Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wcg mutu 21 tsamba 98-tsamba 101
  • Mnyamata Amene Analankhula Molimba Mtima

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mnyamata Amene Analankhula Molimba Mtima
  • Muziyenda Ndi Mulungu Molimba Mtima
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zoti Mufufuze
  • Zomwe Tikuphunzirapo
  • Ganizirani Mfundo Yaikulu
  • Phunzirani Zambiri
  • “Anapitiriza Kukula, Akukondedwa Ndi Yehova”
    Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
  • Samueli Anapitirizabe Kuchita Zabwino
    Nsanja ya Olonda—2008
  • “Anapitiriza Kukula, Akukondedwa ndi Yehova”
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Samueli Anapitiriza Kuchita Zinthu Zabwino
    Phunzitsani Ana Anu
Onani Zambiri
Muziyenda Ndi Mulungu Molimba Mtima
wcg mutu 21 tsamba 98-tsamba 101

21 SAMUELI

Mnyamata Amene Analankhula Molimba Mtima

Losindikizidwa
Losindikizidwa

ZIMENE zinachitika pa moyo wa Samueli n’zofananako ndi zimene zinachitikira mwana wamkazi wa Yefita komanso Samisoni. Anthu atatu onsewa zimene makolo awo anachita zinakhudza kwambiri moyo wawo. Mofanana ndi mwana wamkazi wa Yefita, Samueli anadzipereka kuti azitumikira Yehova m’njira yapadera kwa moyo wake wonse. (1 Sam. 2:11) Mofanana ndi Samisoni, Samueli anali Mnaziri kwa moyo wake wonse. (Ower. 13:7) Nayenso Samueli ankafunika kukhala wolimba mtima ngati anzakewa.

Samueli anasiya kuyamwa mwina ali ndi zaka zitatu kapena kuposa pang’ono. Ndiyeno Hana, yemwe anali mayi ake, anamupititsa kuchihema cha Yehova ku Silo mogwirizana ndi zimene analonjeza. Koma chaka chilichonse ankapita kukamuona ndipo ankamupititsira chovala chatsopano. Samueli ankakhala kuchihemako ndipo mkulu wa ansembe Eli, yemwe anali wachikulire, ndi amene ankamuyang’anira. N’kutheka kuti azimayi ena omwe ankatumikira pachihemapo ankathandiza nawo kusamalira mnyamatayu.

Komabe, anthu ena ankadetsa kulambira koyera pachihemapo koma Eli sankawaletsa. Ana ake awiri, Hofeni ndi Pinihasi ankachita zoipa kwambiri. Iwo ankachita zachiwerewere ndi azimayi ena omwe ankatumikiranso panyumba ya Yehova yopatulikayo. Anthuwa ankasokoneza kulambira koyera m’njira zinanso. Zikuoneka kuti anthu akabwera kuchihemako kudzapereka nsembe zawo, Hofeni ndi Pinihasi ankalamula anthu omwe ankawathandizira kuti azibera anthuwo magawo abwino kwambiri ansembezo omwe ankafunika kuperekedwa kwa Yehova. Eli ankadziwa zimene ana akewa ankachita. Koma ankangowadzudzula mowanyengerera ndipo iwo sankamvera. Ngakhale kuti Samueli ankakhala pamalo oterewa, anali ndi makhalidwe abwino ndipo Mulungu ndi anthu ankasangalala naye. Nthawi ya Yehova itafika yoti akonze zinthu ku Silo, anasankha Samueli kuti akhale mneneri wake.

Tsiku lina usiku Samueli anamva kuitana. Yehova ndi amene ankamuitana koma Samueli ankaganiza kuti mkulu wa ansembe Eli ndi amene akumuitana. Choncho anadzuka n’kupita kwa iye. Eli, yemwe pa nthawiyo anali wachikulire komanso sankaona, anauza mnyamatayo kuti abwerere kukagona chifukwa sanamuitane. Zimenezi zinachitika maulendo enanso awiri. Kenako Eli anazindikira zimene zinkachitika ndipo anauza Samueli kuti apitenso akagone. Anamuuza kuti akamvanso kuitana ayankhe kuti: “Lankhulani Yehova, ine mtumiki wanu ndikumva.” Samueli anachitadi zimene anauzidwazo.

Yehova anaitananso Samueli ulendo wa 4 kuti: “Samueli! Samueli!” Mnyamatayo anayankha kuti: “Lankhulani, ine mtumiki wanu ndikumva.” Zitatero Yehova analankhula naye. Ananena kuti akonza mavuto amene ankachitika ku Silo ndipo alanga Eli chifukwa cholekerera ana ake. Ananena kuti aweruza anthu am’banja lake komanso ana ake oipa aja. Samueli ankafunika kufotokozera Eli uthenga umenewu.

Zimenezi zitachitika Samueli anagonanso koma Baibulo silinena ngati tulo tinabwera. Kutacha anadzuka n’kukatsegula zitseko za bwalo la chihema. Samueli ‘ankaopa kuuza Eli masomphenya amene anaona’ ndipo zimenezi zinali zomveka. Koma Eli anamuitana n’kumuuza kuti amufotokozere zimene Yehova anamuuza. Mwina anazindikira kuti Samueli ankachita mantha choncho anamuuzanso kuti: “Chonde usandibisire.”

Ngakhale kuti anali mnyamata, Samueli anapereka uthenga wachiweruzo wochokera kwa Yehova kwa mkulu wa ansembe Eli

Imeneyitu inali nthawi yovuta kwambiri kwa Samueli. N’kutheka kuti Samueli ankalemekeza kwambiri Eli ndipo ankamuona ngati agogo ake. Ankamulemekezanso chifukwa chakuti anali mkulu wa ansembe mu Isiraeli. Komabe mnyamatayo analankhula molimba mtima moti “sanamʼbisire chilichonse.” Apa ndiye kuti Eli anadziwa kuti Yehova anali atatsala pang’ono kupereka chiweruzo. Koma palibe umboni woti Eli atamva zimenezi anadzudzula ana ake aja.

Samueli ali kamnyamata, waima pafupi ndi zitseko za m’bwalo la chihema ndipo akulankhula ndi mkulu wa ansembe Eli.

Yehova anadalitsa kwambiri Samueli chifukwa chochita zinthu molimba mtima. Baibulo limati: “Yehova anali naye.” Kuwonjezera pamenepa, Yehova anayamba kulankhula kudzera mwa Samueli ndipo “palibe mawu alionse [a Samueli] amene sanakwaniritsidwe.” Patapita nthawi, zonse zimene Samueli ananena zokhudza Eli ndi ana ake zinachitikadi. Pa nthawiyi, Yehova ankagwiritsa ntchito Samueli popereka malangizo kwa Aisiraeli. Kwa zaka zambiri Samueli anatumikira mokhulupirika monga mneneri wa Yehova komanso woweruza. Anaphunzira kuchita zinthu molimba mtima ali wamng’ono ndipo anapitiriza kutumikira Yehova molimba mtima komanso mokhulupirika kwa moyo wake wonse.

Werengani nkhaniyi m’Baibulo:

  • 1 Samueli 1:​9-11, 24-28; 2:​12-36; 3:​1-21; 25:1

  • Aheberi 11:32

Funso lokambirana:

Kodi Samueli anasonyeza kulimba mtima m’njira ziti?

Zoti Mufufuze

  1. 1. Fotokozani zokhudza Silo, malo amene kunali chihema cha Yehova. (w92 11/1 8-9-wcgr) A

    Todd Bolen/BiblePlaces.com

    Chithunzi A: Malo amene panali Silo wakale

  2. 2. Kodi zinthu zinali bwanji pa moyo wa Samueli pamene ankatumikira pachihema? (ia 60-62 ¶9-13) B

    Samueli ali kamnyamata akutsegula zitseko za m’bwalo la chihema.

    Chithunzi B

  3. 3. Kodi mawu akuti Samueli “anali asanadziwe Yehova” akutanthauza chiyani? (1 Sam. 3:7; w02 12/15 8 ¶5-6)

  4. 4. Kodi ulosi wokhudza banja la Eli unakwaniritsidwa bwanji? (it “Eli, 1” ¶5–7-wcgr)

Zomwe Tikuphunzirapo

  • Kodi achinyamata angaphunzire chiyani kwa Samueli zokhudza . . .

    • kumvera mosanyinyirika? (1 Sam. 3:5)

    • kusonyeza ulemu? (1 Sam. 3:​6-10)

    • kukhala wodalirika? (1 Sam. 3:15) C

      M’bale wachinyamata akulemba zinthu zomwe zingafunike pa ntchito yoyeretsa pa Nyumba ya Ufumu. Pamalo olandirira alendo, m’bale akukonza mabuku ndipo mlongo akusesa pogwiritsa ntchito mashini.

      Chithunzi C

  • Ndi pa zinthu ziti pamene wachinyamata ayenera kulankhula molimba mtima, nanga chitsanzo cha Samueli chingamuthandize bwanji?

  • Kodi mungatsanzire Samueli pa nkhani ya kulimba mtima m’njira zinanso ziti?

Ganizirani Mfundo Yaikulu

  • Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?

  • Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?

  • Kodi ndingakonde kudzamufunsa chiyani Samueli akadzaukitsidwa?

Phunzirani Zambiri

Kodi ndi pa nthawi iti pamene achinyamata ndi achikulire angafunike kulimba mtima kuti achite zinthu zoyenera?

Zimene Tingaphunzire Kuchokera kwa Samueli (4:53)

Samueli ali wamng’ono ankachita zoyenera ngakhale kuti anthu amene ankakhala nawo sankalemekeza Mulungu.

“Samueli Anasankha Kutumikira Yehova” (ijwis nkhani 15)

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena