Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Mafunso otsatirawa tidzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira October 28, 2013.
1. Kodi kukhala ndi “maganizo a Khristu” kumatanthauza chiyani? (1 Akor. 2:16) [Sept. 2, w08 7/15 tsa. 27 ndime 7]
2. Kodi tingasonyeze bwanji kuti ‘timathawa dama’? (1 Akor. 6:18) [Sept. 2, w08 7/15 tsa. 27 ndime 9; w04 2/15 tsa. 12 ndime 9]
3. Kodi Paulo ankatanthauza chiyani pamene ananena kuti, “akazi akhale chete m’mipingo”? (1 Akor. 14:34) [Sept. 9, w12 9/1 tsa. 9, bokosi]
4. Kodi mawu a Paulo amene ali pa 2 Akorinto 1:24 angathandize bwanji akulu masiku ano? [Sept. 16, w13 1/15 tsa. 27 ndime 2-3]
5. Kodi tingatsatire bwanji zimene lemba la 2 Akorinto 9:7 limanena? [Sept. 23, g 5/08 tsa. 21, bokosi]
6. Kodi kutsatira malangizo a Paulo a pa Agalatiya 6:4, kungatithandize bwanji? [Sept. 30, w12 12/15 tsa. 13 ndime 18]
7. Kodi “kusunga umodzi wathu mwa mzimu” kumatanthauza chiyani? (Aef. 4:3) [Oct. 7, w12 7/15 tsa. 28 ndime 7]
8. Kodi Paulo ankaona bwanji zinthu zimene anazisiya? (Afil. 3:8) [Oct. 14, w12 3/15 tsa. 27 ndime 12]
9. Kodi tikuphunzira chiyani pa malangizo akuti: “Tisapitirize kugona ngati mmene enawo akuchitira”? (1 Ates. 5:6) [Oct. 21, w12 3/15 tsa. 10 ndime 4]
10. Kodi imfa ya Yesu inali “dipo lokwanira ndendende” motani? (1 Tim. 2:6) [Oct. 28, w11 6/15 tsa. 13 ndime 11]