6:6-9) Ndi chizoloŵezi chathu kukambirana lemba la Baibulo la tsiku lililonse nthaŵi ya 5:40 m’maŵa, pambuyo pake timaŵerenga Baibulo pamodzi. Chifukwa chakuti ana athu amayenera kupita msanga kusukulu, anazoloŵera kudzuka m’maŵa. Lachisanu nthaŵi ya 6 koloko madzulo, timachita phunziro lathu labanja, ndipo nthaŵi imeneyi ana athu amakambirana nafe nkhani za m’Baibulo zimene azifufuza mlungu umenewo. Iyinso ndi nthaŵi imene timachita zitsanzo zokonzekera utumiki.

Ana athu onse ndi obatizidwa. Ndiponso Dorcas ndi Samuel akhala akuchita upainiya kuyambira 1994, ndipo kuyambira pamene anabatizidwa Jaimito wakhala akuchita upainiya wothandiza. Anawa adakali pasukulu, ndipo onse ali ndi cholinga chakuti adzatumikire mokulirapo akadzatsiriza. Alita amagwiritsa ntchito nthaŵi yake mosamala; kuchita upainiya ndi kusamalira ntchito za pakhomo pathu. Kwa zaka zambiri kuphatikizapo zaka zimene ndinali ku misasa, ndinali mpainiya. Komabe, kuyambira 1993, ndakhala ndikumakagwira ntchito pa ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova.

Madalitso Ochokera kwa Mulungu Apitirira

Mu 1997, ndinalandira dalitso lalikulu lokachita kosi ya abale a m’Komiti ya Nthambi ya Mboni za Yehova. Kosi imeneyi inachitikira ku United States ku Likulu la Maphunziro a Watchtower ku Patterson, New York. Choncho, khama langa pa kuphunzira chingerezi ndinapindula nalonso. Pobwerera kwathu, ndinatha kukumana ndi atumiki a Yehova a m’mayiko ena, ndipo zimenezi zinachititsa mtima wanga kusefukira ndi chiyamikiro kaamba ka ubale wathu wapadziko lonse!

Chikondi choterechi pakati pa Akristu oona n’chimenenso chathandiza kwambiri kukokera zikwi za anthu oona mtima kuti agwirizane ndi Mboni za Yehova m’Mozambique monse. (Yohane 13:35) Poyamba panali anthu 7,000 amene ankalalikira pamene tinathamangitsidwira ku misasa, tsopano tili ndi anthu oposa 29,000 amene akulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu m’Mozambique monse. Ameneŵa ali m’mipingo yopitirira 665, koma panali mipingo inayi yokha mu 1958.

Chilolezo chinaperekedwa mu 1993, kuti ku Maputo kumangidwe ofesi ya nthambi imene idzakhale ndi antchito opitirira 75 kuti isamalire kupita patsogolo kwa kulambira koyera kumeneku. Patatha zaka pafupifupi zinayi za kumanga, ntchitoyo inatha. Kenaka, pa December 19, 1998 chisangalalo chathu chinasefukira pamene anthu 1,098 anabwera kuchokera kumayiko ambiri kuti adzakhalepo pa kupatulira kwa nthambi yokongola imeneyi. Pa pologalamuyo, ndinali ndi mwayi wofunsa mafunso anthu othaŵa kwawo amene akhala zaka zambiri ku Carico. Ndinafunsa kuti amene anathamangitsidwira kumeneko akweze manja, ndipo anthu amene anabwera anakhudzidwa mitima kwambiri poona manja ambirimbiri amene anakwezedwa.

Tsiku lotsatira khamu la anthu okwanira 8,525 linabwera ku Nyumba ya Misonkhano ya Matola kuti lidzamvere pologalamu ya kupatulira holoyo, nkhani zolimbikitsa zochokera m’mayiko ena, ndi nkhani zochokera m’Baibulo zokambidwa ndi alendo ochokera ku likulu la Mboni za Yehova padziko lonse ku Brooklyn, New York.

N’zoona, kuyambira nthaŵi imene ndinadziŵa choonadi cha Baibulo ndidakali wachinyamata, ndakhala ndikutsutsidwa ndi a m’banja langa, kutsala pang’ono kuphedwa, ndi chizunzo chopweteka kwambiri chimene nthaŵi zina chinkandipangitsa kuti ndiziganiza kuti kufa ndibwinopo kusiyana ndi kukhalabe moyo. Komabe, ndimasangalala chifukwa chakuti ubwenzi wanga ndi Yehova walimbitsidwa chifukwa cha zinthu zimene ndakumana nazozi, Inde, monga momwe wa masalmo wa m’Baibulo Davide ananenera, “Mulungu ndiye mthandizi wanga; Ambuye ndiye wachirikiza moyo wanga.” (Salmo 54:4) Wakhala mwayi wosayerekezeka kwa banja langa ndi ine kumulambira Yehova pamodzi ndi banja lapadziko lonse la alambiri ake.

[Chithunzi patsamba 23]

Mboni kumaso kwa Nyumba ya Ufumu imene zinamanga m’nthaŵi imene zinalekanitsidwa ndi anthu ena

[Chithunzi patsamba 24]

Tikuchita phunziro lathu la Baibulo la banja

[Chithunzi patsamba 25]

Amene anakhalako ku misasa ya ku Carico anakweza manja

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena