Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g03 3/8 tsamba 31
  • “Galamukani! Inapulumutsa Moyo Wanga!”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Galamukani! Inapulumutsa Moyo Wanga!”
  • Galamukani!—2003
  • Nkhani Yofanana
  • Kugogomezera Kwambiri Baibulo!
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
  • Kwa Owerenga
    Galamukani!—2006
  • Kudziŵa Zizindikiro Zake ndi Kuchitapo Kanthu
    Galamukani!—1996
  • Zoŵaŵitsa Zimene Sizidzakhalakonso
    Galamukani!—1994
Onani Zambiri
Galamukani!—2003
g03 3/8 tsamba 31

“Galamukani! Inapulumutsa Moyo Wanga!”

Ofalitsa Galamukani! analandira kalata yoyamikira kuchokera ku Italy. Mbali ina ya kalatayo inati:

“Ndaŵerenga Galamukani! kwa zaka 40, ndipo ndimachita chidwi ndi mmene imafotokozera nkhani zosiyanasiyana zothandiza kwambiri. Tsiku lina posachedwa pompa, ndinali kuntchito ndipo m’mimba ndi m’chifuwa munayamba kundipweteka kwambiri. Ndinaganiza zopita ku nyumba, koma kupwetekako kutayambiranso, ndinakumbukira zinazake. Ndinakumbukira kuti nkhani ina mu Galamukani! inafotokoza zizindikiro za matenda a mtima.a Choncho, ndinapita kuchipatala. Ndili m’chipinda choyembekezera, mutu wanga unangoti pendekeku kumbali imodzi ndipo ndinakomoka. Ndinauzidwa zimenezi maŵa lake ndili m’chipinda cha odwala mwakayakaya.

“Ndili moyo lero chifukwa adokotala odziŵa bwino ntchito yawo anafulumira kundithandiza. Koma ndithokozenso magazini yanu, imene inandipatsa nzeru zoti ndipite ku chipatala. Galamukani! inapulumutsa moyo wanga!”

[Mawu a M’munsi]

a Onani Galamukani! yachingelezi ya December 8, 1996, tsamba 6.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena