Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • scl tsamba 76-79
  • Makhalidwe Olakwika

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Makhalidwe Olakwika
  • Malemba Othandiza pa Moyo wa Chikhristu
Malemba Othandiza pa Moyo wa Chikhristu
scl tsamba 76-79

Makhalidwe Olakwika

Kodi Akhristu ayenera kupewa makhalidwe olakwika ati?

Mkwiyo

Sl 37:8, 9; Miy 29:22; Akl 3:8

Onaninso Miy 14:17; 15:18

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Ge 37:18, 19, 23, 24, 31-35​—Azibale ake a Yosefe anamuukira, kumugulitsa ngati kapolo komanso ananamiza Yakobo kuti mwana wake wokondedwa Yosefe wamwalira

    • Ge 49:5-7​—Simiyoni ndi Levi anaweruzidwa chifukwa chakuti atakwiya, anachita zinthu zoipa kwambiri

    • 1Sa 20:30-34​—Sauli atakwiya ananyoza mwana wake Yonatani ndipo ankafuna kumupha

    • 1Sa 25:14-17​—Nabala analalatira anthu amene anatumizidwa ndi Davide, ndipo zimenezi zinaika pangozi moyo wa anthu onse am’banja lake

Kukonda mikangano

Afi 2:3; Yak 3:14-16

Mzimu wamantha

2Ti 1:7; Chv 21:8

Nkhanza

De 15:7, 8; Mt 19:8; 1Yo 3:17

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Ge 42:21-24​—Azichimwene a Yosefe anadzimvera chisoni chifukwa cha nkhanza zomwe anachitira Yosefe

    • Mko 3:1-6​—Yesu anakhumudwa kwambiri chifukwa cha nkhanza zimene Afarisi ankachitira anthu

Kupanda ulemu

Onaninso “Kupanda Ulemu”

Kudzikudza

Ga 5:26; Afi 2:3

Onaninso Miy 3:7; 26:12; Aro 12:16

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • 2Sa 15:1-6​—Abisalomu anali wodzikuza ndipo ankakopa mitima ya anthu n’cholinga choti asamamvere Mfumu Davide bambo ake

    • Da 4:29-32​—Mfumu Nebukadinezara anali wonyada ndipo mapeto ake Yehova anamulanga

Nsanje; kusirira mwansanje

Aro 13:9; 1Pe 2:1

Onaninso Aga 5:26; Tit 3:3

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Ge 26:12-15​—Yehova anadalitsa Isaki chifukwa chogwira ntchito mwakhama koma Afilisiti anayamba kumuchitira nsanje

    • 1Mf 21:1-19​—Ahabu Mfumu yoipa anasirira munda wa mpesa wa Naboti ndipo mapeto ake Naboti anaimbidwa mlandu wabodza n’kuphedwa

Kuopa anthu

Sl 118:6; Miy 29:25; Mt 10:28

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Nu 13:25-33​—Pa Aisiraeli 12 omwe anatumidwa kukazonda dziko la Kanani, 10 mwa iwo anachita mantha ndipo anachititsa kuti anthu ena onse achitenso mantha

    • Mt 26:69-75​—Mtumwi Petulo anakana Yesu katatu chifukwa choopa anthu

Dyera

Onani “Dyera”

Chidani

Miy 10:12; Tit 3:3; 1Yo 4:20

Onaninso Nu 35:19-21; Mt 5:43, 44

Chinyengo

Onani “Chinyengo”

Nsanje

Onani “Nsanje”

Ulesi

Miy 6:6-11; Mla 10:18; Aro 12:11

Onaninso Miy 10:26; 19:15; 26:13

Kukonda ndalama; zinthu zakuthupi

Mt 6:24; 1Ti 6:10; Ahe 13:5

Onaninso 1Yo 2:15, 16

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Yob 31:24-28​—Ngakhale kuti anali munthu wolemera, Yobu anapewa msampha wokonda chuma

    • Mko 10:17-27​—Mwamuna wina wachuma ankakonda kwambiri chuma chake moti anakana kutsatira Yesu

Kupsa mtima kwambiri

1Sa 30:6; Aef 4:31; Akl 3:19

Onaninso Yak 3:14

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Ob 10-14​—Mulungu analanga Aedomu chifukwa choti anapsera mtima kwambiri abale awo Aisiraeli

Kudzikuza

Onani “Kudzikuza”

Kunyada; kudzikuza

Onani “Kunyada”

Wokonda mikangano

Miy 26:20; 1Ti 3:2, 3; Tit 3:2

Onaninso Miy 15:18; 17:14; 27:15; Yak 3:17, 18

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Ge 13:5-9​—Mkangano unabuka pakati pa abusa a Abulahamu ndi abusa a Loti koma Abulahamu anakhazikitsa mtendere

    • Owe 8:1-3​—Amuna a ku Efuraimu ankafuna kuyambitsa mkangano ndi Woweruza Gidiyoni koma modzichepetsa, iye anakhazikitsa mtendere

Kupanduka

1Sa 15:23; Yuda 4, 8, 10, 11

Onaninso De 21:18-21; Sl 78:7, 8; Tit 1:10

Kudziona wolungama

Mla 7:16; Mt 7:1-5; Aro 14:4, 10-13

Onaninso Yes 65:5; Lu 6:37

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Mt 12:1-7​—Yesu anaulula kuti Afarisi anali ndi mtima wodziona kuti ndi olungama

    • Lu 18:9-14​—Yesu ananena fanizo losonyeza kuti Mulungu sasangalala ndi anthu odziona kuti ndi olungama

Kuuma mtima

Yer 13:10

Onaninso Yer 7:23-27; Zek 7:11, 12

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • 2Mb 36:11-17​—Zedekiya anali mfumu youma mtima ndipo zimenezi zinachititsa kuti anthu amtundu wake alangidwe ndi Mulungu

    • Mac 19:8, 9​—Mtumwi Paulo anasiya kulalikira kwa anthu omwe anaumitsa mitima yawo kuti asamvetsere uthenga wa Ufumu

Kupanda nzeru

Mko 7:21-23; Aef 5:17

Onaninso 1Pe 2:15

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • 1Sa 8:10-20​—Aisiraeli anakana kumvera mneneri Samueli atawauza kuti si nzeru kudzisankhira mfumu

    • 1Sa 25:2-13, 34​—Nabala akanaphetsa anthu a m’banja lake onse chifukwa chokana kumvetsera pempho la Davide

Kukayikira ena kapena kuwaganizira zolakwika

Yob 1:9-11; 1Ti 6:4

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • 1Sa 18:6-9; 20:30-34​—Mfumu Sauli ankaganiza kuti Davide ndi wosakhulupirika ndipo ankafuna kuti Yonatani azimutsutsa

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena