Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w15 6/15 tsamba 18-19
  • “Ngati Kingsley Akukwanitsa, Kuli Bwanji Ine?”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Ngati Kingsley Akukwanitsa, Kuli Bwanji Ine?”
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • ANKAPITA KU MISONKHANO NDIPO ANALEMBETSA M’SUKULU
  • Kodi Kukhala Mkhristu Kumatanthauza Chiyani?
    Galamukani!—2007
  • Mabuku a Zilembo za Anthu Osaona Akuthandiza Kwambiri
    Kodi Zopereka Zanu Zimagwiritsidwa Ntchito Bwanji?
  • Lalikirani Ufulu!
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Kulembetsa m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
w15 6/15 tsamba 18-19
Kingsley akubatizidwa

“Ngati Kingsley Akukwanitsa, Kuli Bwanji Ine?”

KU SRI LANKA kunali munthu wina wosaona dzina lake Kingsley. Iye analinso ndi vuto losamva bwino ndipo ankayenda pa njinga ya olumala. Tsiku lina, Kingsley anawerenga Baibulo m’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu. Iye anatchula bwinobwino liwu lililonse koma sankagwiritsa ntchito Baibulo lake.

Mwina mukudzifunsa kuti, Kodi zinatheka bwanji kuti Kingsley aphunzire za Yehova n’kufika polembetsa m’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu? Tamvani zimene zinachitika.

Tsiku limene ndinayamba kukumana ndi Kingsley ndinadabwa kwambiri ndi chidwi chimene anali nacho. Iye anali ataphunzira ndi a Mboni angapo ndipo ankafunitsitsa kuphunzirabe. Anali ndi buku lakuti Chidziwitso Chotsogolera ku Moyo Wosathaa la zilembo za anthu osaona koma linali lakutha. Iye anavomera kuti tiyambe kuphunzira koma panali mavuto awiri.

Vuto loyamba linali lakuti Kingsley ankakhala ndi anthu ambirimbiri m’nyumba yosungira okalamba ndi olumala. M’nyumbayi munkakhala phokoso ndiye poti Kingsley sankamva bwinobwino, ndinkafunika kukweza mawu kwambiri. Aliyense m’nyumbamo ankamva zimene tinkakambirana pophunzira.

Vuto lachiwiri linali lakuti tinkafunika kuphunzira zinthu zochepa kwambiri ulendo uliwonse kuti athe kuzimvetsa n’kuzisunga mumtima. Kuti zinthu ziziyenda bwino, Kingsley ankakonzekera mwakhama kwambiri. Iye ankawerenga ndimezo mobwerezabwereza, kuoneratu malemba n’kupezeratu mayankho a mafunso. Pokambirana, iye ankafotokoza mayankho ake mokweza kwambiri ndipo ankachita zimenezi uku akumenya pansi. Tinkaphunzira kawiri pa mlungu ndipo phunziro lililonse linkatenga maola awiri.

ANKAPITA KU MISONKHANO NDIPO ANALEMBETSA M’SUKULU

Kingsley ndi Paul

Kingsley ndi Paul

Kingsley ankafunitsitsa kupita ku misonkhano koma sinali nkhani yophweka. Pankafunika kumukweza ndiponso kumutsitsa m’galimoto. Kenako n’kumukweza panjinga kupita naye m’Nyumba ya Ufumu. Koma abale ambiri ankamuthandiza ndipo ankachita kusinthana. Pa misonkhano, Kingsley ankakhala malo oti azimva bwino, ankamvetsera mwatcheru komanso ankapereka ndemanga.

Patapita nthawi, iye analembetsa m’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu. Kutatsala milungu iwiri kuti akawerenge Baibulo koyamba, ndinamufunsa ngati akukonzekera. Anayankha mosakayikira kuti: “Inde ndakhala ndikukonzekera maulendo 30.” Ndinamuyamikira ndipo ndinamupempha kuti awerenge ine ndikumvetsera. Anatsegula Baibulo kenako n’kugwira patsamba loyenerera. Koma ndinaona kuti zala zake sizinkasuntha pamene ankawerenga. Iye anali ataloweza mavesi onse.

Sindinakhulupirire zimene ndinaonazo moti misozi inayamba kutuluka m’maso mwanga. Kenako ndinamufunsa kuti anakwanitsa bwanji kuloweza zonse atangokonzekera maulendo 30 okha. Iye anayankha kuti: “Iii, ndikunenatu maulendo 30 pa tsiku.” Iye anachita zimenezi kwa mwezi wathunthu mpaka analoweza mavesi onse.

Tsiku loti awerenge Baibulo linafika ndipo atamaliza kuwerenga anthu anaomba m’manja kwa nthawi yaitali mpaka ena misozi inayamba kulengeza. Izi zitachitika, mlongo wina amene anasiya kukamba nkhani m’sukulu chifukwa cha mantha, analembetsa kuti ayambirenso. Mlongoyu anati: “Ngati Kingsley akukwanitsa, kuli bwanji ine?”

Pa September 6, 2008, Kingsley anabatizidwa ataphunzira Baibulo kwa zaka zitatu. Iye ankatumikira Yehova mokhulupirika mpaka pamene anamwalira pa May 13, 2014. Kingsley sankakayikira ngakhale pang’ono kuti m’Paradaiso adzakhala wathanzi ndipo adzapitiriza kutumikira Mulungu. (Yes. 35:5, 6)—Yofotokozedwa ndi Paul McManus.

a Bukuli linasindikizidwa mu 1995 koma pano anasiya kulisindikiza.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena