Lamlungu, August 31
Anthu ozindikira adzawamvetsetsa.—Dan. 12:10.
Tiyenera kupempha Mulungu kuti atithandize kumvetsa ulosi wa m’Baibulo. Taganizirani chitsanzo ichi: Tayerekezerani kuti mukuyenda m’dera lachilendo koma mnzanu amene mwayenda naye akudziwa bwino deralo. Akudziwa bwino pamene muli komanso kumene msewu uliwonse ukulowera. Mosakayikira mungasangalale kuti mnzanuyo anavomera kuti muyende naye. Mofanana ndi zimenezi, Yehova akudziwa bwino nthawi yomwe tikukhalamoyi komanso zimene zichitike kutsogoloku. Choncho kuti tizimvetsa maulosi a m’Baibulo, modzichepetsa tiyenera kupempha Yehova kuti atithandize. (Dan. 2:28; 2 Pet. 1:19, 20) Mofanana ndi kholo lililonse lachikondi, Yehova amafuna kuti ana ake akhale ndi tsogolo labwino. (Yer. 29:11) Koma mosiyana ndi makolo athu, Yehova akhoza kuneneratu zinthu zimene zidzachitike m’tsogolo molondola kwambiri. Iye analola kuti maulosi alembedwe m’Mawu ake ndi cholinga choti tizidziwa zinthu zofunika zisanachitike.—Yes. 46:10. w23.08 8 ¶3-4
Lolemba, September 1
Kuwala kwam’mawa kudzatifikira kuchokera kumwamba.—Luka 1:78.
Mulungu wapatsa Yesu mphamvu zothetsa mavuto onse a anthu. Pochita zozizwitsa, Yesu anasonyeza kuti ali ndi mphamvu zothetsera mavuto omwe sitingathe kuwathetsa patokha. Mwachitsanzo, iye ali ndi mphamvu yotipulumutsa ku zimene zinayambitsa mavuto a anthu, zomwe ndi uchimo umene tinatengera komanso zotsatirapo zake monga matenda ndi imfa. (Mat. 9:1-6; Aroma 5:12, 18, 19) Zozizwitsa zomwe anachita, zimasonyeza kuti iye angathe kuchiritsa “matenda amtundu uliwonse” ngakhalenso kuukitsa akufa. (Mat. 4:23; Yoh. 11:43, 44) Alinso ndi mphamvu yotha kuletsa mphepo zamkuntho komanso kugonjetsa mizimu yoipa. (Maliko 4:37-39; Luka 8:2) N’zolimbikitsa kudziwa kuti Yehova wapatsa Mwana wake mphamvu zochitira zimenezi. Sitikayikira kuti malonjezo omwe tikuyembekezera mu Ufumu wa Mulungu adzakwaniritsidwa. Zozizwitsa zimene Yesu anachita ali munthu padzikoli, zimatiphunzitsa kuti monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, adzachita zambiri m’tsogolomu. w23.04 3 ¶5-7
Lachiwiri, September 2
Mzimu umafufuza zinthu zonse, ngakhale zinthu zozama za Mulungu.—1 Akor. 2:10.
N’kutheka kuti abale ndi alongo ambiri amakonda kuyankha pamisonkhano moti nthawi zambiri mukakweza dzanja sakulozani. Choncho mungaganize kuti bola kungosiya kuyankha. Koma simuyenera kusiya kuyesetsa kuti muyankhe pamisonkhano. Mungachite bwino kumakonzekera ndemanga zingapo pamsonkhano uliwonse. Choncho ngati simunalozedwe kuti muyankhe kumayambiriro kwa phunziro, mungakhalebe ndi mwayi woyankha mkati mwa misonkhanoyo. Mukamakonzekera Phunziro la Nsanja ya Olonda, muziganizira mmene ndime iliyonse ikugwirizanirana ndi mutu wa nkhaniyo. Mukamachita zimenezo mungakhale ndi mfundo zoti muyankhe m’phunziro lonselo. Mungakonzekere kuti mukayankhe pa ndime zimene zikufotokoza mfundo zozama za choonadi, zomwe ndi zovuta kuzifotokoza. Chifukwa chiyani? Chifukwa mwina pangakhale anthu ochepa oimika manja kuti ayankhe pa mbali imeneyi. Koma bwanji ngati pamisonkhano ingapo mwaonabe kuti simunapatsidwe mwayi woyankha? Misonkhano isanayambe mungauze amene akuchititsa phunzirolo funso limene mukufuna kuyankha. w23.04 21-22 ¶9-10