Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • sp tsamba 30-31
  • Dzikoli Lidzakhala Paradaiso

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Dzikoli Lidzakhala Paradaiso
  • Kodi Mizimu ya Akufa Ilipodi?
  • Nkhani Yofanana
  • Moyo Wabwino Kwambiri Ulonjezedwa
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Mabwenzi a Mulungu Adzakhala M’paradaiso
    Mungathe Kukhala Bwenzi la Mulungu!
  • Patsogolopa—Nthaŵi Yabwino Koposa!
    Galamukani!—1995
  • Mutha Kupindula ndi Chipembedzo Choona Kosatha!
    Njira ya ku Moyo Wosatha—Kodi Mwaipeza?
Onani Zambiri
Kodi Mizimu ya Akufa Ilipodi?
sp tsamba 30-31

Dzikoli Lidzakhala Paradaiso

Anthu a mitundu yosiyanasiyana akudya limodzi chakudya m’Paradaiso

Yehova adzathetsa mavuto onse amene Satana anayambitsa ndipo anasankha Yesu kuti akhale Mfumu ya dziko lonse. Yesu akadzayamba kulamulira dzikoli, lidzakhala paradaiso.​—Danieli 7:13, 14; Luka 23:43.

Yehova anatilonjeza zinthu zotsatirazi:

  • PADZAKHALA CHAKUDYA CHAMBIRI: “Dziko lapansi lidzapereka zipatso zake. Mulungu, ndithu Mulungu wathu, adzatidalitsa.” “Padziko lapansi padzakhala tirigu wambiri. Pamwamba pa mapiri padzakhala tirigu wochuluka.”​—Salimo 67:6; 72:16.

  • SIPADZAKHALANSO NKHONDO: “Bwerani anthu inu, onani ntchito za Yehova, onani mmene wakhazikitsira zinthu zodabwitsa padziko lapansi. Akuletsa nkhondo mpaka kumalekezero a dziko lapansi.”​—Salimo 46:8, 9.

  • SIPADZAKHALANSO ANTHU OIPA: “Pakuti ochita zoipa adzaphedwa. Koma oyembekezera Yehova ndi amene adzalandire dziko lapansi. Patsala kanthawi kochepa, woipa sadzakhalakonso. Udzayang’ana pamene anali kukhala, ndipo sadzapezekapo.”​—Salimo 37:9, 10.

  • Moyo m’Paradaiso

    SIPADZAKHALANSO MATENDA, KUVUTIKA KOMANSO IMFA: “Pa nthawi imeneyo, maso a anthu akhungu adzatsegulidwa, ndipo makutu a anthu ogontha adzayamba kumva. Pa nthawiyo, munthu wolumala adzakwera phiri ngati mmene imachitira mbawala yamphongo. Lilime la munthu wosalankhula lidzafuula mokondwa.”​—Yesaya 35:5, 6.

    “Mulunguyo adzakhala nawo. Iye adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”​—Chivumbulutso 21:3, 4.

Yehova amanena zoona zokhazokha koma Satana ndi ziwanda ndi abodza. Yehova amachita chilichonse chimene walonjeza. (Luka 1:36, 37) Iye amakukondani ndipo akufuna kuti mudzakhale m’Paradaiso. A Mboni za Yehova angakuthandizeni kudziwa zinthu zabwino zimene zili m’Mawu a Mulungu. Mukamatsatira mfundo za m’Baibulo simudzanamizidwa, simudzaopa mizimu ndipo mudzakhala ozindikira. M’tsogolomu, tonse sitidzakhalanso akapolo a uchimo ndi imfa. Paja Yesu ananena kuti: “Mudzadziwa choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.”​—Yohane 8:32.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena