-
Yehova Ndi “Woulula Zinsinsi”Nsanja ya Olonda—2012 | June 15
-
-
Yehova Ndi “Woulula Zinsinsi”
“Ndithudi Mulungu wa anthu inu ndi Mulungu wa milungu yonse, Ambuye wa mafumu onse ndiponso Woulula zinsinsi.”—DAN. 2:47.
KODI MUNGAYANKHE BWANJI?
Kodi Yehova anaulula zinthu ziti zam’tsogolo?
Kodi mitu 6 yoyamba ya chilombo ikuimira maufumu ati?
Kodi pali kugwirizana kotani pakati pa chilombo cha m’buku la Chivumbulutso ndi chifaniziro chimene Nebukadinezara anaona?
1, 2. Kodi Yehova watiululira chiyani, nanga n’chifukwa chiyani wachita zimenezi?
KODI ndi maboma ati amene adzakhala amphamvu kwambiri padziko lapansi pa nthawi imene Ufumu wa Mulungu uzidzathetsa ulamuliro wa anthu? Tikudziwa yankho la funsoli chifukwa Yehova Mulungu, yemwe ndi “Woulula zinsinsi,” anatiululira. Iye amatithandiza kudziwa mabomawa kuchokera pa zimene mneneri Danieli ndiponso mtumwi Yohane analemba.
2 Yehova anasonyeza anthu amenewa masomphenya okhala ndi zilombo zosiyanasiyana. Komanso anauza Danieli tanthauzo la loto linalake la chifaniziro chachikulu kwambiri. Yehova anachititsa kuti zinthuzi zilembedwe m’Baibulo kuti zitithandize. (Aroma 15:4) Anachita zimenezi n’cholinga choti tikhale ndi chikhulupiriro champhamvu kuti posachedwapa Ufumu wake udzaphwanya maboma onse a anthu.—Dan. 2:44.
3. Kuti timvetse maulosi molondola, kodi choyamba tiyenera kudziwa chiyani ndipo n’chifukwa chiyani?
3 Masomphenya a Danieli ndi Yohane amasonyeza mafumu 8, kapena kuti maulamuliro 8 a anthu. Amasonyezanso nthawi imene mafumuwa adzakhalapo. Koma kuti timvetse molondola za masomphenyawa, tiyenera kudziwa bwino tanthauzo la ulosi woyambirira wa m’Baibulo. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa chakuti nkhani yaikulu m’Baibulo imakhudza kukwaniritsidwa kwa ulosi umenewu. Choncho maulosi ena onse a m’Baibulo amakhudzana ndi ulosi woyambirirawu.
MBEWU YA NJOKA NDIPONSO CHILOMBO
4. Kodi mbewu ya mkazi ndi ndani, nanga mbewu imeneyi idzachita chiyani?
4 Anthu oyambirira atangopanduka m’munda wa Edeni, Yehova analonjeza kuti “mkazi” adzatulutsa “mbewu.”a (Werengani Genesis 3:15.) Analonjezanso kuti mbewu imeneyi idzaphwanya mutu wa njoka, kapena kuti Satana. Yehova anadzaulula kuti mbewuyi idzachokera mu mzera wa Abulahamu, mu mtundu wa Aisiraeli, m’fuko la Yuda ndiponso kuti idzakhala mbadwa ya Mfumu Davide. (Gen. 22:15-18; 49:10; Sal. 89:3, 4; Luka 1:30-33) Mbali yaikulu ya mbewuyi inadzakhala Khristu Yesu. (Agal. 3:16) Mbali yachiwiri ya mbewuyi ndiyo anthu odzozedwa ndi mzimu mu mpingo wachikhristu. (Agal. 3:26-29) Yesu limodzi ndi odzozedwa amapanga Ufumu wa Mulungu. Mulungu adzagwiritsa ntchito Ufumuwu kuti aphwanye Satana.—Luka 12:32; Aroma 16:20.
5, 6. (a) Kodi Danieli ndi Yohane analemba za maulamuliro amphamvu angati? (b) Kodi mitu ya chilombo chotchulidwa m’buku la Chivumbulutso imaimira chiyani?
5 Ulosi woyambirira umene Mulungu ananena mu Edeni uja unanenanso kuti Satana adzatulutsa “mbewu.” Unanena kuti mbewu yake idzadana ndi mbewu ya mkazi. Kodi mbewu ya njokayo ndi ndani? Ndi onse amene amatsanzira Satana podana ndi Mulungu ndiponso kudana ndi anthu a Mulungu. Kuyambira kalekale, Satana anakonza zoti mbewu yake izikhala ndi maufumu kapena maboma. (Luka 4:5, 6) Koma ndi maufumu ochepa okha padziko lapansi amene alowerera kwambiri m’zochita za anthu a Mulungu omwe ndi Aisiraeli ndiponso Akhristu odzozedwa. Kudziwa zimenezi kungatithandize kumvetsa chifukwa chake masomphenya a Danieli ndiponso Yohane amangonena za maulamuliro amphamvu 8 okha.
6 Cha m’ma 96 C.E., Yesu amene anali ataukitsidwa, anaonetsa mtumwi Yohane masomphenya osiyanasiyana ochititsa chidwi. (Chiv. 1:1) M’masomphenya ena, Yohane anaona Mdyerekezi yemwe anaimiridwa ndi chinjoka chimene chinali chitaima m’mbali mwa nyanja yaikulu. (Werengani Chivumbulutso 13:1, 2.) Yohane anaonanso chilombo chachilendo chikutuluka m’nyanjayo ndipo Mdyerekezi anachipatsa ulamuliro waukulu. Kenako, mngelo anauzanso Yohane kuti mitu 7 ya chilombo chofiira, chomwe ndi chifaniziro cha chilombo cha pa Chivumbulutso 13:1, imaimira “mafumu 7,” kapena kuti maboma 7. (Chiv. 13:14, 15; 17:3, 9, 10) Pa nthawi imene Yohane analemba zimenezi, mafumu asanu anali atagwa, imodzi inalipo ndipo ‘inayo inali isanafikebe.’ Kodi mafumu kapena kuti maulamuliro amphamvu padziko lonse amenewa ndi ati? Tiyeni tikambirane za mutu uliwonse wa chilombo chotchulidwa m’buku la Chivumbulutso. Tionanso mmene ulosi wa Danieli ungatithandizire kudziwa za mafumuwa. Ulosiwu unalembedwa kudakali zaka zambiri ena mwa mafumuwa asanakhaleko.
MITU IWIRI YOYAMBA IKUIMIRA IGUPUTO NDI ASURI
7. Kodi mutu woyamba ukuimira ndani ndipo n’chifukwa chiyani tikutero?
7 Mutu woyamba wa chilombochi ukuimira Iguputo. Tikutero chifukwa chakuti Iguputo unali ufumu wamphamvu woyamba kudana ndi anthu a Mulungu, kapena kuti Aisiraeli. Mbewu ya mkazi yolonjezedwa inayenera kuchokera m’mbadwa za Abulahamu ndipo mbadwa zimenezi zinayamba kuchuluka kwambiri ku Iguputo. Ndiyeno ufumu wa Iguputo unayamba kupondereza Aisiraeliwo. Satana anayesa kuwononga anthu onse a Mulunguwo mbewuyo isanafike. Kodi anachita bwanji zimenezi? Iye anachititsa Farao kuganiza zoti awononge ana aamuna onse a Aisiraeli. Yehova analepheretsa zimenezi ndipo anamasula anthu ake ku ukapolo ku Iguputo. (Eks. 1:15-20; 14:13) Kenako anathandiza Aisiraeliwo kukhazikika m’Dziko Lolonjezedwa.
8. Kodi mutu wachiwiri ukuimira ndani ndipo unayesa kuchita chiyani?
8 Mutu wachiwiri wa chilombo ukuimira Asuri. Ufumu wamphamvu umenewu unayesanso kuwononga anthu onse a Mulungu. N’zoona kuti Yehova anagwiritsa ntchito Asuri polanga ufumu wa mafuko 10 a Isiraeli. Anachita zimenezi chifukwa iwo anali kulambira mafano komanso anapanduka. Koma kenako Asuri anaukiranso Yerusalemu. N’kutheka kuti Satana ankafuna kuwononga mzere wa mafumu umene Yesu anali kudzabadwira. Izi zinali zosemphana ndi cholinga cha Yehova. Choncho iye anapulumutsa anthu ake okhulupirika m’njira yozizwitsa powononga Asuriwo.—2 Maf. 19:32-35; Yes. 10:5, 6, 12-15.
MUTU WACHITATU UKUIMIRA BABULO
9, 10. (a) Kodi Yehova analola Ababulo kuchita chiyani? (b) Kodi ndi zinthu ziti zimene zinayenera kuchitika kuti ulosi ukwaniritsidwe?
9 Mutu wachitatu wa chilombo chimene Yohane anaona ukuimira ufumu umene likulu lake linali Babulo. Yehova analola Ababulo kuwononga Yerusalemu n’kutenga anthu ake kupita nawo ku ukapolo. Koma tsoka limeneli lisanafike, Yehova anachenjeza Aisiraeli opandukawo. (2 Maf. 20:16-18) Iye analosera kuti mzere wa mafumu amene anakhala “pampando wachifumu wa Yehova” ku Yerusalemu udzawonongedwa. (1 Mbiri 29:23) Koma Yehova analonjezanso kuti mbadwa ya Mfumu Davide, yomwe inali ‘yoyenerera mwalamulo,’ idzafika n’kutenga ufumuwo.—Ezek. 21:25-27.
10 Ulosi wina unasonyeza kuti Ayuda adzakhala akulambirabe pakachisi ku Yerusalemu pa nthawi imene Wodzozedwa, kapena kuti Mesiya amene Mulungu analonjeza, azidzafika. (Dan. 9:24-27) Ulosi wina, umene unalembedwa Aisiraeli asanapite ku ukapolo ku Babulo, unanena kuti Mesiyayo adzabadwira ku Betelehemu. (Mika 5:2) Kuti maulosi amenewa akwaniritsidwe, panafunika kuti Ayuda amasulidwe ku ukapolo, abwerere kwawo ndiponso amangenso kachisi. Koma Ababulo sankamasula akapolo awo. Ndiyeno kodi Ayudawo akanamasulidwa bwanji? Yehova anaulula zimenezi kwa aneneri ake.—Amosi 3:7.
11. Kodi ndi zinthu ziti zimene zinaimira ufumu wa Babulo? (Onani mawu a m’munsi.)
11 Mneneri Danieli anali m’gulu la anthu amene anatengedwa n’kupita ku ukapolo ku Babulo. (Dan. 1:1-6) Yehova anamugwiritsa ntchito poulula maufumu amene anadzabwera pambuyo pa ufumu wa Babulo. Yehova anaulula zinsinsizi pogwiritsa ntchito zizindikiro zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, anachititsa Mfumu Nebukadinezara ya ku Babulo kulota za chifaniziro chachikulu chopangidwa ndi zinthu zosiyanasiyana. (Werengani Danieli 2:1, 19, 31-38.) Kudzera mwa Danieli, Yehova anaulula kuti mutu wagolide wa chifanizirochi unkaimira ufumu wa Babulo.b Chifuwa ndi manja a chifanizirochi zinali zasiliva ndipo zinkaimira ulamuliro wamphamvu padziko lonse umene unabwera pambuyo pa Babulo. Kodi ufumu umenewu unali uti ndipo unachita chiyani ndi anthu a Mulungu?
MUTU WACHINAYI UKUIMIRA MEDIYA NDI PERISIYA
12, 13. (a) Kodi Yehova anaulula zinthu ziti zokhudza kugonjetsedwa kwa Babulo? (b) N’chifukwa chiyani zili zomveka kunena kuti ufumu wa Mediya ndi Perisiya ukuimiridwa ndi mutu wachinayi wa chilombo?
12 Kudakali zaka zoposa 100 kuti nthawi ya Danieli ifike, Yehova anaulula kudzera mwa mneneri Yesaya zinthu zina zokhudza ulamuliro wamphamvu padziko lonse umene udzagonjetse Babulo. Yehova anafotokoza mmene ufumuwo udzagonjetsere mzinda wa Babulo komanso dzina la munthu amene adzaugonjetse. Mfumu yodzagonjetsa Babulo inali Koresi wa ku Perisiya. (Yes. 44:28; 45:1-2) Danieli anaonanso masomphenya ena awiri okhudza ufumu wa Mediya ndi Perisiya. M’masomphenya oyamba, ufumuwu unaimiridwa ndi chimbalangondo chomwe chinali chotukuka mbali imodzi ndipo chinauzidwa kuti: “Idya nyama yambiri.” (Dan. 7:5) M’masomphenya achiwiri, Danieli anaona nkhosa yamphongo ya nyanga ziwiri yomwe inkaimiranso ufumu womwewu.—Dan. 8:3, 20.
13 Yehova anagwiritsa ntchito ufumu wa Mediya ndi Perisiya pofuna kukwaniritsa ulosi. Ufumuwu unagonjetsa Babulo n’kulola Aisiraeli kubwerera kwawo. (2 Mbiri 36:22, 23) Koma pa nthawi ina, ufumu womwewu unangotsala pang’ono kuwononga anthu onse a Mulungu. M’buku la Esitere muli nkhani ya chiwembu chimene nduna yaikulu ya ufumu wa Perisiya, dzina lake Hamani, anakonza. Iye anakonza zoti Ayuda onse amene anali m’zigawo zolamulidwa ndi ufumu wa Perisiya aphedwe. Ndipo iye anakonzeratu tsiku loti chiwembuchi chichitike. Koma Yehova analowererapo n’kupulumutsa anthu ake kuti asawonongedwe ndi mbewu ya Satana. (Esitere 1:1-3; 3:8, 9; 8:3, 9-14) Choncho, m’pomveka kunena kuti ufumu wa Mediya ndi Perisiya ukuimiridwa ndi mutu wachinayi wa chilombo cha m’buku la Chivumbulutso.
MUTU WACHISANU UKUIMIRA GIRISI
14, 15. Kodi Yehova anaulula zinthu ziti zokhudza ufumu wakale wa Girisi?
14 Mutu wachisanu wa chilombo cha m’buku la Chivumbulutso ukuimira Girisi. Pomasulira loto la Nebukadinezara, Danieli anaulula kuti ufumuwu ukuimiridwanso ndi mimba ndi ntchafu zamkuwa za chifaniziro chija. Danieli anaonanso masomphenya awiri amene anafotokoza zinthu zochititsa chidwi zokhudza ufumuwu komanso mfumu yake yamphamvu.
15 M’masomphenya oyamba, ufumu wa Girisi unaimiridwa ndi kambuku wokhala ndi mapiko anayi. Izi zinasonyeza kuti ufumuwu uzidzagonjetsa mofulumira. (Dan. 7:6) M’masomphenya achiwiri, Danieli anaona mbuzi yokhala ndi nyanga imodzi yaikulu imene inapha mwamsanga nkhosa yamphongo yokhala ndi nyanga ziwiri, yomwe inkaimira ufumu wa Mediya ndi Perisiya. Yehova anauza Danieli kuti mbuziyi ikuimira Girisi ndipo nyanga yake yaikuluyo ikuimira mfumu yake ina. Kenako Danieli analemba kuti nyanga yaikuluyo idzathyoka ndipo m’malo mwake padzamera zina zinayi. Ngakhale kuti ulosiwu unalembedwa zaka mahandiredi angapo ufumu wa Girisi usanakhale wamphamvu, zonse zimene analemba zinakwaniritsidwa. Nyangayi ikuimira Alekizanda Wamkulu, yemwe anali mfumu yamphamvu ya ufumu wa Girisi. Iye anatsogolera pa nkhondo yomenyana ndi Mediya ndi Perisiya. Koma nyangayi inathyoka msanga. Tikutero chifukwa chakuti mfumuyi inamwalira ili ndi zaka 32 zokha ndipo pa nthawiyi inali yamphamvu kwambiri. Ndiyeno akuluakulu anayi a asilikali ake anagawana ufumuwu.—Werengani Danieli 8:20-22.
16. Kodi Antiyokasi Wachinayi anachita zotani?
16 Ufumu wa Girisi utagonjetsa Perisiya, unayamba kulamulira dziko limene anthu a Mulungu ankakhala. Pa nthawiyi, Ayuda anali atabwerera ku Dziko Lolonjezedwa ndipo anali atamanganso kachisi ku Yerusalemu. Ayudawo anali adakalibe anthu osankhidwa a Mulungu ndipo kachisi amene anamumanganso uja ndi amene anali malo awo olambirira. Koma m’zaka za m’ma 100 B.C.E., ufumu wa Girisi, womwe ndi mutu wachisanu wa chilombo chija, unaukira anthu a Mulungu. Antiyokasi Wachinayi anali mmodzi wa asilikali amene analowa m’malo mwa Alekizanda. Iye anaika guwa lansembe loperekera nsembe kwa milungu yonyenga m’bwalo la kachisi ku Yerusalemu. Analamula kuti munthu aliyense wotsatira chipembedzo chachiyuda aphedwe. Izi zikusonyeza kuti mbewu ya Satana inali kudana kwambiri ndi anthu a Mulungu. Koma posapita nthawi, ufumu wa Girisi unalowedwa m’malo ndi ulamuliro wina wamphamvu padziko lonse. Kodi mutu wa 6 ukuimira ufumu uti?
MUTU WA 6 UKUIMIRA UFUMU WA ROMA UMENE UNALI ‘WOOPSA KWAMBIRI’
17. Kodi mutu wa 6 unachita chiyani chokhudza kukwaniritsidwa kwa ulosi wa pa Genesis 3:15?
17 Pa nthawi imene Yohane ankaona masomphenya a chilombo, ufumu wa Roma ndi umene unali wamphamvu. (Chiv. 17:10) Mutu wa 6 umenewu unachita chinthu chachikulu chokhudza kukwaniritsidwa kwa ulosi wa pa Genesis 3:15. Satana anagwiritsa ntchito asilikali achiroma kuti avulaze “chidendene” cha mbewu yolonjezedwa. Kodi anachita bwanji zimenezi? Iwo anaimba Yesu mlandu wabodza woukira boma ndipo anamupha. (Mat. 27:26) Koma bala limeneli linachira mwamsanga chifukwa Yehova anaukitsa Yesu.
18. (a) Kodi Yehova anasankha mtundu watsopano uti ndipo n’chifukwa chiyani? (b) Kodi mbewu ya njoka inasonyeza bwanji kuti inkalusirabe mbewu ya mkazi?
18 Atsogoleri achipembedzo a Isiraeli anagwirizana ndi Aroma pokonzera Yesu chiwembu ndipo Ayuda ambiri anakana Yesu. Choncho, Yehova anasiya kuona mtundu wa Isiraeli ngati anthu ake. (Mat. 23:38; Mac. 2:22, 23) M’malomwake, anasankha mtundu watsopano womwe ndi “Isiraeli wa Mulungu.” (Agal. 3:26-29; 6:16) Mtundu watsopanowu ndi wa Akhristu odzozedwa ndipo wapangidwa ndi Ayuda komanso anthu amitundu ina. (Aef. 2:11-18) Yesu atafa n’kuukitsidwa, mbewu ya njoka inapitirizabe kulusira mbewu ya mkazi. Aroma anayesanso kuwononga mpingo wa Akhristu odzozedwa, womwe ndi mbali yachiwiri ya mbewu ya mkazi.c
19. (a) Kodi Danieli anafotokoza bwanji ulamuliro wamphamvu padziko lonse wa nambala 6? (b) Kodi tidzakambirana chiyani m’nkhani imene ili patsamba 14?
19 M’loto la Nebukadinezara limene Danieli anamasulira, ufumu wa Roma ukuimiridwa ndi miyendo yachitsulo. (Dan. 2:33) Danieli anaonanso masomphenya ena osonyeza ufumu wa Roma komanso ulamuliro wina wamphamvu padziko lonse wochokera mu ufumu wa Roma womwewo. (Werengani Danieli 7:7, 8.) Kwa zaka zambiri, adani a ufumu wa Roma ankaona kuti ufumuwo uli ngati chilombo “choopsa kwambiri ndiponso chochititsa mantha komanso champhamvu kwambiri.” Koma ulosiwo unanena kuti “nyanga 10” zidzachokera mu ufumuwo ndipo nyanga ina yaing’ono idzamera yomwe idzakhala yamphamvu kwambiri. Kodi nyanga 10 zikuimira chiyani, nanga yaing’onoyo ikuimira chiyani? Kodi nyanga yaing’onoyo ikugwirizana bwanji ndi chifaniziro chachikulu chimene Nebukadinezara anaona? Nkhani imene ili patsamba 14 iyankha mafunso amenewa.
-
-
Yehova Waulula “Zimene Ziyenera Kuchitika Posachedwapa”Nsanja ya Olonda—2012 | June 15
-
-
Yehova Waulula “Zimene Ziyenera Kuchitika Posachedwapa”
“Chivumbulutso choperekedwa ndi Yesu Khristu, chimene Mulungu anamupatsa, kuti aonetse akapolo ake zinthu zimene ziyenera kuchitika posachedwapa.”—CHIV. 1:1.
KODI MUNGAYANKHE BWANJI?
Kodi ndi mbali iti ya chifaniziro chachikulu imene ikuimira ulamuliro wamphamvu padziko lonse wa Britain ndi America?
Kodi Yohane anafotokoza bwanji mgwirizano wa pakati pa ulamuliro wa Britain ndi America ndi bungwe la United Nations?
Kodi Danieli ndi Yohane anafotokoza kuti ulamuliro wa anthu udzatha bwanji?
1, 2. (a) Kodi maulosi a Danieli ndi Yohane amatithandiza bwanji? (b) Kodi mitu 6 yoyambirira ya chilombo imaimira chiyani?
MAULOSI a Danieli ndiponso a Yohane amagwirizana ndipo amatithandiza kudziwa tanthauzo la zinthu zimene zikuchitika panopa ndiponso zimene zidzachitike m’tsogolo. Kodi tikuphunzira chiyani pa masomphenya a Yohane onena za chilombo, zimene Danieli anafotokoza zokhudza chilombo choopsa cha nyanga 10 komanso zimene Danieli ananena zokhudza chifaniziro chachikulu? Kodi kumvetsa bwino maulosi amenewa kuyenera kutilimbikitsa kuchita chiyani?
2 Tiyeni tikambirane masomphenya a Yohane onena za chilombo. (Chiv. 13:1-18) Monga tinaonera m’nkhani yoyamba ija, mitu 6 yoyamba ikuimira ufumu wa Iguputo, Asuri, Babulo, Mediya ndi Perisiya, Girisi ndiponso Roma. Maufumu onsewa anadana ndi mbewu ya mkazi. (Gen. 3:15) Ufumu wa Roma, womwe ndi mutu wa 6, unakhalabe wamphamvu kwa zaka mahandiredi ambiri kuchokera pamene Yohane analemba masomphenya ake. Ndiyeno patapita nthawi, mutu wa 7 unayenera kulowa m’malo mwa Roma. Kodi ndi ulamuliro uti wamphamvu padziko lonse umene unalowa m’malo? Nanga unachitira zotani mbewu ya mkazi?
MAYIKO A BRITAIN NDI UNITED STATES ANAKHALA AMPHAMVU
3. Kodi chilombo choopsa cha nyanga 10 chikuimira chiyani ndipo nyanga 10 zikuimira chiyani?
3 Kodi tingadziwe bwanji ufumu umene mutu wa 7 wa chilombo cha m’chaputala 13 cha buku la Chivumbulutso ukuimira? Tiyenera kuyerekezera masomphenya a Yohane ndi a Danieli okhudza chilombo choopsa cha nyanga 10.a (Werengani Danieli 7:7, 8, 23, 24.) Chilombo chimene Danieli anaona chinaimira ufumu wamphamvu padziko lonse wa Roma. (Onani tchati patsamba 12 ndi 13.) Ufumu wa Roma unayamba kugawikana m’zaka za m’ma 400 C.E. Nyanga 10 zimene zinamera pamutu wa chilombo choopsachi zikuimira maufumu amene anachokera mu ufumu wa Roma womwewu.
4, 5. (a) Kodi nyanga yaing’ono inachita zotani? (b) Kodi mutu wa 7 wa chilombo ukuimira ufumu uti?
4 Koma nyanga zinayi zokha za chilombo choopsachi ndi zimene zimatchulidwa mwapadera. Pa nyanga zinayizi, imodzi “yaing’ono” inazula zitatu zinazo. Zimenezi zinakwaniritsidwa pamene dziko la Britain, lomwe linali m’dera lolamulidwa ndi ufumu wa Roma, linakhala lamphamvu kwambiri. Koma pamene zinkafika zaka za m’ma 1600, zimenezi zinali zisanachitike. Mayiko ena atatu amene anachokera mu ufumu wa Roma, omwe anali Spain, Netherlands ndi France ndi amene anali amphamvu. Ndiyeno ufumu wa Britain unazula maufumu enawo m’njira yoti unayamba kukhala wamphamvu kwambiri kuposa maufumuwo. Pakati pa zaka za m’ma 1700, ufumu wa Britain unali utayamba kukula mphamvu. Koma pa nthawiyi, unali usanakhale mutu wa 7 wa chilombo.
5 Ngakhale kuti ufumu wa Britain unali utayamba kukhala wamphamvu, madera a ku North America anachoka mu ulamuliro wake. Komabe, ufumu wa Britain unateteza maderawo ndi asilikali ake apanyanja. Maderawo ndi amene anapanga dziko la United States ndipo dzikolo linakhala lamphamvu kwambiri. Pamene tsiku la Ambuye linkayamba mu 1914, dziko la Britain linali kulamulira dera lalikulu kwambiri kuposa ufumu uliwonse m’mbuyomo. Ndipo dziko la United States linali lamphamvu padziko lonse pa nkhani zamalonda.b Ndiyeno pa nkhondo yoyamba ya padziko lonse, dziko la United States linapanga mgwirizano wapadera ndi dziko la Britain. Izi zinachititsa kuti Britain ndi America apange ufumu wamphamvu padziko lonse womwe unaimiridwa ndi mutu wa 7 wa chilombo. Kodi ufumu umenewu unachita zotani ndi mbewu ya mkazi?
6. Kodi mutu wa 7 wa chilombo wachitira zotani anthu a Mulungu?
6 Tsiku la Ambuye litangoyamba, mutu wa 7 wa chilombo unaukira anthu a Mulungu kapena kuti otsalira a abale a Khristu padziko lapansi. (Mat. 25:40) Yesu anasonyeza kuti pa nthawi ya kukhalapo kwake, otsalira a mbewu adzakhala akugwira ntchito padziko lapansi. (Mat. 24:45-47; Agal. 3:26-29) Ulamuliro wamphamvu padziko lonse wa Britain ndi America unachita nkhondo ndi oyerawo. (Chiv. 13:3, 7) Pa nthawi ya nkhondo yoyamba ya padziko lonse, ulamulirowu unapondereza anthu a Mulungu, kuotcha mabuku awo ndiponso kuika m’ndende anthu oimira gulu la kapolo wokhulupirika. Zimene mutu wa 7 wa chilombochi unachita zinali ngati kupha ntchito yolalikira kwakanthawi. Yehova anali ataoneratu zochitikazi ndipo anaziulula kwa Yohane. Yehova anauzanso Yohane kuti mbali yachiwiri ya mbewu idzakhalanso ndi mphamvu n’kuyamba kutumikira Mulungu mwakhama. (Chiv. 11:3, 7-11) Mbiri ya atumiki a Yehova a masiku ano ikusonyeza kuti zimenezi zinachitikadi.
ULAMULIRO WA BRITAIN NDI AMERICA KOMANSO MAPAZI ACHITSULO NDI DONGO
7. Kodi mutu wa 7 wa chilombo ukugwirizana bwanji ndi chifaniziro chachikulu?
7 Mapazi a chifaniziro chachikulu akuimira ufumu umene ukuimiridwanso ndi mutu wa 7 wa chilombo. Ufumu umenewu ndi ufumu wa Britain ndi America. Ufumu wa Britain unachokera mu ufumu wa Roma. Popeza dziko la United States linachokera mu ufumu wa Britain, tinganenenso kuti unachokera mu ufumu wa Roma. Choncho mapaziwo apangidwa ndi chitsulo koma chitsulocho n’chosakanizidwa ndi dongo. (Werengani Danieli 2:41-43.) Mmene mapaziwa alili zikugwirizana ndi nthawi imene mutu wa 7, womwe ndi ulamuliro wa Britain ndi America, unakhala wamphamvu padziko lonse. Chitsulo n’cholimba koma chikasakanizidwa ndi dongo, sichilimba. Mofanana ndi zimenezi, ulamuliro wamphamvu padziko lonse wa Britain ndi America ndi wofooka tikayerekezera ndi kumene unachokera, ku ulamuliro wa Roma. N’chifukwa chiyani tikutero?
8, 9. (a) Kodi ulamuliro wa padziko lonse wa 7 unasonyeza bwanji kuti ndi wolimba ngati chitsulo? (b) Kodi dongo la kumapazi a chifaniziro likuimira chiyani?
8 Nthawi zina, mutu wa 7 wa chilombo unkachita zinthu mwamphamvu ngati chitsulo. Mwachitsanzo, unapambana pa nkhondo yoyamba ya padziko lonse. Pa nthawi ya nkhondo yachiwiri ya padziko lonse, mutu wa 7 unasonyezanso kuti ndi wolimba ngati chitsulo.c Nkhondoyi itatha, nthawi zina mutu wa 7 unali kusonyezabe kuti ndi wolimba ngati chitsulo. Komabe, chitsulochi n’chosakanizidwa ndi dongo.
9 Kwa nthawi yaitali, atumiki a Yehova akhala akuyesetsa kumvetsa tanthauzo la mapazi a chifaniziro chimenechi. Lemba la Danieli 2:41 limafotokoza msanganizo wa chitsulo ndi dongo monga “ufumu,” osati maufumu. Choncho dongolo likuimira zinthu zimene anthu ena amene ali pansi pa ulamuliro wa Britain ndi America akuchita. Zochita za anthuwa zimachititsa kuti ulamulirowu ukhale wosalimba poyerekezera ndi ulamuliro wa Roma, womwe unali ngati chitsulo. Dongolo likufotokozedwa ngati “ana a anthu,” kapena kuti anthu wamba. (Dan. 2:43) Anthu amene ali pansi pa ulamulirowu apanga magulu omenyera ufulu wosiyanasiyana. Anthu wamba amenewa achepetsa mphamvu za ulamuliro wa Britain ndi America kuti usakhale ngati chitsulo. Anthu ambiri amasiyana maganizo pa nkhani zokhudza boma ndipo olamulira ena amawina chisankho ndi mavoti ochepa. Zimenezi zimachititsa kuti olamulirawo asakhale ndi mphamvu zokwanira zochita zimene akufuna. Danieli anati: “Pa zinthu zina ufumuwo udzakhala wolimba koma pa zinthu zina udzakhala wosalimba.”—Dan. 2:42; 2 Tim. 3:1-3.
10, 11. (a) Kodi n’chiyani chidzachitikire “mapazi”? (b) Kodi tinganene chiyani pa nkhani ya chiwerengero cha zala za chifanizirochi?
10 M’nthawi yathu ino, mayiko a Britain ndi United States akugwirizanabe kwambiri ndipo nthawi zambiri amachitira zinthu limodzi. Maulosi okhudza chifaniziro chachikulu ndiponso chilombo amatsimikizira kuti sipakhalanso ulamuliro wina wamphamvu padziko lonse umene udzalowa m’malo ulamuliro wa Britain ndi America. Ulamuliro wamphamvu padziko lonse womalizirawu ndi wosalimba tikauyerekezera ndi ufumu umene ukuimiridwa ndi miyendo yachitsulo. Koma sikuti udzangotha wokha.
11 Kodi chiwerengero cha zala zakumiyendo za chifanizirochi chili ndi tanthauzo lapadera? Taganizirani izi. M’masomphenya ena, Danieli anatchula ziwerengero za zinthu. Mwachitsanzo, anatchula chiwerengero cha nyanga pamitu ya zilombo zosiyanasiyana. Ziwerengero zimenezi zinali ndi tanthauzo lapadera. Koma pofotokoza chifanizirochi, Danieli sanatchule chiwerengero cha zala zake. Choncho zikuoneka kuti chiwerengero chake chilibe tanthauzo lapadera ngati mmene zilili ndi chiwerengero cha manja, miyendo ndi mapazi ake. Koma zimene Danieli anatchula n’zoti zalazo zidzakhala zachitsulo ndi dongo. Zimene Danieli anafotokoza zikutithandiza kuzindikira kuti ulamuliro wa Britain ndi America ndi umene udzakhale wamphamvu padziko lonse pamene “mwala” woimira Ufumu wa Mulungu udzaphwanya mapazi a chifanizirochi.—Dan. 2:45.
ULAMULIRO WA BRITAIN NDI AMERICA UKUIMIRIDWANSO NDI CHILOMBO CHA NYANGA ZIWIRI
12, 13. Kodi chilombo cha nyanga ziwiri chikuimira chiyani ndipo chinachita zotani?
12 Ngakhale kuti ulamuliro wa Britain ndi America uli ngati chitsulo chosakanizidwa ndi dongo, masomphenya amene Yesu anaonetsa Yohane amasonyeza kuti ulamulirowu udzakhalabe wamphamvu m’masiku otsiriza. N’chifukwa chiyani tikutero? Yohane anaona masomphenya a chilombo cha nyanga ziwiri cholankhula ngati chinjoka. Kodi chilombo chodabwitsachi chikuimira chiyani? Popeza kuti chili ndi nyanga ziwiri, chikuimira ulamuliro wopangidwa ndi mayiko awiri. Apa Yohane anaona ulamuliro wamphamvu padziko lonse wa Britain ndi America koma ukuchita zinthu zina zapadera.—Werengani Chivumbulutso 13:11-15.
13 Chilombo chimenechi chinalimbikitsa anthu kupanga chifaniziro cha chilombo chotchulidwa pa Chivumbulutso 13:1. Yohane analemba kuti chifaniziro cha chilombochi chidzaonekera n’kuzimiririka ndipo kenako chidzaonekeranso. Zimenezi ndi zimene zinachitikadi ndi bungwe limene mayiko a Britain ndi United States analimbikitsa kuti likhazikitsidwe. Bungweli linapangidwa ndi cholinga choti ligwirizanitse ndiponso kuimira maufumu a padziko lapansi.d Bungweli linaonekera nkhondo yoyamba ya padziko lonse itatha ndipo linkatchedwa League of Nations. Koma linazimiririka pamene nkhondo yachiwiri ya padziko lonse inkayamba. Pa nthawi ya nkhondo yachiwiri imeneyi, anthu a Mulungu analengeza kuti malinga ndi ulosi wa m’buku la Chivumbulutso, chifaniziro cha chilombochi chidzaonekeranso. Chifanizirochi chinaonekeradi monga bungwe la United Nations.—Chiv. 17:8.
14. N’chifukwa chiyani chifaniziro cha chilombo chikutchedwa “mfumu ya 8”?
14 Yohane anafotokoza chifaniziro cha chilombo monga “mfumu ya 8.” Koma chifanizirochi sichisonyezedwa ngati mutu wa 8 pa chilombo choyamba chija chifukwa chakuti ndi chifaniziro chabe. Mphamvu zake zimachokera kwa mamembala ake, makamaka Britain ndi America, omwe ndi mamembala ake akuluakulu. (Chiv. 17:10, 11) Nanga n’chifukwa chiyani chikutchedwa “mfumu ya 8”? Chifukwa chakuti chifanizirochi chidzapatsidwa mphamvu zochita zinthu ngati mfumu. Zimene chidzachitezo zidzasinthiratu zinthu padzikoli.
CHIFANIZIRO CHA CHILOMBO CHIDZAWONONGA HULE
15, 16. Kodi hule likuimira chiyani ndipo chikuchitika n’chiyani ndi anthu ake?
15 Yohane ananena kuti pamsana pa chilombo chofiira kwambiri, chomwe ndi chifaniziro cha chilombo, panali hule lophiphiritsa limene linkachilamulira. Dzina la hulelo ndi “Babulo Wamkulu.” (Chiv. 17:1-6) Hulelo likuimira zipembedzo zonse zonyenga ndipo mbali yaikulu ya zipembedzozi ndi matchalitchi amene amati ndi achikhristu. Zipembedzo zimagwirizana ndi chifaniziro cha chilombochi ndipo zimayesetsa kuchilamulira.
16 Koma m’tsiku la Ambuye, Babulo Wamkulu waona kuti madzi ake auma kwambiri, kapena kuti anthu ake ambiri amusiya. (Chiv. 16:12; 17:15) Mwachitsanzo, pamene chifaniziro cha chilombo chinkayamba kuonekera, matchalitchi amene amati ndi achikhristu anali amphamvu kwambiri kumayiko akumadzulo ngati ku Ulaya ndi ku America. Matchalitchi amenewa ndi mbali yaikulu ya Babulo Wamkulu. Masiku ano, anthu asiya kulemekeza kapena kuikira kumbuyo matchalitchiwo komanso atsogoleri awo. Anthu ambiri akukhulupirira kuti zipembedzo zimalimbikitsa kapena kuyambitsa mikangano. Ndipo anthu ena ophunzira ayamba kunena kuti m’pofunika kuthetsa zipembedzo.
17. Kodi n’chiyani chidzachitikire zipembedzo zonyenga posachedwapa, ndipo n’chifukwa chiyani?
17 Koma zipembedzo zonyenga sizidzangotha pazokha. Hulelo lidzapitiriza kukhala lamphamvu ndiponso kuyesetsa kulamulira mafumu mpaka pamene Mulungu adzaika maganizo enaake m’mitima ya mafumuwo. (Werengani Chivumbulutso 17:16, 17.) Posachedwapa, Yehova adzachititsa magulu andale a dziko la Satanali, amene akuimiridwa ndi bungwe la United Nations, kuti aukire zipembedzo zonyenga. Iwo adzathetsa mphamvu zake ndiponso kusakaza chuma chake. Zaka zochepa zapitazo, anthu sakanakhulupirira kuti zimenezi zingachitike. Koma masiku ano, huleli lili pendapenda pamsana wa chilombo chofiira kwambiri. Ngakhale zili choncho, silidzagwa pang’onopang’ono koma lidzagwetsedwa mwadzidzidzi ndiponso mwamphamvu.—Chiv. 18:7, 8, 15-19.
MAPETO A ZILOMBO
18. (a) Kodi chilombo chidzachita chiyani, ndipo zotsatira zake zidzakhala zotani? (b) Kodi lemba la Danieli 2:44 limasonyeza kuti Ufumu wa Mulungu udzawononga mafumu ati? (Onani bokosi patsamba 17.)
18 Zipembedzo zonyenga zitawonongedwa, chilombocho, chomwe ndi mabungwe andale m’dziko la Satanali, chidzalimbikitsidwa kuukira Ufumu wa Mulungu. Popeza sangathe kufika kumwamba, mafumu a dziko adzaukira anthu a padziko lapansi amene ali ku mbali ya Ufumu wa Mulungu. Koma zotsatira zake n’zodziwikiratu. (Chiv. 16:13-16; 17:12-14) Danieli anafotokoza chinthu china chimene chidzachitike pa nkhondo yomaliza. (Werengani Danieli 2:44.) Chilombo chotchulidwa pa Chivumbulutso 13:1, chifaniziro chake ndiponso chilombo cha nyanga ziwiri zidzawonongedwa.
19. Kodi sitiyenera kukayikira za chiyani, ndipo ino ndi nthawi yochita chiyani?
19 Panopo tikukhala m’masiku a mutu wa 7. Palibenso mutu wina umene udzaonekere chilombo chisanawonongedwe. Ulamuliro wa Britain ndi America ndi umene udzakhala wamphamvu padziko lonse pamene zipembedzo zonyenga zizidzawonongedwa. Maulosi a Danieli ndi Yohane akwaniritsidwa ndendende. Choncho sitikukayikira kuti posachedwapa zipembedzo zonyenga zidzawonongedwa ndipo nkhondo ya Aramagedo ifika. Mulungu waulula zinthu zimenezi pasadakhale. Kodi tidzatsatira machenjezo opezeka m’maulosi? (2 Pet. 1:19) Inoyi ndi nthawi yoti tikhale ku mbali ya Yehova ndi Ufumu wake.—Chiv. 14:6, 7.
[Mawu a M’munsi]
a M’Baibulo, nambala ya 10 nthawi zambiri imasonyeza kukwanira choncho apa nambalayi ikuimira maufumu onse amene anachokera mu ufumu wa Roma.
b Ngakhale kuti mayiko a Britain ndi United States analipo m’zaka za m’ma 1700, Yohane ankafotokoza mmene ulamuliro wamphamvu padziko lonse wa mayikowa udzakhalire kumayambiriro kwa tsiku la Ambuye. Masomphenya a m’buku la Chivumbulutso amakwaniritsidwa “m’tsiku la Ambuye.” (Chiv. 1:10) Mutu wa 7 unaonekera kwenikweni pa nthawi ya nkhondo yoyamba ya padziko lonse pamene mayiko a Britain ndi United States anayamba kugwirizana ngati ulamuliro wamphamvu umodzi padziko lonse.
c Danieli anaona kuti mfumuyi idzasakaza zinthu zambiri pa nthawi ya nkhondoyi. Iye analemba kuti: “Idzawononga zinthu zambiri.” (Dan. 8:24) Mwachitsanzo, dziko la United States linasakaza zambiri pamene linaponya mabomba awiri anyukiliya m’dziko limene linkadana ndi ulamuliro wa Britain ndi America.
d Onani buku lakuti Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso Ayandikira, tsamba 240, 241 ndi 253.
[Bokosi patsamba 17]
KODI MAWU OTI “MAUFUMU ENA ONSEWO” AKUNENA ZA NDANI?
Ulosi wa pa Danieli 2:44 unafotokoza kuti Ufumu wa Mulungu “udzaphwanya ndi kuthetsa maufumu ena onsewo.” Ulosi umenewu umanena za maufumu okhawo amene akuimiridwa ndi mbali zosiyanasiyana za chifaniziro.
Koma nanga bwanji za maboma ena onse a anthu? Ulosi wofanana ndi umenewu uli m’buku la Chivumbulutso ndipo umaulula za maboma enawo. Umasonyeza kuti “mafumu a dziko lonse lapansi kumene kuli anthu” adzasonkhanitsidwa kuti amenyane ndi Yehova pa “tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.” (Chiv. 16:14; 19:19-21) Choncho, mafumu oimiridwa ndi mbali za chifaniziro komanso maboma ena onse a anthu adzawonongedwa pa Aramagedo.
-
-
Yehova Anaulula Mafumu 8Nsanja ya Olonda—2012 | June 15
-
-
Yehova Anaulula Mafumu 8
Mabuku a m’Baibulo a Danieli ndiponso Chivumbulutso amaulula mafumu 8, kapena kuti maulamuliro 8 a anthu. Amasonyezanso nthawi imene maulamulirowo adzaonekera. Kumvetsa ulosi woyambirira wa m’Baibulo kungatithandize kumvetsanso maulosi a m’buku la Danieli ndiponso Chivumbulutso amenewa.
Kuyambira kalekale, Satana anakonza zoti mbewu yake izikhala ndi maufumu kapena maboma. (Luka 4:5, 6) Koma ndi maufumu ochepa okha padziko lapansi amene alowerera kwambiri m’zochita za anthu a Mulungu, omwe ndi Aisiraeli ndiponso Akhristu odzozedwa. Masomphenya a Danieli ndi Yohane amafotokoza maulamuliro 8 okha amene achita zimenezi.
[Tchati/Zithunzi pamasamba 12, 13]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
MAULOSI A MAULOSI A M’BUKU
M’BUKU LA DANIELI LA CHIVUMBULUTSO
1. Iguputo
2. Asuri
3. Babulo
4. Mediya ndi
Perisiya
5. Girisi
6. Roma
7. Britain ndi
United Statesa
8. Mabungwe a League of Nations
ndi United Nationsb
ANTHU A MULUNGU
2000 B.C.E.
Abulahamu
1500
Mtundu wa Isiraeli
1000
Danieli 500
B.C.E./C.E.
Yohane
Isiraeli wa Mulungu 500
1000
1500
2000 C.E.
[Mawu a M’munsi]
[Zithunzi]
Chifaniziro chachikulu (Dan. 2:31-45)
Zilombo zinayi zimene zinatuluka m’nyanja (Dan. 7:3-8, 17, 25)
Nkhosa yamphongo ndi mbuzi (Dan. 8)
Chilombo cha mitu 7 (Chiv. 13:1-10, 16-18)
Chilombo cha nyanga ziwiri chinalimbikitsa anthu kupanga chifaniziro cha chilombo (Chiv. 13:11-15)
[Mawu a Zithunzi]
Photo credits: Egypt and Rome: Photograph taken by courtesy of the British Museum; Medo-Persia: Musée du Louvre, Paris
-
-
Mafunso Ochokera kwa OwerengaNsanja ya Olonda—2012 | June 15
-
-
Mafunso Ochokera kwa Owerenga
Kodi ndi liti pamene ulamuliro wa Britain ndi America unakhala ulamuliro wamphamvu padziko lonse wa 7 wotchulidwa mu ulosi wa m’Baibulo?
▪ Chifaniziro chachikulu chimene Mfumu Nebukadinezara inalota sichiimira maulamuliro onse amphamvu apadzikoli. (Dan. 2:31-45) Chimangoimira maulamuliro asanu amene analamulira kuyambira nthawi ya Danieli, omwe analowerera kwambiri pa zochita za anthu a Mulungu.
Zimene Danieli anafotokoza pomasulira chifanizirocho zinasonyeza kuti ulamuliro wa Britain ndi America udzachokera mu ulamuliro wa Roma osati kuugonjetsa. Danieli anaona kuti miyendo ya chifanizirochi inali yachitsulo ndipo chitsulocho chinafika mpaka kumapazi ndi kuzala zakumapazi. (Koma chitsulo cha kumapazi ndi zala chinasakanizidwa ndi dongo.)a Zimenezi zinasonyeza kuti ulamuliro wa Britain ndi America udzachokera m’miyendo yachitsulo. Mbiri yakale ikusonyeza kuti izi n’zimene zinachitikadi. Dziko la Britain linali mu ulamuliro wa Roma ndipo linayamba kukhala lamphamvu chakumapeto kwa zaka za m’ma 1700. Kenako dziko la United States nalonso linakhala lamphamvu. Koma pa nthawiyi, ulamuliro wamphamvu padziko wa 7 wotchulidwa mu ulosi wa m’Baibulo unali usanayambe. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa pa nthawiyi mayiko a Britain ndi United States anali asanachitire limodzi zinthu zikuluzikulu. Koma anachitira limodzi zinthu pa nkhondo yoyamba ya padziko lonse.
Pa nthawi imeneyo, “ana a ufumu” ankagwira ntchito yawo makamaka m’dziko la United States. Likulu lawo linali m’dzikoli, ku Brooklyn ku New York. (Mat. 13:36-43) Koma Akhristu odzozedwa ankalalikiranso m’mayiko amene ankalamulidwa ndi ufumu wa Britain. Pa nkhondo yoyamba ya padziko lonse, dziko la Britain linachita mgwirizano wapadera ndi dziko la United States pomenyana ndi adani awo. Chifukwa cha nkhondoyo, kunali mzimu wokonda kwambiri dziko ku Britain ndi ku United States. Zimenezi zinachititsa kuti mayikowa ayambe kudana ndi anthu omwe anali mbali ya mbewu ya “mkazi” wa Mulungu. Analetsa mabuku awo ndipo anamanga anthu amene ankatsogolera pa ntchito yolalikira.—Chiv. 12:17.
Malinga ndi zimene ulosi wa m’Baibulo umanena, ulamuliro wamphamvu padziko lonse wa 7 unali usanakhazikitsidwe pamene dziko la Britain linayamba kukhala lamphamvu chakumapeto kwa zaka za m’ma 1700. M’malomwake, unakhazikitsidwa chakumayambiriro kwa tsiku la Ambuye.b
-