Abale Achinyamata, Kodi Mukuyesetsa Kuti Muyenerere Udindo mu Mpingo?
1. Kodi m’bale wachinyamata angayambe liti kutsatira malangizo a pa 1 Timoteyo 3:1?
1 “Ngati munthu aliyense akuyesetsa . . . , akufuna ntchito yabwino.” (1 Tim. 3:1) Mawu ouziridwa amenewa akulimbikitsa abale kuyesetsa kuti ayenerere udindo mu mpingo. Kodi muyenera kudikira kuti mukule kaye musanayambe kuchita zimenezi? Ayi. Ndi bwino kuyamba kuchita zimenezi mudakali wachinyamata. Mukamachita zimenezi mungaphunzire zambiri, ndipo zingakuchititseni kuti mudzayenerere kukhala mtumiki wothandiza mukadzakula. (1 Tim. 3:10) Ngati ndinu m’bale wachinyamata wobatizidwa, kodi mungatani kuti muyenerere udindo mu mpingo?
2. Kodi mungasonyeze bwanji mtima wodzipereka?
2 Kudzipereka: Kumbukirani kuti mukuyesetsa kuti muyenerere ntchito yabwino, osati kufuna kutchuka kapena kungofuna udindo. Choncho khalani ndi mtima wofuna kuthandiza abale ndi alongo anu. Njira imodzi imene mungachitire zimenezi ndi kuganizira chitsanzo cha Yesu. (Mat. 20:28; Yoh. 4:6, 7; 13:4, 5) Pemphani Yehova kuti akuthandizeni kuti muzikhala ndi chidwi ndi anthu ena. (1 Akor. 10:24) Kodi mungathandize odwala kapena achikulire mu mpingo wanu? Kodi mungadzipereke kugwira nawo ntchito yotchetcha, yosesa, yokolopa komanso yokonza zinthu zina pa Nyumba ya Ufumu? Kodi mumadzipereka kukamba nkhani ya m’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ngati mwiniwake sanabwere? Mukamadzipereka kuthandiza ena mudzakhala wosangalala kwambiri.—Mac. 20:35.
3. Kodi kukonda zinthu zauzimu n’kofunika bwanji, ndipo mungatani kuti muzikonda zinthu zauzimu?
3 Muzikonda Zinthu Zauzimu: N’kofunika kwambiri kuti munthu azikhala wokonda zinthu zauzimu m’malo mongokhala ndi luso lochitira zinthu. Munthu wokonda zauzimu amaona zinthu mmene Yehova komanso Yesu amazionera. (1 Akor. 2:15, 16) Iye amaonetsa “makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa.” (Agal. 5:22, 23) Amakhalanso wakhama pa ntchito yolalikira, ndipo amaika zinthu zaufumu patsogolo. (Mat. 6:33) Mukhoza kukhala ndi makhalidwe amenewa ngati mutakhala ndi chizolowezi chophunzira mawu a Mulungu panokha. Zimenezi zikuphatikizapo kuwerenga Baibulo tsiku lililonse, kuwerenga magazini alionse a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!, kukonzekera misonkhano komanso kupezeka pa misonkhano ya mpingoyo. (Sal. 1:1, 2; Aheb. 10:24, 25) Polimbikitsa Timoteyo kuti apite patsogolo mwauzimu, Paulo analemba kuti: “Nthawi zonse uzisamala ndi zimene . . . umaphunzitsa.” (1 Tim. 4:15, 16) Choncho mukapatsidwa nkhani m’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, muziyesetsa kuikamba bwino. Muzikonzekera utumiki wakumunda n’kumalalikira nawo nthawi zonse. Muyeneranso kukhala ndi zolinga zauzimu, monga kuchita upainiya, utumiki wa pa Beteli kapena kudzapita ku Sukulu Yophunzitsa Baibulo ya Abale Osakwatira. Kukonda zinthu zauzimu kungakuthandizani ‘kuthawa zilakolako zaunyamata.’—2 Tim. 2:22.
4. Kodi kukhala wodalirika komanso wokhulupirika n’kofunika bwanji?
4 Khalani Wodalirika Komanso Wokhulupirika: Chifukwa choti abale omwe anapatsidwa udindo wogawa chakudya kwa Akhristu osauka m’nthawi ya atumwi anali “a mbiri yabwino,” omwenso ankadziwika kuti anali odalirika komanso okhulupirika, atumwi sankadera nkhawa za mmene ntchitoyi ingayendere. Zimenezi zinathandiza atumwiwo kuti azichita zinthu zina zofunika. (Mac. 6:1-4) Choncho mukapatsidwa ntchito inayake mu mpingo, muyenera kugwira ntchitoyo ndi mtima wonse. Muyenera kutsanzira Nowa, yemwe anatsatira malangizo amene anapatsidwa omangira chingalawa. (Gen. 6:22) Yehova amaona kuti munthu wokhulupirika ndi wa mtengo wapatali ndipo kukhulupirika kumasonyeza kuti munthuyo amakonda zinthu zauzimu.—1 Akor. 4:2; onani bokosi lakuti, “Ubwino Wophunzitsa Achinyamata.”
5. N’chifukwa chiyani abale achinyamata akufunika kuyesetsa kuti ayenerere udindo mu mpingo?
5 Monga mmene zinaloseredwera, Yehova akuchititsa kuti ntchito yosonkhanitsa anthu ipite patsogolo. (Yes. 60:22) Chaka chilichonse anthu oposa 250,000 amabatizidwa. Chifukwa choti anthu ambiri akubwera m’gulu la Yehova, pakufunika abale ambiri oyenerera omwe angamatumikire m’mipingo. Masiku ano m’gulu la Yehova muli ntchito yambiri yofunika kuti igwiridwe kusiyana ndi m’mbuyomu. (1 Akor. 15:58) Abale achinyamatanu, kodi mukuyesetsa kuti muyenerere udindo mu mpingo? Ngati mukutero, ndiye kuti mukufuna ntchito yabwino.
[Mawu Otsindika patsamba 2]
Chifukwa choti anthu ambiri akubwera m’gulu la Yehova, pakufunika abale ambiri oyenerera omwe angamatumikire m’mipingo
[Bokosi patsamba 3]
Ubwino Wophunzitsa Achinyamata
Abale achinyamata amapindula akulu akamawapatsa ntchito zoti agwire komanso kuwaphunzitsa mmene angagwirire ntchitozo. Mwachitsanzo, pa mpingo wina misonkhano itatha, woyang’anira dera ankacheza ndi wofalitsa wina pafupi ndi pulatifomu. Ndiyeno woyang’anira derayo anaona wachinyamata wina ataima pafupi nawo ndipo anamufunsa ngati akufuna kulankhula ndi iyeyo. M’bale wachinyamatayo anamuyankha kuti anapatsidwa ntchito yosesa kupulatifomu misonkhano ikatha. Makolo ake amafuna azipita, koma iye sankafuna kupita chifukwa ankafunitsitsa kuti agwire kaye ntchito yakeyo. Choncho woyang’anira derayo atamva zimenezi anasuntha. Iye anati: “Akulu mu mpingo umenewu ankaphunzitsa achinyamata powapatsa ntchito zoti azigwira. Chifukwa cha zimenezi, nthawi zambiri ndikamachezera mpingowo pankakhala achinyamata omwe akulu awavomereza kuti akhale atumiki othandiza.”