Mutu 21
“Siali a Dziko Lapansi”
1. (a) Kodi nchiyani chimene Yesu anapempherera ophunzira ake usiku uja asanafe? (b) Kodi nchifukwa ninji kusakhala wa “mbali yadziko” kunali kofunika kwambiri?
PAUSIKUWO asanapachikidwe, Yesu anapempherera mwaphamphu ophunzira ake. Pomadziwa kuti akapsinjidwa kwakukulu ndi Satana, anati kwa Atate wake: “Sindipempha kuti muwachotse iwo m’dziko lapansi, koma kuti muwasunge iwo kuletsa woipayo. Siali adziko lapansi monga ine sindiri wadziko lapansi.” (Yoh. 17:15, 16) Kodi nchifukwa ninji kulekana ndi dziko kuli kofunika kwambiri? Chifukwa chakuti Satana ndiye wolamulira wake. Awo amene ali mbali yadziko ali pansi pa ulamuliro wake. (Yoh. 14:30, 1 Yoh. 5:19) Polingalira izi, kuli kofunika kwa Mkristu aliyense kuzindikiradi chimene chikutanthauzidwa ndi kusakhala “mbali yadziko.” Kodi ndimotani mmene zinaliri choncho ponena za Yesu?
2. Kodi Yesu sanali “wa mbali yadziko” m’njira zotani?
2 Ndithudi Yesu sanadzilekanitse ndi anthu ena. Kusakhala kwake “mbali yadziko” sikunatanthauze kusakonda ena. M’malo mwake, iye anamka kuchokera kumzinda ndi mzinda kukawauza mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu. Anachiritsa odwala, anapenyetsa akhungu, anaukitsa akufa, anapereka ngakhale moyo wa iyemwini m’malo mwa anthu. Koma sanakonde makhalidwe opanda umulungu ndi zochita zoipa za anthu amene anadzazidwa ndi mzimu wadziko. Anachenjeza motsutsana ndi zilakolako zachisembwere, njira ya moyo yokondetsa zinthu zakuthupi ndi kulakalaka kwadyera kofunafuna kutchuka kwaumwini. (Mat. 5:27, 28; 6:19-21; Luka 12:15-21; 20:46, 47) M’malo mwa kutsanzira njira ya moyo ya anthu otalikirana ndi Mulungu, Yesu anayenda m’njira za Yehova. (Yoh. 8:28, 29) Ponena za mikangano iri yonse yandale zadziko ya Roma ndi Ayuda, Yesu, ngakhale kuli kwakuti anali Myuda, sanachirikize mbali iriyonse.
“Ufumu Wanga Suli Mbali Yadziko Lino”
3. (a) Kodi ndimlandu wotani wonena za Yesu umene atsogoleri achipembedzo Achiyuda anamneneza kwa Pilato, ndipo chifukwa ninji? (b) Kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti Yesu analibe chikondwerero m’kukhala mfumu yaumunthu?
3 Komabe, atsogoleri achipembedzo a Ayuda, anaimba mlandu Yesu wa kusokoneza zinthu zamtunduwo. Anamchititsa kumangidwa ndi kupititsidwa kwa Pontiy Pilato, bwanamkubwa wa Roma. Chimene chinawavutitsadi maganizo chinali chakuti kuphunzitsa kwa Yesu kunavumbula chinyengo chawo. Koma kuti achititse bwanamkubwa kuchitapo kanthu, anapanga chinenezo chakuti: “Tinapeza munthu uyu ali kupandutsa anthu amtundu wathu, ndi kuwaletsa kupereka msonkho kwa Kaisara, nadzinenera kuti iye yekha ndiye Kristu mfumu.” (Luka 23:2) Chenicheni nchakuti chaka chimodzi izi zisanachitike pamene anthu anafuna kumpanga kukhala mfumu, Yesu anali atakana. (Yoh. 6:15) Iye anadziwa kuti adzakhala Mfumu yakumwamba ndi kuti nthawi yakuti iye akhale Mfumu inali isanakwane, ndipo adzaikidwa pampando wachifumu, osati mwa mchitidwe wa demokratiki kapena masankho, koma ndi Yehova Mulungu.
4. Kodi maumboni amavumbulanji ponena za kaimidwe ka maganizo ka Yesu pa “kukhoma msonkho kwa Kaisara”?
4 Ponena za kukhoma msonkho, masiku atatu okha Yesu asanamangidwe Afarisi anali atayesa kumchititsa kunena kanthu kena kaupandu pankhani iyi. Koma m’kuyankha funso lawo lokola, Yesu anali atayankha kuti: “Tandiwonetsani ine lupiya latheka [ndalama Yachiroma]. Chithunzithunzi ndi cholemba chake nchayani? Pamene iwo anati, “cha Kaisara,” iye anayankha: “Chifukwa chake perekani kwa Kaisara zake za Kaisara, ndi kwa Mulungu zake za Mulungu.”—Luka 20:20-25.
5. (a) Kodi ndiphunziro lotani limene Yesu anaphunzitsa ophunzira ake panthawi ya kumangidwa kwake? (b) Kodi ndimotani mmene Yesu analongosolera Pilato chifukwa cha zimene adachita?
5 Chimene chinachitika panthawi yeniyeniyo ya kumangidwa kwa Yesu chinasonyeza kuti iye sanali kusonkhezera chipanduko motsutsana ndi Roma, ndipo sanafune ophunzira ake kuti atero. Asilikali Achiroma limodzi ndi Ayuda atanyamula malupanga ndi nthungo anadza kudzagwira Yesu. (Yoh. 18:3, 12; Marko 14:43) Powona ichi, mtumwi Petro anasolola lupanga nakantha mmodzi wa amunawo, akumadula khutu lake lamanja. Koma Yesu anadzudzula Petro, akumati: “Tabweza lupanga lako m’chimakemo, pakuti onse akugwira lupanga adzawonongeka ndi lupanga.” (Mat. 26:51, 52) M’mawa mwake, pamaso pa Pilato, Yesu analongosola chifukwa cha chochita chakecho, akumati: “Ufumu wanga suli wadziko lino lapansi; ufumu wanga ukadakhala wadziko lino lapansi, anyamata anga akadalimbika nkhondo, kuti ndisaperekedwe kwa Ayuda; koma tsopano ufumu wanga suli wochokera konkuno.”—Yoh. 18:36.
6. Kodi nchiyani chimene chinali chotulukapo cha kuweruzidwa kumeneko?
6 Atatha kupenda umboni, Pilato analengeza kuti ‘panalibe maziko azinenezo’ zonenedwa motsutsana ndi Yesu. Komabe, iye anagonjera ku zifunsiro za kagulu ka chipoloweko ndipo anachititsa kuti Yesu apachikidwe.—Luka 23:13-15; Yoh. 19:12-16.
Ophunzira Atsatira Chitsogozo cha Mbuye
7. Kodi ndimotani mmene Akristu oyambirira anasonyezera kuti anapewa mzimu wadziko koma anakonda anthu?
7 Cholembedwa cha Chikristu choyambirira, ponse pawiri m’Baibulo ndi m’mabukhu ena a mbiri yakale, chimasonyeza zimene ophunzira a Yesu anazindikira chimene kusakhala a “mbali yadziko” kunafunikiritsa kwa iwo. Iwo anayesayesa kupewa mzimu wadziko. Chifukwa chakuti anakana zosangulutsa zachiwawa ndi zachisembwere zamasewera a zirombo za Roma ndi m’nyumba yamasewera, iwo anali kunyozedwa monga akuda fuko laumunthu. Komabe, m’malo mwa kukhala akuda anthu anzawo, iwo anadzigwiritsira ntchito iwo eni kuthandiza ena kupindula ndimakonzedwe achikondi a Mulungu achipulumutso.
8. (a) Chifukwa cha kusakhala a “mbali yadziko,” kodi nchiyani chimene ophunzira oyambirira amenewo anakumana nacho? (b) Koma kodi ndimotani mmene anawonera olamulira andale zadziko ndi kukhoma misonkho, ndipo chifukwa ninji?
8 Monga momwe analiri Mbuye wawo, iwonso anali mikhole yachizunzo chachikulu, kawirikawiri chochitidwa ndi akuluakulu aboma ouzidwa molakwa. (Yoh. 15:18-20) Koma pafupifupi mu 56 C.E. mtumwi Paulo analembera Akristu anzake mu Roma akumachirikiza uphungu umene Yesu anali atapereka. Paulo anawalimbikitsa kukhala “ogonjera ku maulamuliro aakulu,” olamulira a ndale zadziko, “pakuti palibe ulamuliro wina kusiyapo wochokera kwa Mulungu.” Osati kuti Yehova anakhazikitsa maboma adziko, koma iwo amalamulira mwa chilolezo chake. Paulo analongosola kuti iwo “amakhala m’malo awo aang’no mololedwa ndi Mulungu,” chifukwa chakuti Mulungu anawoneratu naneneratu dongosolo m’limene iwo akakhalira mu ulamuliro. Chifukwa chake “maulamuliro aakulu” amaphatikizapo “kakonzedwe ka Mulungu” kwa nthawi ino, kufikira Ufumu wa Mulungu mwini m’manja a Yesu Kristu utakhala boma lokha lolamulira dziko lapansi. Chotero Paulo analangiza Akristu kusonyeza ulemu woyenerera kwa olamulira adziko ndi kukhoma misonkho imene iwo angalamule.—Aroma 13:1-7; Tito 3:1, 2.
9. (a) Kodi nchiyani chimene sichiyenera kunyalanyazidwa pogonjera ku “maulamuliro aakulu”? (b) Kodi ndimotani mmene mbiri imasonyezera kuti Akristu oyambirira anatsatira chitsanzo cha Yesu mosamalitsa?
9 Komabe, Paulo sanawauze, kukhala ogonjera kotheratu mosawerengera Mulungu, Mawu a Mulungu ndi chikumbumtima chawo Chachikristu. Iwo anadziwa kuti Yesu anali atalambira Yehova yekha, kuti Yesu anakana kuti anthu ampange kukhala mfumu ndi kuti anali atauza Petro kubwezera lupanga lake. Mwachikumbumtima iwo anamamatira kuchitsogozo cha Mbuye wawo. Bukhu lotchedwa On the Road to Civilization—A World History (lolembedwa ndi Heckel ndi Sigman, tsamba 237, 238) limasimba kuti: “Akristu anakana kukhala ndi mbali m’ntchito zina za nzika za Roma. Akristuwo . . . anakulingalira kuswa chikhulupiriro chawo kulowa m’mautumiki ankhondo. Iwo sakanalola kukhala ndi malo antchito m’ndale zadziko. Sakanalola kulambira mfumu.”
10. (a) Kodi nchifukwa ninji Akristu m’Yerusalemu anachita monga momwe anachitiramo mu 66 C.E.? (b) Kodi zimenezo zimaperekera chitsanzo chabwino m’njira yotani?
10 Ponena za mikangano yandale zadziko ndi nkhondo za m’tsiku lawo, ophunzira a Yesu anasunga uchete weniweni. M’chaka cha 66 C.E. Ayuda a m’chigawo cha Roma cha Yudeya anapandukira Kaisara. Magulu ankhondo Achiroma mwamsanga anazinga Yerusalemu. Kodi nchiyani chimene Akristu mu mzindawo anachita? Anakumbukira uphungu wa Yesu wa kukhala achete ndi kuchoka pakati pa asilikali ankhondo ochita nkhondowo. Pamene magulu ankhondo anachoka kwakanthawi, Akristu anagwiritsira ntchito mwayiwo nathawa kuwoloka Mtsinje wa Yordano kumka kuchigawo cha mapiri a Pela. (Luka 21:20-24) Mu mkhalidwe wawo wauchete anatumikira monga chitsanzo chokhulupirika kaamba ka Akristu amtsogolo.
Uchete w̃achikristu m’Nthawi Yamapeto
11. (a) Kodi Mboni za Yehova zikutanganitsidwa m’ntchito yotani, ndipo chifukwa ninji? (b) Kodi izo ziri zauchete ponena za chiyani?
11 Kodi cholembedwa cha m’mbiri chimasonyeza kuti kagulu kalikonse mu “nthawi yamapeto” ino kuyambira 1914 C.E. kalondola njira yauchete Wachikristu motsanzira Akristu oyambirira amenewo? Inde, Mboni za Yehova zatero. M’dziko lapansi zatanganitsidwa kulalikira kuti Ufumu wa Mulungu ndiyo njira yokha mwa imene mtendere, kulemerera ndi chimwemwe chosatha zingatheketsedwere kaamba ka okonda chilungamo m’dziko lonse lapansi. (Mat. 24:14) Koma ponena za nkhondo pakati pamitundu, iwo asunga uchete wotheratu.
12. (a) Kodi ndimotani mmene uchete wa Mboni umasiyanirana ndi zochita za atsogoleri achipembedzo? (b) Kodi uchete wandale zadziko umaphatikizapo chiyani kwa Mboni za Yehova?
12 Mosiyana kotheratu, atsogoleri achipembedzo a Dziko Lachikristu ali ophatikizidwa kwambiri m’zochitika zandale zadziko zadzikoli. M’maiko ena iwo amachita mkupiti wochirikiza kapena kutsutsa oyembekezera kusankhidwa. Ena a atsogoleri achipembedzo enieniwo amakhala ndi malo antchito andale zadziko. Ena amatsendereza kwambiri andale zadziko kuti ayanje maprogramu amene atsogoleri achipembedzo avomereza. Kumalo ena atsogoleri achipembedzo “osakonda kusintha” ali ogwirizana athithithi a amuna okhala mu ulamuliro pamene ansembe ndi aminisitala “okonda kusintha” angakhale akuchirikiza magulu a zigawenga zofunafuna kuwagubuduza. Komabe, Mboni za Yehova sizimalowerera m’ndale zadziko, mosasamala kanthu za dziko m’limene zikukhala. Izo sizimadodometsa zimene ena achita ponena za kugwirizana ndi chipani cha ndale zadziko, kulimbirana mpando kapena kuchita voti m’masankho. Koma, popeza Yesu ananena kuti ophunzira ake sakakhala “ambali yadziko,” Mboni za Yehova sizimatenga mbali iriyonse m’machitachita a ndale zadziko.
13. Ponena za kukhala kwawo ndi phande m’nkhondo, kodi maumboni akusonyeza kuti nchiyani chimene chakhala lingaliro la Mboni za Yehova?
13 Monga momwe Yesu ananeneratu, mkati mwa “nthawi yamapeto” mitundu mobwerezabwereza yachita nkhondo, ndipo ngakhale magulu mkati mwa mitundu anyamula zida kumenyana lina ndi linzake. (Mat. 24:3, 6, 7) Pokumana ndi zonsezi, kodi ndimalo ati amene Mboni za Yehova zatenga? Uchete wawo m’mikangano imeneyi ngwodziwika bwino mbali zonse zadziko. Mogwirizana ndi lingaliro limene Yesu Kristu ndipo pambuyo pake losonyezedwa ndi ophunzira ake oyambirira, Nsanja ya Olonda m’kope lake la November 1, 1939, (Chingelezi), inati: “Onse amene ali kumbali ya Ambuye adzakhala achete ku mitundu yochita nkhondo, ndipo adzakhala ochirikiza kotheratu ndi kwathunthu Teokrati wamkulu [Yehova] ndi Mfumu yake [Yesu Kristu].” Zenizeni zikusonyeza kuti Mboni za Yehova m’mitundu yonse pansi pamikhalidwe iriyonse zikupitirizabe kukhala ndi lingaliro iri. Sizinalole ndale zadziko zogawanitsa zadziko ndi nkhondo kuswa ubale wawo wa m’mitundu yonse monga olambira a Yehova.—Yes. 2:3, 4; Yerekezerani ndi 2 Akorinto 10:3, 4.
14. (a) Chifukwa cha kaimidwe kawo kauchete, kodi nchiyaninso chimene Mboni zakana kuchita? (b) Kodi ndimotani mmene zimalongosolera chifukwa chochitira izi?
14 Kupenda maumboni a m’mbiri kumasonyeza kuti sikokha kuti Mboni za Yehova zinakana kuvala mayunifomu ankhondo ndi kunyamula zida zankhondo koma, mkati mwa zaka makumi asanu kapena kuposa zapita, zakananso kuchita mautumiki osakhala ankhondo kapena kuvomereza magawo ena antchito monga olowa m’malo mwa utumiki wankhondo. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti izo zaphunzira zofunika za Mulungu ndiyeno zapanga chosankha cha munthu mwini chogwirizana ndi chikumbumtima. Palibe munthu amaziuza chimene ziyenera kuchita. Ndiponso izo sizimadodometsa zimene ena asankha kuchita. Koma pamene izo zifunsidwa kulongosola lingaliro lawo, Mboni za Yehova zalongosola kuti, monga anthu amene adzipereka iwo eni kwa Mulungu m’kudzipatulira, ziri ndi thayo la kugwiritsira ntchito matupi awo mu utumiki wake ndipo tsopano sizingakhoze kuwapereka kwa ambuye a dziko lapansi amene akuchita motsutsana ndi chifuno cha Mulungu.—Aroma 6:12-14; 12:1, 2; Mika 4:3.
15. (a) Chifukwa cha kusunga kulekana kwawo ndi dziko, kodi Mboni za Yehova zakumana nchiyani? (b) Ngakhale pamene zinaikidwa m’ndende, kodi ndimotani mmene malamulo a makhalidwe abwino Achikristu azitsogolerera?
15 Chotulukapo chakhala monga momwe Yesu ananenera kuti: “Popeza simuli adziko lapansi . . . dziko likudani.” (Yoh. 15:19) Ambiri a Mboni za Yehova aikidwa m’ndende chifukwa chakuti sakanaswa uchete wawo Wachikristu. Ena achitiridwa mwankhalwe, ngakhale mpaka kufikira imfa. Ena apitirizabe kusonyeza uchete wawo mkati mwa zaka za kubindikiritsidwa. Bukhu lotchedwa Values and Violence in Auschwitz (lolembedwa ndi Anna Pawelczynska, tsamba 89) likusimba kuti: “Aliyense anadziwa kuti palibe Mboni ya Yehova [mu msasa wachibalo] ikamvera lamulo lotsutsana ndi chikhulupiriro chake chachipembedzo ndi zikhutiro kapena machitachita aliwonse olunjikitsidwa kutsutsana ndi munthu wina, ngakhale ngati munthuyo anali wambanda ndi mdindo wa SS. Kumbali ina, iye akanachita ntchito ina iriyonse, ngakhale yonyansa koposa, kumlingo umene maluso ake onse akanamlola, ngati kwa iye inali yauchete mwa makhalidwe.”
16. (a) Kodi mitundu yonse ikuguba kumka kuti, ndipo chotero kodi nchiyani chimene Mboni za Yehova mosamala zikupewa? (b) Pamenepa, kodi nchifukwa ninji kulekana ndi dziko iri nkhani yofunika kwambiri motero?
16 Mboni za Yehova zimazindikira kuti mitundu yonse iri kuguba kumka ku “nkhondo yatsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse” pa Armagedo. Monga anthu ogwirizana, atumiki a Yehova atenga kaimidwe kawo koyanja Ufumu Wake Waumesiya. Chotero zimachita mosamala kupewa kuti zisalole kulowetsedwa mu mkhalidwe wotsutsana ndi Ufumu umenewo. (Chiv. 16:14, 16; 19:11-21) Zimazindikira kukhala ofunika kwambiri kwa mawu a Yesu akuti otsatira ake owona sali “mbali yadziko.” Zimadziwa kuti dongosolo loipa lino lidzachoka posachedwa, ndi kuti awo okha ochita chifuniro cha Mulungu mowona mtima adzakhala kosatha.—1 Yoh. 2:15, 17.
Makambitsirano Openda
● Kodi ndimotani mmene Yesu anasonyezera chimene chikuphatikizidwa m’kusakhala wa “mbali yadziko”?
● Kodi nchiyani chimene chimasonyeza mkhalidwe wa Akristu oyambirira kulinga ku (1) mzimu wadziko? (2) olamulira adziko ndi kukhoma misonkho? (3) utumiki wankhondo?
● Kodi ndim’njira zotani m’zimene Mboni za Yehova m’nthawi zamakono zaperekera umboni wa uchete wawo Wachikristu?