26 NATANI
Anadzudzula Mfumu
‘KODI munthu wabwino ngati ameneyu angapangirenji choipa chimenechi?’ Mneneri Natani ayenera kuti ankadzifunsa funso limeneli pamene ankapita kunyumba yachifumu kukakumana ndi Mfumu Davide yemwe anali mnzake. Zaka zingapo m’mbuyomo, Yehova analamula Natani kuti auze Davide zinthu zosangalatsa zodzachitika m’tsogolo zoti Mesiya adzachokera ku banja lake. (2 Sam. 7:4, 12, 13) Apa n’kuti Davide atachita machimo aakulu ndipo Yehova anatumiza Natani kuti akamudzudzule.
Davide anachita zinthu mobisa koma Yehova ankaona ndipo ayenera kuti anauza Natani zimene zinachitikazo. Tsiku lina madzulo Davide akuyendayenda padenga la nyumba, anaona mkazi akusamba. Iye anaona kuti mkaziyo anali “wokongola kwambiri” choncho anamuitanitsa. Mfumu Davide inkadziwa kuti anali Bati-seba mkazi wa Uriya Muhiti yemwe anali msilikali wake wokhulupirika. Ngakhale zinali choncho Davide anachita naye chigololo. Patapita nthawi, Bati-seba anauza Davide kuti ndi woyembekezera. Davide anayesa kubisa zomwe anachita. Iye anauza Uriya kuti asakhale ndi asilikali anzake koma apite kukagona kunyumba kwake ndi mkazi wake. (Yerekezerani ndi 1 Samueli 21:5.) Uriya anakana ndipo anakhalabe wokhulupirika pa ntchito yake monga msilikali. Kenako Davide anakonza zoti kunkhondo, Uriya amuike pamalo poti akhoza kuphedwa. Zomwe Davide anakonza zinachitikadi. Uriya ataphedwa, Davide anatenga Bati-seba kukhala mkazi wake.
Baibulo limanena kuti: “Zimene Davide anachitazi zinamunyansa kwambiri Yehova.” Choncho Yehova analamula mneneri Natani kuti akadzudzule Davide chifukwa cha zimene anachitazo. Ndiye kodi pamene Natani ankapita kwa Davide ankaganizira kuti Davideyo akamva bwanji? Kuwonjezera pamenepo, Natani ankadziwa kuti Davide anapha Uriya, ndiye kodi mwina ankaganiza kuti nayenso akhoza kuphedwa akaulula machimo ake komanso kumudzudzula? Natani ankafuna kuthandiza Davide kumvetsa kuti zomwe anachita zinali zoipa kwambiri. Mneneriyu ayenera kuti anapempherera nkhaniyi. Choncho anapita kwa mfumu ali ndi fanizo m’maganizo mwake.
Natani anauza Davide zokhudza amuna awiri amene ankakhala mumzinda umodzi. Wina anali wolemera ndipo anali ndi nkhosa komanso ng’ombe zambiri. Pomwe wina anali wosauka ndipo anali ndi kamwana ka nkhosa kamodzi, ankakakonda kwambiri moti kankakula limodzi ndi ana ake. Tsiku lina munthu wolemera uja mosayembekezereka analandira mlendo ndipo ankafuna nkhosa yoti akonzere chakudya mlendoyo. Koma iye sanatenge nkhosa yake. M’malomwake, “anatenga kamwana ka nkhosa ka munthu wosauka uja” n’kuphera mlendoyo. Natani atamaliza kufotokoza fanizoli, Davide anakwiya kwambiri. Iye ananena kuti: “Ndikulumbira mʼdzina la Yehova Mulungu wamoyo, munthu amene anachita zimenezi ayenera kufa!” Iye anakwiya kwambiri chifukwa munthu wolemerayu “sanasonyeze chifundo.”
Natani ankafunika kupereka malangizo a mphamvu komanso kudzudzula mfumu yomwe ankaikonda komanso kuilemekeza
Natani anagwiritsa ntchito fanizo labwino kwambiri. Davide anakhalapo m’busa ndipo mosakayikira ankadana ndi zinthu zopanda chilungamo. Choncho molimba mtima Natani anatchula mfundo yaikulu m’fanizoli kuti: “Munthu ameneyu ndi iweyo.” Davide ayenera kuti anadabwa kwambiri atamva zimenezi. Anamufotokozera zonse zimene Davideyo anachita komanso zonse zimene Yehova anaona. Choncho mneneriyu anamuuza uthenga wochokera kwa Yehova wakuti anthu am’banja lake adzakumana ndi mavuto aakulu kwa zaka zambiri. Ndiye kodi Davide anatani?
Mfumu Davide inati: “Ndachimwira Yehova.” Davide anakhudzidwa kwambiri ndipo analapa kuchokera pansi pa mtima. Natani anasangalala kuti anauza Davide zoti Yehova adzamuchitira chifundo. Iye anati: “Yehova wakukhululukira tchimo lako ndipo suufa.” Komabe, Davide anakumana ndi mavuto chifukwa cha tchimo limene anachita ndi Bati-seba. Mwana amene anabereka ndi Bati-seba anafa. Ndipo kwa zaka zambiri, banja lake linkakumana ndi mavuto osiyanasiyana.
Ngakhale zinali choncho, Davide anakhalabe wokhulupirika. Yehova anamuuzira kulemba masalimo olimbikitsa onena za kulapa komanso zimene Yehova amachita pokhululukira munthu yemwe wachita tchimo. (Salimo 32 ndi 51) Zitatero anakhalanso pa ubwenzi wabwino ndi Yehova ndipo ankadziwika kuti anali wokhulupirika komanso anatsatira kwa moyo wake wonse malangizo amene Natani anamupatsa. Patapita nthawi, Davide anamwalira adakali mtumiki wa Yehova wokhulupirika. (1 Maf. 9:4) Natani anasangalala kuti anasonyeza kulimba mtima kupereka malangizo kwa mfumu.
Werengani nkhaniyi m’Baibulo:
Funso lokambirana:
Kodi Natani anasonyeza kulimba mtima m’njira ziti?
Zoti Mufufuze
1. Ngakhale kuti Natani analemba nawo Baibulo, sitidziwa chilichonse chokhudza banja kapena moyo wake. Kodi zimenezi zikutiuza chiyani zokhudza iyeyo? (w12 2/15 25 ¶2-3)
2. Uriya anali Muhiti. Ndiye n’chifukwa chiyani anali m’gulu la asilikali a Davide? (w24.04 31)
3. Natani analosera kuti anthu am’banja la Davide adzakumana ndi mavuto. Kodi ulosi umenewu unakwaniritsidwa bwanji? (it “Davide” ¶29-wcgr)
4. Kodi Natani anasonyeza bwanji kulimba mtima mu zaka zomaliza za ulamuliro wa Davide? (w12 2/15 25 ¶1) A
Chithunzi A
Zomwe Tikuphunzirapo
Mnzathu akachita tchimo lalikulu, kodi tiyenera kuchita chiyani potengera chitsanzo cha Natani?
Tingatsanzire bwanji Natani kuti timufike munthu pa mtima? B
Chithunzi B
Kodi tingatsanzire kulimba mtima kwa Natani m’njira zinanso ziti?
Ganizirani Mfundo Yaikulu
Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?
Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?
Kodi ndingakonde kudzamufunsa chiyani Natani akadzaukitsidwa?
Phunzirani Zambiri
Kodi zomwe Davide anachita zinakhudza bwanji iyeyo, anzake, banja lake komanso Yehova Mulungu?
Onani chomwe chinapangitsa kuti malangizo a Natani akhale othandiza.
“Muzilandira Uphungu Modzichepetsa” (Nkhani zapawebusaiti “Zoti Muchite Pophunzira Baibulo”)