GAWO 3
Nthawi ya Mesiya Komanso Otsatira Ake
Gawoli likufotokoza zinthu zimene zinachitika mkati mwa zaka pafupifupi 100. Tiyamba ndi kukambirana za namwali wina wa Chiyuda dzina lake Mariya, yemwe anapatsidwa umodzi mwa utumiki wovuta kwambiri umene Yehova anaperekapo kwa munthu wopanda ungwiro. Pomaliza tikambirana zokhudza mtumwi Yohane amene Yesu ankamukonda kwambiri. M’gawoli tikambirananso zitsanzo za anthu omwe anasonyeza kulimba mtima monga Yohane M’batizi, mtumwi Petulo, Mariya wa ku Magadala, Sitefano ndiponso mtumwi Paulo. Mwachitsanzo, anthuwa analimba mtima kuuza ena kuti Yesu ndi Mesiya ngakhale kuti anthu ena sankavomereza zimenezi. Iwo ankatengera chitsanzo cha Yesu komanso ankalalikira uthenga wonena za iye ngakhale kuti anthu ena ankadana nawo komanso kuwazunza.