Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mrt nkhani 32
  • Samalani Kuti Musamapusitsike Ndi Nkhani Zabodza

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Samalani Kuti Musamapusitsike Ndi Nkhani Zabodza
  • Nkhani Zina
  • Nkhani Yofanana
  • Nkhani Yovomereza Ana Kugwiritsa Ntchito Intaneti—Gawo 1: Kodi Mwana Wanga Azigwiritsa Ntchito Intaneti?
    Mfundo Zothandiza Mabanja
  • Kodi Malo Ochezera a pa Intaneti Akusokoneza Moyo Wanga?
    Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Samalani ndi Nkhani Zabodza
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
  • Kodi Malo Ochezera a pa Intaneti Akusokoneza Mwana Wanu?—Mmene Baibulo Lingathandizire Makolo
    Nkhani Zina
Onani Zambiri
Nkhani Zina
mrt nkhani 32
Munthu akuganizira nkhani zochokera kosiyanasiyana.

Samalani Kuti Musamapusitsike Ndi Nkhani Zabodza

Masiku ano, n’zosavuta kupeza nkhani zosiyanasiyana kuposa kale, kuphatikizapo zimene zingakuthandizeni kuti mukhale otetezeka komanso athanzi. Koma mukamafufuza nkhani, muyenera kusamala ndi zinthu izi:

  • Nkhani zosocheretsa

  • Malipoti abodza

  • Mphekesera

Mwachitsanzo, pa nthawi ya mliri wa COVID-19, mlembi wamkulu wa bungwe la United Nations anachenjeza kuti nkhani zabodza zafalikira kwambiri. Iye anati: “Malangizo abodza okhudza mankhwala akufala kwambiri. Tikumamva nkhani zambiri zabodza pa TV komanso wailesi. Anthu akufalitsa nkhani zopanda umboni pa intaneti. Komanso anthu akulimbikitsa kwambiri tsankho chifukwa chosiyana chikhalidwe, mitundu ndi zinthu zina.”

Nkhani zabodza zakhala zikufalikira kuyambira kalekale. Komabe, Baibulo linaneneratu kuti m’masiku otsiriza ano, “anthu oipa ndi onyenga adzaipiraipirabe. Iwo azidzasocheretsa ena ndiponso azidzasocheretsedwa.” (2 Timoteyo 3:1, 13) Panopa intaneti yachititsa kuti tizitha kulandira komanso kufalitsa mosadziwa nkhani zabodza mwamsanga ndiponso mosavuta kuposa kale. Chifukwa cha zimenezi, maimelo, mameseji komanso nkhani zina zimene timalandira zimaoneka ngati zolondola koma zili zabodza.

Kodi mungatani kuti musamapusitsidwe ndi mphekesera komanso nkhani zosocheretsa? Tiyeni tione mfundo za m’Baibulo zimene zingakuthandizeni.

  • Munthu akuganizira zinthu zimene waona komanso kumva.

    Musamakhulupirire zinthu zonse zimene mwaona kapena kumva

    Zimene Baibulo limanena: “Munthu amene sadziwa zinthu amakhulupirira mawu alionse, koma wochenjera amaganizira za mmene akuyendera.”​—Miyambo 14:15.

    Ngati sitingasamale, tikhoza kupusitsidwa mosavuta. Mwachitsanzo, taganizirani za timavidiyo kapena zithunzi zokhala ndi mawu ofotokozera zomwe anthu akumatumizirana pamalo ochezera a pa intaneti. Nthawi zambiri anthu amachita zimenezi pongofuna kuseketsa anthu. Komabe, zithunzi ndi mavidiyowa zingasinthidwe kapenanso sizingasonyeze nkhani yonse. Nthawi zina, anthu amapanga mavidiyo a anthu ena akuchita kapena kunena zinthu zimene sanazichite kapena kuzinena n’komwe.

    “Nthawi zambiri, nkhani zimene anthu ochita kafukufuku amapeza pa intaneti zimakhala zoti zinasinthidwa kapena kupotozedwa komanso zoti sizikufotokoza nkhani yonse.”​—Axios Media.

    Dzifunseni kuti: ‘Kodi nkhaniyi ndi yoona kapena ndi yabodza?’

  • Galasi loonera zinthu zing’onozing’ono.

    Muzifufuza kumene nkhaniyo yachokera komanso zimene ikufotokoza

    Zimene Baibulo limanena: “Tsimikizirani zinthu zonse.”​—1 Atesalonika 5:21.

    Musanakhulupirire nkhani inayake kapena kuitumiza, ngakhale imene ndi yodziwika kapena imene yalengezedwa pa nyuzi, muzitsimikizira kaye kuti ndi yoona. Kodi mungachite bwanji zimenezi?

    Muzifufuza kuti mudziwe ngati nkhaniyo yachokera kwa anthu odalirika. Makampani kapena mabungwe ofalitsa nkhani akhoza kusintha nkhanizo chifukwa cha maganizo awo andale kapena pofuna kutsatsa malonda. Mukamva nkhani inayake yochokera kwa ofalitsa nkhani, muziyerekezera ndi zimene ena alemba pa nkhani yomweyo. Nthawi zina, anzanu angakutumizireni mameseji abodza kapena kutumiza zinthu pamalo ochezera a pa intaneti mosadziwa. Choncho musamakhulupirire nkhani iliyonse musanatsimikizire kumene yachokera.

    Muzitsimikiziranso kuti nkhaniyo ndi yatsopano komanso yoona. Muziona madeti, mfundo zotsimikizirika komanso umboni wamphamvu wosonyeza kuti nkhaniyo ndi yoona. Muzisamala kwambiri ngati nkhani ikufotokoza zinthu zovuta m’njira yosavuta kwambiri kapena ngati yalembedwa mokufikani pamtima kwambiri.

    “Zikuoneka kuti kutsimikizira nkhani n’kofunika kwambiri masiku ano mofanana ndi kusamba m’manja.”​—Sridhar Dharmapuri, yemwe amagwira ntchito yoona za zakudya zopatsa thanzi ku Bungwe la United Nations.

    Dzifunseni kuti: ‘Kodi nkhaniyi ikufotokoza maganizo a anthu ngati kuti ndi mfundo zoona kapena ikungofotokoza mbali imodzi?’

  • Ndandanda ya zinthu.

    Muzikhulupirira mfundo zimene n’zoona osati zongokusangalatsani

    Zimene Baibulo limanena: “Munthu wodalira mtima wake ndi wopusa.”​—Miyambo 28:26.

    Anthufe sitimakayikira nkhani zomwe zikugwirizana ndi zimene ifeyo tikufuna kukhulupirira. Nthawi zambiri, makampani a Intaneti amatumiza nkhani zogwirizana ndi zimene mumakonda komanso zimene mwakhala mukufufuza. Koma si nthawi zonse pamene nkhani zomwe timakonda kumva zimakhaladi zimene tikufunikira kumva.

    “N’zoona kuti anthufe timatha kuchita zinthu moganiza bwino. Koma nthawi zambiri zimene timakonda, kufuna komanso kuopa, zimachititsa kuti tiziona kuti nkhani inayake ndi yoona chifukwa choti ndi yogwirizana ndi zimene tikufuna kukhulupirira.”​—Peter Ditto, katswiri wa maphunziro amaganizo.

    Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndikukhulupirira nkhaniyi chifukwa choti ikugwirizana ndi zimene ndimakonda?’

  • Nkhani zabodza zikutayidwa m’bini.

    Musamafalitse nkhani zabodza

    Zimene Baibulo limanena: “Usafalitse nkhani yabodza.”​—Ekisodo 23:1.

    Muzikumbukira kuti nkhani zimene mungatumize kwa anthu ena zikhoza kukhudza mmene amaganizira komanso mmene amachitira zinthu. Ngakhale mutatumiza nkhani zabodza mosadziwa kapena mwangozi, zotsatirapo zake zingakhale zoipa.

    “Chofunika kwambiri n’chakuti muziima kaye n’kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndikudziwa kuti nkhaniyi ndi yoona moti ndikhoza kuitumiza kwa ena?’ Ngati aliyense atamachita zimenezi, nkhani zabodza zimene zimafalitsidwa pa intaneti zingachepe kwambiri.”​—Peter Adams, wachiwiri kwa woyang’anira bungwe la News Literacy Project.

    Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndikutumiza nkhaniyi chifukwa choti ndikudziwa kuti ndi yoona?’

Zoona zake zokhudza mphekesera

Shauna Bowes, yemwe ndi katswiri wa maphunziro amaganizo, anati: “Masiku ano, mphekesera zikukhudza kwambiri zimene anthu amaganiza komanso kuchita kuposa m’mbuyomu.” Mukufunika kudziwa mfundo zotsatirazi zokhudza mphekesera.

Kodi mphekesera ndi chiyani? Tikamanena za mphekesera munkhaniyi, tikutanthauza nkhani zabodza zimene anthu amafalitsa zakuti zigawenga kapena magulu achifwamba akufuna kuchita chiwembu choopsa.

N’chifukwa chiyani nkhani zimenezi n’zoopsa? Nkhani ngati zimenezi zingachititse anthu kuti asamakhulupire nkhani zoona komanso kuti azikana kutsatira malangizo odzitetezera ku matenda ndi mavuto ena. Zingachititsenso kuti anthu azidana komanso kuchita zachiwawa kapena kuchitira nkhanza gulu limene akuganiza kuti linakonza chiwembucho.

N’chifukwa chiyani nkhanizi n’zofala kwambiri? Buku lina (Encyclopaedia Britannica) limanena kuti nkhani zamphekesera zimafala kwambiri “pamene anthu ambiri akuda nkhawa kapena kuvutika” mwachitsanzo “pa nthawi ya nkhondo, mavuto azachuma, ngozi zam’chilengedwe ngati kusefukira kwa madzi kapena zivomerezi komanso pa nthawi ya miliri.” Pa nthawi ngati zimenezi, anthu amakhulupirira mphekesera chifukwa choti zimagwirizana ndi zimene amakhulupirira kapena zimawathandiza kumvetsa chifukwa chake zinthu zoipa zimachitika.

Kodi Baibulo lingakuthandizeni bwanji kuti musamapusitsidwe ndi mphekesera? Baibulo limapereka malangizo otithandiza kuti tisamade nkhawa kwambiri pa nthawi yovuta. Limafotokoza chifukwa chake timakumana ndi mavuto komanso mmene mavutowo adzathere. Kuti mudziwe zambiri, onerani vidiyo yakuti, N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzira Baibulo?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena