11 MOSE
“Pita kwa Farao”
MOSE anali atasintha kwambiri. Panali patadutsa zaka zambiri chichokereni ku Iguputo ndipo n’kutheka kuti sankaganizirakonso kuti Yehova angadzamugwiritse ntchito kupulumutsa Aisiraeli ku ukapolo. Pa nthawiyi n’kuti ali ndi zaka 80 ndipo anali ndi mkazi komanso ana awiri. Anaphunzira kudzichepetsa pa zaka 40 zomwe ankaweta nkhosa za apongozi ake aamuna m’dera lotentha la ku Midiyani.
Yehova anaona mmene Mose anasinthira. Tsiku lina, m’munsi mwa phiri la Horebe, (Sinai) Mulungu anachititsa chitsamba chaminga kuyaka koma osanyeka. Mose atayandikira, Yehova anayamba kulankhula naye kuchokera pamotopo pogwiritsa ntchito mngelo wamphamvu. Iye anauza Mose kuti abwererenso ku Iguputo kuti akapulumutse anthu ake. Pofuna kumulimbikitsa, anamuuza mbali ina ya tanthauzo la dzina lake lakuti Yehova. Anamuuza kuti: “Ndidzakhala Amene Ndidzafune Kukhala.” Choncho, Yehova ankayembekezeka kukhala Mpulumutsi wa anthu ake omwe ankaponderezedwa. Iye anali wokonzekanso kuchita chilichonse chofunika kuti awapulumutse ndi kuwachititsa kukhala mtundu wamphamvu.
Mose ankazengereza, ankadziona kuti ndi wosayenerera komanso sangakwanitse kukalankhula pamaso pa Farao. Yehova anamuthandiza kuona zinthu moyenera ndipo analimbitsa chikhulupiriro chake pochita zodabwitsa. Kwa nthawi yoyamba, timawerenga m’Baibulo kuti Yehova anapatsa Mose mphamvu zochitira zodabwitsa. Komanso anamupatsa mchimwene wake Aroni kuti azimuthandiza ndi kulankhula m’malo mwake. Mose anavomera koma monyinyirika. Apa tsopano analola kuti Mulungu amudzoze kuti akapulumutse anthu ake.—Aheb. 11:26.
Atabwerera ku Iguputo, Mose ndi Aroni anakakumana ndi Farao. Koma iye anakwiya kwambiri ndipo m’malo molola kuti Aisiraeli azipita, analamula kuti awawonjezere ntchito yambiri. Kenako Yehova anauza Mose kuti apitenso kwa Farao kukamuuza zoti awagwetsera mliri. Mliriwo unagwadi ndipo madzi a mtsinje wa Nailo anasanduka magazi. Komabe Farao sanasinthe maganizo. Yehova ankatumiza Mose kwa Farao mobwerezabwereza kukamuuza za mliri wotsatira. Koma mfumu yonyadayo siinamvere. Kuyambira ndi mliri wanambala 4, Yehova ankateteza anthu ake ndipo Aiguputo okha ndi omwe ankavutika ndi miliriyi.
Mliri uliwonse unkasonyeza kuti milungu ya Aiguputo ndi yopanda mphamvu, chifukwa inkalephera kuimitsa miliriyi. Ndipo palibe chomwe Farao ndi ansembe ake ochita zamatsenga akanachita. Ngakhale zinali choncho, Farao anakanitsitsa kuti Aisiraeli apite. Mliri wanambala 9 unachititsa kuti ku Iguputo kugwe mdima wandiweyani, koma m’nyumba za Aisiraeli munkawala. Poyamba, Farao anavomera kuti Aisiraeli azipita, koma kenako anasinthanso maganizo ndipo anaopseza Mose kuti akangoyerekeza kupitanso kwa Farao adzamupha.
Mose ankapita mobwerezabwereza kwa Farao kukamuuza uthenga wa Yehova, ngakhale kuti zinkakwiyitsa mfumuyi
Komabe Yehova anauza Mose kuti apitenso kwa Farao ndipo Moseyo anapitadi. Kenako kunagwa mliri womaliza. Ana onse aamuna oyamba kubadwa, komanso a ziweto za Aiguputo anaphedwa. Nayenso mwana wamwamuna wa Farao anafa. Farao anachititsidwa manyazi ndipo anaitanitsa Mose kuti atenge Aisiraeli. Anapemphanso Mose kuti amudalitse. Pamapeto pake, Aisiraeli anamasulidwa patatha ndendende zaka 430 kuchokera pomwe Abulahamu analowa m’Dziko Lolonjezedwa kwa nthawi yoyamba. Aisiraeli anamasuka ku ukapolo ndipo ananyamuka limodzi ndi “gulu la anthu a mitundu yosiyanasiyana.” N’kutheka kuti ambiri mwa iwo anali Aiguputo. Kenako Farao anasinthanso maganizo. Anasonkhanitsa gulu lalikulu la asilikali ake n’kuyamba kutsatira Aisiraeli.
Mose ndi Aisiraeli anafika m’mbali mwa Nyanja Yofiira ndipo zinaoneka ngati alibe kolowera. Aisiraeli anachita mantha kwambiri ndipo anapemphera kwa Yehova kuti awathandize. Yehova anawayankha ndipo anachita zinthu zodabwitsa kwambiri. Iye anagawanitsa madzi a Nyanja Yofiira moti Aisiraeli anawoloka panthaka youma. Farao ataona kuti Aisiraeli akupita, anatsogolera asilikali ake n’kuyamba kuwathamangira. Koma Aisiraeli atafika tsidya lina, Yehova anachititsa madzi a nyanjayo kubwereranso n’kumiza Aiguputo aja. Gulu la asilikali amphamvu kwambiri padziko lonse, linathera pomwepo.
Mose sanaiwale zomwe zinachitikazi ndipo zinalimbitsa kwambiri chikhulupiriro chake. Kwa zaka 40 zotsatira mpaka pomwe anamwalira ali ndi zaka 120, iye anatsogolera anthu a Mulungu mwachikondi ndipo ndi chitsanzo chabwino pa nkhani ya kukhulupirika, chikondi komanso kulimba mtima.
Werengani nkhaniyi m’Baibulo:
Funso lokambirana:
Kodi Mose anasonyeza kulimba mtima m’njira ziti pa nthawi iyi ya moyo wake?
Zoti Mufufuze
1. Farao amene ankalamulira pa nthawiyi sadziwika dzina lake ndipo ku Iguputo sikunapezeke zolemba za mbiri yakale zokhudza ulendo wa Aisiraeli. Ndiye tili ndi zifukwa zotani zotichititsa kukhulupirira kuti nkhaniyi inachitikadi? (g04 4/8 23 ¶3–24 ¶2)
2. N’chifukwa chiyani anthu ankaopa kwambiri Farao? (w14 4/15 8 ¶1) A
PRISMA ARCHIVO/Alamy Stock Photo
Chithunzi A: Chithunzi chapakhoma chakale cha Farao
3. Kodi Miliri 10 inasonyeza bwanji kuti milungu ya ku Iguputo inali yopanda mphamvu? (it “Milungu Komanso Milungu Yaikazi” ¶24-26-wcgr)
4. N’chiyani chimatsimikizira kuti Yehova anatsegula msewu waukulu pa Nyanja Yofiira, nanga angakhale kuti ndi Aisiraeli angati omwe anawolokera pamsewu umenewu? (it “Ulendo wa Aisiraeli Wochoka ku Iguputo” ¶46-51-wcgr) B
Chithunzi B: Chithunzi cha Nyanja Yofiira chojambulidwa kuchokera ku Sinai, mwinanso apa ndi pomwe Aisiraeli anawolokera nyanjayi
Zomwe Tikuphunzirapo
Kodi chitsanzo cha Mose chingatilimbikitse bwanji tikamadziona ngati osayenerera kuchita utumiki umene Yehova watipatsa? (Eks. 4:10; 7:6, 7)
Monga mmene zinakhalira kuti Aroni anathandiza Mose kuti alimbe mtima ndi kukwanitsa utumiki wake, kodi ifenso tingathandize bwanji abale ndi alongo athu? (Eks. 4:14-16) C
Chithunzi C
Mungatsanzire bwanji kulimba mtima komwe Mose anasonyeza munkhaniyi?
Ganizirani Mfundo Yaikulu
Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?
Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?
Kodi Mose akadzaukitsidwa ndingakonde kudzamufunsa chiyani zokhudza zomwe zinachitika pa nthawi iyi ya moyo wake?
Phunzirani Zambiri
Ganizirani mmene kudziwa tanthauzo la dzina la Yehova kungathandizire ana aang’ono kukhala olimba mtima.
Kodi zimene zinachitikira Mose zinamuphunzitsa chiyani zokhudza makhalidwe a Yehova?