Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb21 November tsamba 3
  • Timathokoza Yehova Chifukwa cha Chikondi Chanu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Timathokoza Yehova Chifukwa cha Chikondi Chanu
  • Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
  • Nkhani Yofanana
  • “Khalani Opatsa”
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2022
  • ‘Timakobidi Tiwiri Tating’ono’ Tamtengo Wapatali
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
  • “Muzipereka Mphatso kwa Yehova”
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
  • ‘Muziika Kenakake Pambali’
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
Onani Zambiri
Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
mwb21 November tsamba 3
Zithunzi: 1. M’bale akuponya ndalama m’bokosi la zopereka. 2. JW Box. 3. Abale akukonza malo amene akufuna ajambulirepo vidiyo.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Timathokoza Yehova Chifukwa cha Chikondi Chanu

Ngakhale kuti Akhristu a mpingo wa ku Tesalonika ankakumana ndi mavuto, iwo anasonyeza chikondi kwa Akhristu anzawo. (2At 1:3, 4) Masiku anonso, anthu a Yehova amasonyeza chikondi choterechi kwa abale awo padziko lonse. Nkhani za pa jw.org za mutu wakuti “Kodi Zopereka Zanu Zimagwiritsidwa Ntchito Bwanji?” zimafotokoza mmene zopereka zanu zimathandizira abale panthawi imene akukumana ndi mavuto. Timakuyamikirani chifukwa cha chikondi chanu komanso mtima wanu wopatsa.

ONERANI VIDIYO YAKUTI NTHAWI ZONSE ‘TIMAYAMIKA MULUNGU CHIFUKWA CHA INU,’ NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

• Kodi zopereka zathu zimathandiza pa zinthu ziti?

• Kodi njira yabwino kwambiri yoperekera thandizo la ndalama kwa abale ndi alongo amene akufunikira thandizo ndi iti?​—Onaninso nkhani ya pa jw.org yakuti “Zimene Ena Ali Nazo Zimathandizira pa Zimene Ena Akusowa”

DZIWANI ZAMBIRI PAWEBUSAITI YATHU

Kodi mungapereke bwanji ndalama zothandizira ntchito ya Mboni za Yehova? Dinani pa mawu oti “Donations” m’munsi mwa tsamba loyamba la JW Library. M’mayiko ambiri, pangakhale linki ina yopita ku nkhani yakuti “Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri” imene imayankha mafunso okhudza zopereka.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena