Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • gf phunziro 5 tsamba 8-9
  • Mabwenzi a Mulungu Adzakhala M’paradaiso

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mabwenzi a Mulungu Adzakhala M’paradaiso
  • Mungathe Kukhala Bwenzi la Mulungu!
  • Nkhani Yofanana
  • Moyo Wabwino Kwambiri Ulonjezedwa
    Nsanja ya Olonda—1995
  • “Iwe Udzakhala ndi Ine m’Paradaiso”
    Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
  • Paradaiso
    Galamukani!—2013
  • “Tidzaonana M’Paradaiso”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2018
Onani Zambiri
Mungathe Kukhala Bwenzi la Mulungu!
gf phunziro 5 tsamba 8-9

PHUNZIRO 5

Mabwenzi a Mulungu Adzakhala M’paradaiso

Paradaiso sadzakhala ngati dziko limene tikukhalamoli. Sichinali chifuniro cha Mulungu kuti dziko lapansi likhale ndi mavuto ochuluka, chisoni, zopweteka ndiponso kuvutika. M’tsogolo muno, Mulungu adzasandutsa dziko lapansi kukhala paradaiso. Kodi Paradaiso adzakhala wotani? Tiyeni tione zimene Baibulo limanena:

Anthu akuchita phwando m’paradaiso

Anthu abwino. Paradaiso adzakhala mudzi wa mabwenzi a Mulungu. Adzachitirana zinthu zabwino zokhazokha. Adzakhala ndi moyo motsatira njira za Mulungu zolungama.—Miyambo 2:21.

Chakudya chamwana alirenji. M’Paradaisomo njala siidzakhalamo. Baibulo limati: “M’dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka [kapena kuti chakudya chambiri].”—Salmo 72:16.

M’paradaiso anthu akumanga nyumba, ena akuika pamodzi zakudya ndipo mayi wanyamula mwana wake

Nyumba zabwino ndi ntchito yosangalatsa. M’dziko lapansi la Paradaiso, banja lililonse lidzakhala ndi nyumba yawoyawo. Aliyense adzagwira ntchito yom’patsa chisangalalo chenicheni.—Yesaya 65:21-23.

Mtendere padziko lonse. Anthu sazidzamenyananso ndi kufa m’nkhondo ayi. Mawu a Mulungu amati: “[Mulungu] aletsa nkhondo.”—Salmo 46:8, 9.

Thanzi labwino. Baibulo limalonjeza kuti: “Wokhalamo [m’Paradaiso] sadzanena, Ine ndidwala.” (Yesaya 33:24) Ndiponso, simudzapezeka wopunduka kapena wakhungu kapena wogontha kapena wosalankhula.—Yesaya 35:5, 6.

Kutha kwa zopweteka, chisoni, ndi imfa. Mawu a Mulungu amati: “Sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa; zoyambazo zapita.”—Chivumbulutso 21:4.

Anthu oipa adzachotsedwa. Yehova walonjeza kuti: “Oipa adzalikhidwa m’dziko, achiwembu adzazulidwamo.”—Miyambo 2:22.

Anthu adzakondana ndi kulemekezana wina ndi mnzake. Sipadzakhalanso kusoŵa chilungamo, kuponderezana, umbombo, ndi chidani. Anthu adzakhala ogwirizana ndipo adzakhala ndi moyo wotsatira njira za Mulungu zolungama.—Yesaya 26:9.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena