5 ABULAHAMU
Anavomera Kuchita Chinthu Chovuta Kwambiri
ABULAHAMU anayamba kuyenda pang’onopang’ono kulowera kumalo amene Yehova anamuuza. Ulendowu unali waufupi koma wovuta kwambiri pa maulendo onse omwe anayendapo.
Iye ankangoganizira zomwe Yehova anamuuza kuti: “Tenga Isaki mwana wako mmodzi yekhayo, mwana wako amene umamukonda kwambiriyo, ndipo mupite ku Moriya. Kumeneko ukamupereke nsembe yopsereza paphiri limene ndidzakuuza.” Yehova ankadziwa kuti Abulahamu ankakonda kwambiri Isaki. Ndiye anamuuziranji zimenezi? Nanga n’chiyani chikanamuthandiza kukhala ndi chikhulupiriro komanso kulimba mtima kuti amvere zimene anauzidwazi?
Baibulo limati Abulahamu ndi “bambo wa onse . . . amene ali ndi chikhulupiriro.” (Aroma 4:11) Yehova asanamuuze zimenezi, iye anali atasonyeza kale kuti anali ndi chikhulupiriro cholimba ndipo anamuthandiza kuti chikhulupiriro chake chilimbe kwambiri. Mwachitsanzo, zaka zambiri m’mbuyomo, Mulungu anauza Abulahamu kuti adzawononga mizinda yoipa ya Sodomu ndi Gomora. Zimenezi zinamusokoneza maganizo ndipo anafunsa Yehova ngati akanawononga anthu oipa limodzi ndi abwino omwe. Koma moleza mtima, Yehova anauza Abulahamu kuti sadzawononga mizindayo ngati atapeza anthu olungama ngakhale ochepa. (Gen. 18:16-33) Abulahamu anaphunzira kuti Yehova ndi wachifundo komanso wachilungamo.
Yehova atauza Abulahamu kuti apereke mwana wake nsembe, n’chiyani chinamuthandiza kuti alimbe mtima n’kumvera?
Pasanapite nthawi yaitali, Yehova anachitira Abulahamu ndi Sara chinthu chodabwitsa. Anawathandiza kukhala ndi mwana wamwamuna dzina lake Isaki ngakhale kuti pa nthawiyi Sara anali ndi zaka 90 ndipo Abulahamu anali ndi zaka 100. Abulahamu anaphunzira kuti chilichonse ndi chotheka ndi Yehova ndipo akhoza kubwezeretsa mphamvu m’thupi limene linali ngati lakufa. (Aroma 4:18, 19) Abulahamu sanaiwale zimene anaphunzira pamenepa.
Tsopano patatha zaka 25, Abulahamu ayenera kuti ankakumbukirabe zimenezi pamene ankapita ku Moriya. Iye anazindikira kuti ngakhale Isaki atafa, Yehova akhoza kudzamuukitsanso. (Aheb. 11:19) Kudziwa zimenezi kunamupatsa chiyembekezo chomwe chinamuthandiza kukhala wolimba mtima n’kupitiriza ulendo wake.
Atafika paphiri lomwe Yehova anasankha, Abulahamu anauza antchito ake kuti atsalire, pomwe iye ndi Isaki anapitiriza kukwera phirilo kukapereka nsembe. Anawatsimikizira kuti iye ndi Isaki awapeza. Ali okhaokha m’phirimo, Isaki anadzipereka kuti bambo ake achikulirewo, amumange n’kumuika paguwa la nsembe. Abulahamu anali wokonzeka kuchita zomwe bambo wachikondi sangachitire mwana wake. Iye anatenga mpeni n’kuukweza m’mwamba kuti amuphe. Kenako, anamva mngelo akuitana dzina lake ndi kumuuza kuti: “Usamuvulaze mwanayo.”
Mulungu anasangalala kwambiri ndi kumvera komanso chikhulupiriro cha Abulahamu. Ndipo anabwerezanso kumulonjeza kuti adzamudalitsa komanso adzachulukitsa mbadwa zake. Anamulonjezanso kuti “mitundu yonse yapadziko lapansi,” idzapeza madalitso ambiri chifukwa cha zomwe anachitazi.
Yehova akupitirizabe kukwaniritsa zonse zomwe analonjeza Abulahamu. Zomwe analonjezazi zidzabweretsa madalitso mpaka kalekale. Nkhani ya Abulahamuyi imatiphunzitsanso kanthu kena ponena za Yehova. Imatithandiza kumvetsa ululu umene anamva pofuna kupulumutsa anthu okhulupirika. Monga mmene zinalili kuti Abulahamu anali wokonzeka kupereka mwana wake yemwe ankamukonda kwambiri, Yehova nayenso anali wokonzeka kupereka Mwana wake wobadwa yekha, Yesu, kuti aliyense adzakhale ndi tsogolo labwino. (Yoh. 3:16) Choncho tikaona zomwe Abulahamu anachita pololera kupereka mwana wake, timaphunzira mmene Yehova amatikondera.
Ifenso tingakhale ndi chikhulupiriro cholimba tikamaganizira zimene Yehova ananena ndi kuchita m’mbuyomu. Tikakhala ndi chikhulupiriro cholimba, tidzakhalanso olimba mtima. Tisamadere nkhawa kuti Mulungu angatiuze kuchita chinthu chovuta ngati mmene anauzira Abulahamu. Iye sanauzeponso munthu wina kuchita zimenezi. Komabe tingakhale otsimikiza kuti ngati tili ndi chikhulupiriro cholimba, chilichonse chomwe angatiuze, tingakwanitse kumumvera. Ndipo kukhala omvera, kudzatithandiza kuti tidzapeze madalitso ambiri.
Werengani nkhaniyi m’Baibulo:
Funso lokambirana:
Kodi Abulahamu anasonyeza kulimba mtima m’njira ziti pa nthawiyi?
Zoti Mufufuze
1. Kodi pali umboni wotani wosonyeza kuti Abulahamu anali munthu weniweni? (g 5/12 18, bokosi; it “Abulahamu” ¶22-23-wcgr) A
Chithunzi A: Zolemba zakale zonena za “Munda wa Abulamu” pakhoma la ku Karnak ku Egypt
2. Kodi n’kutheka kuti Abulahamu anaphunzira bwanji zokhudza Yehova Mulungu? (ia 26 ¶4-5)
3. N’chiyani chinachititsa kuti Yehova avomereze kulambira kwa Abulahamu? (rr 20 ¶18)
4. Kodi zimene Yehova analonjeza Abulahamu pa Genesis 22:17, zimatsimikizira bwanji kuti Baibulo limanena zoona? (g88 4/8 25-wcgr) B
Chithunzi B
Chithunzi B
Zomwe Tikuphunzirapo
Kodi chiyembekezo chinathandiza bwanji Abulahamu kukhala wolimba mtima? Nanga kuganizira za chiyembekezo chathu, kungatithandize bwanji kukhala olimba mtima? C
Chithunzi C
Kodi tingatsanzire bwanji Abulahamu pa nkhani yokhala olimba mtima komanso kukhala wodzipereka. . .
tikapeza mwayi wolalikira? (Aheb. 13:15)
tikamaganizira mmene tingagwiritsire ntchito zinthu zathu? (Miy. 3:9)
tikadziwa kuti Akhristu anzathu akufunikira thandizo lathu? (Afil. 4:18)
Mogwirizana ndi nkhaniyi, tingatsanzire kulimba mtima kwa Abulahamu m’njira zinanso ziti?
Ganizirani Mfundo Yaikulu
Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?
Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?
Kodi ndingakonde kudzamufunsa chiyani Abulahamu kapena Isaki akadzaukitsidwa?
Phunzirani Zambiri
Yerekezerani kuti mukuona zomwe zinachitika pa nthawiyo.
Kodi zinatheka bwanji kuti Abulahamu akhale mnzake wa Yehova, nanga ifeyo tingatani kuti Yehova akhale mnzathu wapamtima?