Mawu Omaliza
SITIKHOZA kufotokoza zonse ponena za zikhulupiriro za chipembedzo za Mboni za Yehova m’brosha lino. M’malo mwake, tangolongosola zikhulupiriro zina za Mboni ndi kusonyeza bwino lomwe mkhalidwe wa banja umene ukuyambukira mwana wanu wa sukulu ngati kholo limodzi kapena onse aŵiri ali Mboni.
Mboni za Yehova zimaika chisamaliro chachikulu pa kakulidwe kauzimu ka ana awo. Ndipo zili ndi chidaliro chakuti zimenezi zimachirikiza kukula kwa ana awo m’zinthu zina. Zikhulupiriro zawo ndi malamulo omwe zimatsatira zimachititsa moyo wawo kukhala ndi chifuno ndi kuwathandiza kuchita ndi mavuto a tsiku ndi tsiku. Ndiponso, zikhulupiriro ndi malamulo amenewo zimawasonkhezera kukhala ana a sukulu akhama ndi nzika zabwino kwa moyo wawo wonse.
Mboni zimaona moyo moona mtima, chotero zimaika chisamaliro chachikulu pa maphunziro. Chifukwa chake, zimafuna kugwira ntchito limodzi nanu malinga ndi kukhoza kwawo. Komabe izo zidzapitirizabe kulimbikitsa ana awo, m’nyumba zawo ndi pamalo awo olambirira, kotero kuti zichite mbali yawo m’ntchito yogwirizana ndi yopindulitsa imeneyi.